Yeremiya 50:1-46

  • Ulosi wokhudza Babulo (1-46)

    • Thawani mʼBabulo (8)

    • Aisiraeli adzawabwezera kwawo (17-19)

    • Madzi a ku Babulo adzaumitsidwa (38)

    • MʼBabulo simudzakhalanso anthu (39, 40)

50  Awa ndi mawu okhudza Babulo,+ dziko la Akasidi, amene Yehova ananena kudzera mwa mneneri Yeremiya. Iye anati:   “Nenani ndi kulengeza zimene zachitika kwa anthu a mitundu ina. Imikani mtengo wachizindikiro ndipo lengezani zimenezi. Musabise chilichonse. Nenani kuti, ‘Babulo walandidwa.+ Beli wachititsidwa manyazi.+ Merodaki wachita mantha. Mafano a Babulo achititsidwa manyazi. Mafano ake onyansawo* achita mantha.’   Chifukwa mtundu wina wa anthu wabwera kudzamuukira kuchokera kumpoto.+ Mtundu umenewu wasandutsa dziko lake kukhala chinthu chochititsa mantha.Palibe aliyense amene akukhala mʼdzikoli. Anthu ndiponso ziweto zathawa.Zathawira kutali.”  “Mʼmasiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo anthu a ku Isiraeli komanso anthu a ku Yuda adzabwera limodzi,”+ akutero Yehova. “Iwo azidzayenda akulira+ ndipo onse pamodzi adzafunafuna Yehova Mulungu wawo.+  Iwo adzafunsira njira yopita ku Ziyoni nkhope zawo zitayangʼana kumeneko.+ Iwo adzanena kuti, ‘Bwerani, tiyeni tikhalenso anthu a Yehova pochita pangano limene lidzakhalapo mpaka kalekale lomwe silidzaiwalika.’+  Anthu anga akhala ngati gulu la nkhosa zosochera.+ Abusa awo ndi amene anawasocheretsa.+ Anawatenga nʼkupita nawo mʼmapiri ndipo ankangowayendetsa kuchoka paphiri kupita pachitunda. Iwo aiwala malo awo opumulirako.  Adani awo akawapeza, akumawadya+ ndipo akumanena kuti, ‘Ife tilibe mlandu uliwonse, chifukwa iwo anachimwira Yehova, malo amene chilungamo chimakhalamo. Anachimwira Yehova, chiyembekezo cha makolo awo.’”   “Thawani mʼBabulo,Tulukani mʼdziko la Akasidi,+Ndipo mukhale ngati mbuzi kapena nkhosa zamphongo zimene zikutsogolera gulu lonse.   Inetu ndikuutsa gulu lalikulu la mitundu yamphamvuNdi kulibweretsa kuchokera kudziko lakumpoto kuti lidzaukire Babulo.+ Mitunduyi idzabwera ili yokonzeka kumenya nkhondoNdipo Babulo adzagonjetsedwa. Mauta awo ndi ofanana ndi mauta a msilikaliAmene akupha ana.+Iwo sabwerera asanachitepo kanthu. 10  Adani adzagonjetsa dziko la Kasidi nʼkulitenga.+ Onse amene adzatenge zinthu zamʼdzikoli adzakhutira,”+ akutero Yehova. 11  “Chifukwa munkasangalala+ komanso kukondweraPamene munkalanda cholowa changa.+ Munkadumphadumpha pamsipu ngati ngʼombe yaikazi imene sinaberekepoNdipo munkamemesa* ngati mahatchi amphongo. 12  Mayi wanu wachititsidwa manyazi.+ Mayi amene anakuberekani wakhumudwa. Taonani! Iye ndi wosafunika kwenikweni pakati pa mitundu ina,Iye ali ngati dera lopanda madzi ndiponso chipululu.+ 13  Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova, mʼdzikomo simudzakhalanso anthu.+Dziko lonselo lidzakhala bwinja.+ Aliyense wodutsa pafupi ndi Babulo adzayangʼanitsitsa mwamanthaNdipo adzamuimbira mluzu chifukwa cha miliri yake yonse.+ 14  Bwerani ndi kuzungulira Babulo kumbali zonse muli okonzeka kumenya nkhondo,Inu nonse amene mumadziwa kukunga uta. Mulaseni ndipo musasunge muvi uliwonse,+Chifukwa iye wachimwira Yehova.+ 15  Mufuulireni mfuu yankhondo kuchokera kumbali zonse. Iye wavomereza kuti wagonja.* Zipilala zake zagwa, mipanda yake yagwetsedwa,+Chifukwa Yehova akumubwezera.+ Inunso mubwezereni. Muchitireni zimene iye anakuchitirani.+ 16  Iphani munthu amene akufesa mbewu mu BabuloNdiponso amene akugwira chikwakwa nthawi yokolola.+ Chifukwa choopa lupanga loopsa, aliyense adzabwerera kwa anthu a mtundu wake,Aliyense adzathawira kudziko lakwawo.+ 17  Anthu a ku Isiraeli ali ngati nkhosa zomwazikana.+ Mikango ndi imene yawabalalitsa.