Yeremiya 40:1-16

  • Nebuzaradani anamasula Yeremiya (1-6)

  • Gedaliya anasankhidwa kuti akhale wolamulira dziko (7-12)

  • Chiwembu chimene anakonzera Gedaliya (13-16)

40  Awa ndi mawu amene Yehova anauza Yeremiya pambuyo poti Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu wamumasula kuchoka ku Rama.+ Nebuzaradani anatenga Yeremiya kumeneko atamangidwa maunyolo amʼmanja ndipo anali mʼgulu la anthu onse a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo.  Ndiyeno mkulu wa asilikali olondera mfumuyu anatengera Yeremiya pambali nʼkumuuza kuti: “Yehova Mulungu wako ananeneratu kuti tsoka ili lidzagwera dziko lino  ndipo Yehova wabweretsadi tsokali mogwirizana ndi zimene ananenazo, chifukwa anthu inu munachimwira Yehova ndipo simunamvere mawu ake. Nʼchifukwa chake zimenezi zakuchitikirani.+  Lero ndikumasula maunyolo amene ali mʼmanja mwako. Ngati ungakonde kupita nane ku Babulo, tiye ndipo ndizikakuyangʼanira. Koma ngati sukufuna kupita nane ku Babulo, usapite. Taona! Dziko lonse lili pamaso pako. Pita kulikonse kumene ungakonde.”+  Yeremiya akuganizira koti apite, Nebuzaradani anamuuza kuti: “Bwerera kwa Gedaliya,+ mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani,+ amene mfumu ya Babulo yamuika kuti azilamulira mizinda ya Yuda. Ukakhale naye pakati pa anthuwo, kapena ukhoza kupita kulikonse kumene ungakonde.” Kenako mkulu wa asilikali olondera mfumu anamupatsa chakudya chapaulendo ndi mphatso ndipo anamulola kuti apite.  Choncho Yeremiya anapita ku Mizipa+ kwa Gedaliya, mwana wa Ahikamu nʼkumakhala naye limodzi ndi anthu amene anatsala mʼdziko la Yuda.  Patapita nthawi, akuluakulu onse a asilikali amene anali mʼdziko lonselo limodzi ndi asilikali awo, anamva kuti mfumu ya Babulo yaika Gedaliya mwana wa Ahikamu kuti akhale wolamulira dzikolo. Anamvanso kuti yamuika kuti azilamulira amuna, akazi ndi ana ochokera pakati pa anthu osauka mʼdzikolo amene sanatengedwe kupita ku Babulo.+  Choncho akuluakulu amenewa anapita kwa Gedaliya ku Mizipa.+ Mayina awo anali Isimaeli+ mwana wa Netaniya, Yohanani+ ndi Yonatani ana a Kareya, Seraya mwana wa Tanumeti, ana a Efai wa ku Netofa, Yezaniya+ mwana wa munthu wa ku Maaka limodzi ndi asilikali awo.  Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani analumbira pamaso pa akuluakuluwo ndi asilikali awo kuti: “Musaope kutumikira Akasidi. Zikhalani mʼdzikoli nʼkumatumikira mfumu ya Babulo ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino.+ 10  Koma ine ndizikhala ku Mizipa kuno kuti ndizikuimirirani kwa* Akasidi amene azibwera kwa ife. Koma inuyo musonkhanitse vinyo, zipatso zamʼchilimwe* ndi mafuta nʼkuziika mʼziwiya zanu zosungira zinthu ndipo muzikhala mʼmizinda imene mwaitenga kuti ikhale yanu.”+ 11  Ndiye Ayuda onse amene anali ku Mowabu, ku Amoni, ku Edomu komanso amene anali mʼmayiko ena onse anamvanso kuti mfumu ya Babulo yalola kuti anthu amene anatsala azikhala ku Yuda komanso kuti yaika Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani kuti aziwalamulira. 12  Choncho Ayuda onse anayamba kubwerera kuchokera kumadera onse kumene anawabalalitsira ndipo anabwera mʼdziko la Yuda kwa Gedaliya ku Mizipa. Iwo anasonkhanitsa vinyo ndi zipatso zamʼchilimwe zochuluka kwambiri. 13  Nayenso Yohanani mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a asilikali amene anali mʼdziko lonselo, anabwera kwa Gedaliya ku Mizipa. 14  Iwo anauza Gedaliya kuti: “Kodi sukudziwa kuti Baalisi mfumu ya a Amoni,+ watumiza Isimaeli mwana wa Netaniya kuti adzakuphe?”+ Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanawakhulupirire. 15  Kenako Yohanani mwana wa Kareya anauza mwachinsinsi Gedaliya ku Mizipa kuti: “Ndikufuna ndipite kukapha Isimaeli mwana wa Netaniya ndipo palibe amene adziwe. Nʼchifukwa chiyani iyeyo akufuna kukupha? Nʼchifukwa chiyani akufuna kuti anthu onse a mu Yuda amene akubwera kwa iwe amwazike komanso kuti anthu amene anatsala mu Yuda awonongeke?” 16  Koma Gedaliya+ mwana wa Ahikamu anauza Yohanani mwana wa Kareya kuti: “Usachite zimenezi chifukwa zimene ukunena zokhudza Isimaeli, ndi zabodza.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti ndiziima pamaso pa.”
Mawu akuti “zipatso zamʼchilimwe” akunena za nkhuyu ndipo nthawi zina amatanthauza zipatso za kanjedza.