Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku la Yeremiya

Machaputala

Mitu

 • 1

  • Yeremiya anasankhidwa kuti akhale mneneri (1-10)

  • Masomphenya a mtengo wa amondi (11, 12)

  • Masomphenya a mphika (13-16)

  • Yeremiya analimbikitsidwa kuti agwire ntchito yake (17-19)

 • 2

  • Isiraeli anasiya Yehova nʼkuyamba kulambira milungu ina (1-37)

   • Isiraeli ali ngati mtengo wa mpesa wachilendo (21)

   • Zovala zake zathimbirira ndi magazi (34)

 • 3

  • Isiraeli anapanduka kwambiri (1-5)

  • Isiraeli ndi Yuda anachita tchimo la chigololo (6-11)

  • Anawalimbikitsa kuti alape (12-25)

 • 4

  • Kulapa kumabweretsa madalitso (1-4)

  • Tsoka lidzachokera kumpoto (5-18)

  • Yeremiya anamva kupweteka mumtima chifukwa cha tsoka limene linkabwera (19-31)

 • 5

  • Anthu anakana malangizo a Yehova (1-13)

  • Adzawonongedwa koma sadzawawononga onse (14-19)

  • Yehova anaimba mlandu anthu (20-31)

 • 6

  • Nthawi yoti Yerusalemu azunguliridwe yayandikira (1-9)

  • Yehova anakwiyira Yerusalemu (10-21)

   • Akunena kuti, “Mtendere!” pamene kulibe mtendere (14)

  • Anaukiridwa mwankhanza ndi anthu akumpoto (22-26)

  • Yeremiya anasandutsidwa woyenga zitsulo (27-30)

 • 7

  • Kukhulupirira kachisi wa Yehova sikunawathandize (1-11)

  • Kachisi adzakhala ngati Silo (12-15)

  • Mulungu sasangalala ndi kulambira kwachinyengo (16-34)

   • Analambira “Mfumukazi Yakumwamba” (18)

   • Ankapereka nsembe ana ku Hinomu (31)

 • 8

  • Anthu anasankha njira imene anthu ambiri ankaitsatira (1-7)

  • Kodi anthu angakhale ndi nzeru popanda mawu a Yehova? (8-17)

  • Yeremiya analira chifukwa cha kuwonongedwa kwa Yuda (18-22)

   • “Kodi mu Giliyadi mulibe mafuta a basamu?” (22)

 • 9

  • Yeremiya anali ndi chisoni chachikulu (1-3a)

  • Yehova anaimba mlandu Yuda (3b-16)

  • Kulirira Yuda (17-22)

  • Adzitame chifukwa chodziwa Yehova (23-26)

 • 10

  • Milungu ya anthu a mitundu ina singafanane ndi Mulungu wamoyo (1-16)

  • Nthawi yoti awonongedwe komanso kutengedwa kupita kudziko lina yayandikira (17, 18)

  • Yeremiya anamva chisoni (19-22)

  • Pemphero la mneneri (23-25)

   • Munthu alibe ulamuliro wosankha yekha njira ya moyo wake (23)

 • 11

  • Yuda anaphwanya pangano limene anapanga ndi Mulungu (1-17)

   • Anali ndi milungu yochuluka mofanana ndi mizinda yawo (13)

  • Yeremiya anali ngati mwana wa nkhosa amene akupita kukaphedwa (18-20)

  • Yeremiya anatsutsidwa ndi anthu akwawo (21-23)

 • 12

  • Kudandaula kwa Yeremiya (1-4)

  • Zimene Yehova anayankha (5-17)

 • 13

  • Lamba wa nsalu amene anawonongeka (1-11)

  • Mitsuko ya vinyo idzaphwanyidwa (12-14)

  • Yuda amene sangathenso kusintha adzatengedwa kupita ku ukapolo (15-27)

   • “Kodi Mkusi angasinthe khungu lake?” (23)

 • 14

  • Chilala, njala ndi lupanga (1-12)

  • Aneneri abodza adzawonongedwa (13-18)

  • Yeremiya anavomereza kuti anthuwo anali ochimwa (19-22)

 • 15

  • Yehova sadzasintha chiweruzo chake (1-9)

  • Kudandaula kwa Yeremiya (10)

