Yeremiya 38:1-28

  • Yeremiya anaponyedwa mʼchitsime (1-6)

  • Ebedi-meleki anapulumutsa Yeremiya (7-13)

  • Yeremiya analimbikitsa Zedekiya kuti adzipereke mʼmanja mwa Ababulo (14-28)

38  Ndiyeno Sefatiya mwana wa Mateni, Gedaliya mwana wa Pasuri,+ Yukali+ mwana wa Selemiya ndi Pasuri mwana wa Malikiya anamva mawu onse amene Yeremiya ankauza anthu onse kuti:  “Yehova wanena kuti, ‘Amene atsale mumzinda uno adzafa ndi lupanga, njala ndi mliri.*+ Koma amene adzadzipereke* kwa Akasidi adzapitiriza kukhala ndi moyo. Adzapulumutsa moyo wake, sadzafa ayi.’+  Yehova wanena kuti, ‘Mzinda uno udzaperekedwa ndithu mʼmanja mwa asilikali a mfumu ya Babulo ndipo mfumuyo idzaulanda.’”+  Akalonga anauza mfumu kuti: “Chonde lamulani kuti munthu uyu aphedwe+ chifukwa akufooketsa asilikali amene atsala mumzinda uno komanso anthu onse, powauza mawu amenewa. Munthu ameneyu sakuwafunira mtendere anthuwa, koma akuwafunira tsoka.”  Mfumu Zedekiya inawayankha kuti: “Taonani! Iye ali mʼmanja mwanu, ndipo palibe chilichonse chimene ndingachite kuti ndikuletseni.”  Choncho iwo anagwira Yeremiya nʼkumuponya mʼchitsime cha Malikiya mwana wa mfumu, chimene chinali mʼBwalo la Alonda.+ Iwo analowetsa Yeremiya mʼchitsimemo pogwiritsa ntchito zingwe. Mʼchitsimemo munalibe madzi koma munali matope ndipo Yeremiya anayamba kumira mʼmatopemo.  Ebedi-meleki+ wa ku Itiyopiya, amene anali nduna mʼnyumba ya mfumu, anamva kuti Yeremiya amuponya mʼchitsime. Apa nʼkuti mfumu itakhala pa Geti la Benjamini.+  Choncho Ebedi-meleki anatuluka mʼnyumba ya mfumuyo ndipo anakauza mfumu kuti:  “Inu mbuyanga mfumu, zimene anthu awa achitira mneneri Yeremiya ndi zoipa. Iwo amuponya mʼchitsime ndipo afera momwemo chifukwa cha njala, popeza mkate watheratu mumzindawu.”+ 10  Kenako mfumu inalamula Ebedi-meleki wa ku Itiyopiya kuti: “Tenga amuna 30 kunoko, ndipo mukatulutse mneneri Yeremiya mʼchitsimemo asanafe.” 11  Choncho Ebedi-meleki anatenga amunawo ndipo analowa mʼnyumba ya mfumu, mʼchipinda chimene chinali pansi pa malo osungira chuma.+ Kumeneko anatengako nsanza ndi nsalu zakutha nʼkuzilowetsa mʼchitsime momwe munali Yeremiya pogwiritsa ntchito zingwe. 12  Ndiyeno Ebedi-meleki wa ku Itiyopiya anauza Yeremiya kuti: “Nsanza komanso nsalu zakuthazo uzikulunge kuzingwezo nʼkuziika mʼkhwapa.” Yeremiya anachitadi zimenezo, 13  ndipo iwo anakoka Yeremiya ndi zingwezo nʼkumutulutsa mʼchitsimemo. Yeremiya anapitiriza kukhala mʼBwalo la Alonda.+ 14  Mfumu Zedekiya inatumiza anthu kuti akaitane mneneri Yeremiya kuti abwere kwa iye pakhomo lachitatu lamʼnyumba ya Yehova. Yeremiya atafika, mfumu inamuuza kuti: “Ndikufuna ndikufunse zinazake. Usandibisire kalikonse.” 15  Yeremiya anauza Zedekiya kuti: “Ndikakuuzani, ndithu mundipha. Komanso ndikakupatsani malangizo, simundimvera.” 16  Choncho Mfumu Zedekiya inalumbira kwa Yeremiya mwachinsinsi kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo, amene anatipatsa moyowu, sindikupha ndiponso sindikupereka mʼmanja mwa anthu awa amene akufuna kuchotsa moyo wako.” 17  Ndiyeno Yeremiya anauza Zedekiya kuti: “Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Mukadzipereka mʼmanja mwa akalonga* a mfumu ya Babulo, mudzakhalabe ndi moyo ndipo mzindawu sudzawotchedwa ndi moto komanso inuyo ndi banja lanu mudzakhalabe ndi moyo.+ 18  Koma ngati simudzadzipereka mʼmanja mwa akalonga* a mfumu ya Babulo, mzindawu udzaperekedwa mʼmanja mwa Akasidi ndipo adzauwotcha ndi moto.+ Inuyo simudzathawa mʼmanja mwawo.’”+ 19  Ndiyeno Mfumu Zedekiya inauza Yeremiya kuti: “Ndikuopa Ayuda amene athawira kwa Akasidi chifukwa ngati ndingaperekedwe mʼmanja mwawo akhoza kundizunza.” 20  Koma Yeremiya anauza mfumuyo kuti: “Sadzakuperekani mʼmanja mwawo. Chonde, mverani mawu a Yehova amene ndikukuuzani. Mukatero zinthu zidzakuyenderani bwino ndipo mudzakhalabe ndi moyo. 21  Koma mukakana kudzipereka mʼmanja mwawo,* Yehova wandiululira izi: 22  Taonani! Akazi onse amene anatsala mʼnyumba ya mfumu ya Yuda akupita nawo kwa akalonga a mfumu ya Babulo,+ ndipo akaziwo akunena kuti,‘Amuna amene munkawadalira* akuputsitsani ndipo akugonjetsani.+ Achititsa kuti mapazi anu amire mʼmatope Tsopano akubwerera ndipo akusiyani.’ 23  Akazi anu onse ndi ana anu aamuna akupita nawo kwa Akasidi ndipo inuyo simudzathawa mʼmanja mwawo. Koma mfumu ya Babulo+ idzakugwirani ndipo mzindawu udzawotchedwa chifukwa cha inu.”+ 24  Kenako Zedekiya anauza Yeremiya kuti: “Munthu aliyense asadziwe zimenezi, kuti usafe. 25  Ngati akalonga atamva kuti ndalankhula nawe, nʼkubwera kwa iwe kudzakuuza kuti, ‘Chonde tiuze zimene unalankhula ndi mfumu, usatibisire kalikonse ndipo sitikupha.+ Kodi mfumu yakuuza chiyani?’ 26  Uwauze kuti, ‘Ndimapempha mfumu kuti isandibwezere kunyumba ya Yehonatani chifukwa ndingakafere kumeneko.’”+ 27  Patapita nthawi, akalonga onse anafika kwa Yeremiya nʼkumufunsa mafunso. Yeremiya anawayankha mogwirizana ndi zonse zimene mfumu inamulamula kuti anene. Choncho akalongawo sananenenso chilichonse chifukwa sanamve zimene anakambirana. 28  Yeremiya anapitirizabe kukhala mʼBwalo la Alonda+ mpaka tsiku limene Yerusalemu analandidwa. Iye anali adakali konko pamene Yerusalemu analandidwa.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “matenda.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene adzapite.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mukapita kwa akalonga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Koma ngati simudzapita kwa akalonga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Koma mukakana kupita.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Amuna amene munkakhala nawo pa mtendere.”