  • Zimene Yehova anayankha (11-14)

  • Pemphero la Yeremiya (15-18)

   • Ankasangalala ndi kudya mawu a Mulungu (16)

  • Yeremiya analimbikitsidwa ndi Yehova (19-21)

 • 16

  • Yeremiya anauzidwa kuti asakwatire, kulira kapena kusala kudya (1-9)

  • Anapatsidwa chilango kenako nʼkubwezeretsedwa mwakale (10-21)

 • 17

  • Tchimo la Yuda lalembedwa mochita kugoba (1-4)

  • Madalitso amene amabwera chifukwa chokhulupirira Yehova (5-8)

  • Mtima ndi wopusitsa (9-11)

  • Yehova, chiyembekezo cha Isiraeli (12, 13)

  • Pemphero la Yeremiya (14-18)

  • Sabata lizikhala lopatulika (19-27)

 • 18

  • Dongo mʼdzanja la wowumba (1-12)

  • Yehova adzafulatira Isiraeli (13-17)

  • Chiwembu chimene anakonzera Yeremiya komanso kuchonderera kwake (18-23)

 • 19

  • Yeremiya anauzidwa kuti akaswe botolo la dothi (1-15)

   • Kupereka ana nsembe kwa Baala (5)

 • 20

  • Pasuri anamenya Yeremiya (1-6)

  • Yeremiya sangasiye kulalikira (7-13)

   • Uthenga wa Mulungu unali ngati moto woyaka (9)

   • Yehova ali ngati msilikali woopsa (11)

  • Kudandaula kwa Yeremiya (14-18)

 • 21

  • Yehova anakana zimene Zedekiya anapempha (1-7)

  • Anthu ayenera kusankha pakati pa moyo ndi imfa (8-14)

 • 22

  • Uthenga wachiweruzo wokhudza mafumu oipa (1-30)

   • Uthenga wokhudza Salumu (10-12)

   • Uthenga wokhudza Yehoyakimu (13-23)

   • Uthenga wokhudza Koniya (24-30)

 • 23

  • Abusa abwino komanso oipa (1-4)

  • Tidzakhala otetezeka mu ulamuliro wa “mfumu yolungama” (5-8)

  • Aneneri abodza anadzudzulidwa (9-32)

  • “Katundu wolemera” wa Yehova (33-40)

 • 24

  • Nkhuyu zabwino komanso zoipa (1-10)

 • 25

  • Yehova anadzudzula mitundu ya anthu (1-38)

   • Mitundu ya anthu idzatumikira Ababulo kwa zaka 70 (11)

   • Kapu ya vinyo wa mkwiyo wa Mulungu (15)

   • Tsoka likufalikira kuchokera ku mtundu wina kupita ku mtundu wina (32)

   • Anthu amene adzaphedwe ndi Yehova (33)

 • 26

  • Yeremiya anaopsezedwa kuti aphedwa (1-15)

  • Yeremiya anapulumutsidwa (16-19)

   • Ananena zimene Mika ananena mu ulosi wake (18)

  • Mneneri Uliya (20-24)

 • 27

  • Goli la Babulo (1-11)

  • Zedekiya anauzidwa kuti azimvera mfumu ya Babulo (12-22)

 • 28

  • Yeremiya anatsutsana ndi mneneri wabodza Hananiya (1-17)

 • 29

  • Kalata imene Yeremiya analembera anthu amene anatengedwa ukapolo ku Babulo (1-23)

   • Aisiraeli adzabwerera kwawo pambuyo pa zaka 70 (10)

  • Uthenga wopita kwa Semaya (24-32)

 • 30

  • Malonjezo okhudza kubwezeretsedwa mwakale komanso kuchiritsidwa (1-24)

 • 31

  • Aisiraeli amene anatsala adzakhalanso mʼdziko lawo (1-30)

   • Rakele akulirira ana ake (15)

  • Pangano latsopano (31-40)

 • 32

  • Yeremiya anagula munda (1-15)

  • Pemphero la Yeremiya (16-25)

  • Zimene Yehova anayankha (26-44)

 • 33

  • Analonjezedwa kuti adzabwerera mwakale (1-13)

  • Tidzakhala otetezeka mu ulamuliro wa “mfumu yolungama” (14-16)

  • Pangano limene anachita ndi Davide komanso ansembe (17-26)

   • Pangano lokhudza masana ndi usiku (20)

 • 34

  • Uthenga wachiweruzo wopita kwa Zedekiya (1-7)

  • Anaphwanya pangano loti amasule akapolo (8-22)

 • 35

  • Arekabu anasonyeza chitsanzo chabwino pa nkhani yomvera (1-19)

 • 36

  • Yeremiya ankanena mawu oti alembedwe mumpukutu (1-7)

  • Baruki anawerenga mpukutu mokweza (8-19)

  • Yehoyakimu anawotcha mpukutu (20-26)

  • Uthengawo unalembedwanso mumpukutu watsopano (27-32)

 • 37

  • Akasidi anabwerera kwa kanthawi kochepa (1-10)

  • Yeremiya anaikidwa mʼndende (11-16)

  • Zedekiya anakumana ndi Yeremiya (17-21)

   • Yeremiya ankapatsidwa mkate (21)

 • 38

  • Yeremiya anaponyedwa mʼchitsime (1-6)

  • Ebedi-meleki anapulumutsa Yeremiya (7-13)

  • Yeremiya analimbikitsa Zedekiya kuti adzipereke mʼmanja mwa Ababulo (14-28)

 • 39

  • Kuwonongedwa kwa Yerusalemu (1-10)

   • Zedekiya anathawa koma anamugwira (4-7)

  • Yeremiya ankayenera kulonderedwa (11-14)

  • Ebedi-meleki anapulumutsidwa (15-18)

 • 40

  • Nebuzaradani anamasula Yeremiya (1-6)

  • Gedaliya anasankhidwa kuti akhale wolamulira dziko (7-12)

  • Chiwembu chimene anakonzera Gedaliya (13-16)

 • 41

  • Gedaliya anaphedwa ndi Isimaeli (1-10)

  • Yohanani anathamangitsa Isimaeli (11-18)

 • 42

  • Anthu anapempha Yeremiya kuti afunsire malangizo kwa Mulungu (1-6)

  • Yehova anawauza kuti: “Musapite ku Iguputo” (7-22)

 • 43

  • Anthu sanamvere ndipo anapita ku Iguputo (1-7)

  • Zimene Yehova anauza Yeremiya ku Iguputo (8-13)

 • 44

  • Ananeneratu za tsoka limene lidzagwere Ayuda ku Iguputo (1-14)

  • Anthu anakana kumvera zimene Mulungu anawachenjeza (15-30)

   • Ankalambira “Mfumukazi Yakumwamba” (17-19)

 • 45

  • Uthenga wa Yehova wopita kwa Baruki (1-5)

 • 46

  • Ulosi wokhudza Iguputo (1-26)

   • Iguputo adzagonjetsedwa ndi Nebukadinezara (13, 26)

  • Zimene Aisiraeli analonjezedwa (27, 28)

 • 47

  • Ulosi wokhudza Afilisiti (1-7)

 • 48

  • Ulosi wokhudza Mowabu (1-47)

 • 49

  • Ulosi wokhudza Aamoni (1-6)

  • Ulosi wokhudza Edomu (7-22)

   • Mtundu wa Edomu sudzakhalaponso (17, 18)

  • Ulosi wokhudza Damasiko (23-27)

  • Ulosi wokhudza Kedara ndi Hazori (28-33)

  • Ulosi wokhudza Elamu (34-39)

 • 50

  • Ulosi wokhudza Babulo (1-46)

   • Thawani mʼBabulo (8)

   • Aisiraeli adzawabwezera kwawo (17-19)

   • Madzi a ku Babulo adzaumitsidwa (38)

   • MʼBabulo simudzakhalanso anthu (39, 40)

 • 51

  • Ulosi wokhudza Babulo (1-64)

   • Babulo adzawonongedwa mwadzidzidzi ndi Amedi (8-12)

   • Buku linaponyedwa mumtsinje wa Firate (59-64)

 • 52

  • Zedekiya anagalukira mfumu ya Babulo (1-3)

  • Nebukadinezara anazungulira Yerusalemu (4-11)

  • Kuwonongedwa kwa mzinda komanso kachisi (12-23)

  • Anthu anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo (24-30)

  • Yehoyakini anatulutsidwa mʼndende (31-34)