+ Poyamba, mfumu ya Asuri inawadya.+ Kenako Mfumu Nebukadinezara* ya ku Babulo inakukuta mafupa awo.+ 18  Choncho Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: ‘Ine ndilanga mfumu ya Babulo komanso dziko lake ngati mmene ndinalangira mfumu ya Asuri.+ 19  Isiraeli ndidzamubwezeretsa kumalo ake odyerako msipu+ moti adzadya msipu paphiri la Karimeli ndi ku Basana.+ Ndipo iye adzakhutira mʼmapiri a Efuraimu+ ndi Giliyadi.’”+ 20  “Mʼmasiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo,Cholakwa cha Isiraeli chidzafufuzidwa,Koma sichidzapezeka,” akutero Yehova.“Machimo a Yuda sadzapezeka,Chifukwa ine ndidzakhululukira anthu amene ndidzawasiye ndi moyo.”+ 21  “Pitani mukaukire dziko la Merataimu komanso anthu amene akukhala ku Pekodi.+ Iphani anthu onse nʼkuwawonongeratu,” akutero Yehova. “Chitani zonse zimene ndakulamulani. 22  Mʼdzikomo mukumveka phokoso lankhondo,Tsoka lalikulu lawagwera. 23  Taonani! Hamala yophwanyira mitundu ya anthu padziko lonse lapansi yathyoledwa nʼkuwonongedwa.+ Taonani! Babulo wakhala chinthu chochititsa mantha pakati pa anthu a mitundu ina.+ 24  Iwe Babulo ndinakutchera msampha ndipo wakodwa,Koma iwe sunadziwe. Unapezeka ndi kugwidwa,+Chifukwa unkalimbana ndi Yehova. 25  Yehova watsegula nyumba yake yosungiramo zida,Ndipo akutulutsamo zida zimene amagwiritsa ntchito posonyeza mkwiyo wake.+ Chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa, ali ndi ntchito yoti achiteMʼdziko la Akasidi. 26  Bwerani mudzamuukire kuchokera mʼmadera akutali.+ Tsegulani nkhokwe zake.+ Muunjikeni pamodzi ngati milu ya tirigu. Mumuwonongeretu.+ Mʼdzikomo musapezeke aliyense wotsala. 27  Iphani ngʼombe zake zonse zazingʼono zamphongo.+Zonse zipite kokaphedwa. Tsoka kwa iwo, chifukwa tsiku lawo lafika,Nthawi yoti alangidwe yafika. 28  Kukumveka phokoso la anthu amene akuthawa,Amene apulumuka mʼdziko la Babulo,Kuti akanene ku Ziyoni kuti Yehova Mulungu wathu akubwezera adani ake.Akuwabwezera chifukwa cha kuwonongedwa kwa kachisi wake.+ 29  Itanani anthu oponya mivi ndi uta kuti adzaukire Babulo,Anthu onse amene akukunga uta.+ Mangani misasa momuzungulira. Pasapezeke wothawa. Mubwezereni zimene anachita.+ Muchitireni zonse zimene iye anachita.+ Chifukwa iye wachita zinthu modzikuza pamaso pa Yehova,Pamaso pa Woyera wa Isiraeli.+ 30  Choncho anyamata ake adzaphedwa mʼmabwalo a mizinda yake,+Ndipo tsiku limenelo asilikali ake onse adzaphedwa,”* akutero Yehova. 31  “Taona! Ine ndikupatsa chilango,+ iwe Babulo wodzikuza,”+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa.“Chifukwa tsiku lako lifika, nthawi imene ndikuyenera kukupatsa chilango. 32  Iwe Babulo wodzikuza, udzapunthwa nʼkugwa,Ndipo sipadzapezeka aliyense wokudzutsa.+ Mizinda yako ndidzaiyatsa moto,Ndipo motowo udzawononga chilichonse chimene chakuzungulira.” 33  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Aisiraeli komanso Ayuda akuponderezedwa,Ndipo anthu onse amene anawagwira nʼkupita nawo kudziko lina akuwakakamira.+ Akukana kuwalola kuti abwerere kwawo.+ 34  Koma Wowawombola ndi wamphamvu.+ Dzina lake ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+ Iye sadzalephera kuwaweruzira mlandu wawo,+Kuti abweretse mtendere mʼdziko lawo+Ndi kusokoneza mtendere wa anthu okhala mʼBabulo.”+ 35  “Lupanga lidzawononga Akasidi,” akutero Yehova,“Lidzawononga anthu amene akukhala mʼBabulo, akalonga ake ndi anthu ake anzeru.+ 36  Lupanga lidzawononga anthu amene amalankhula zinthu zopanda pake.* Anthu amenewo adzachita zinthu mopanda nzeru. Lupanga lidzawononga asilikali a mʼBabulo, moti adzachita mantha kwambiri.+ 37  Lupanga lidzawononga mahatchi awo, magaleta awo ankhondoNdi anthu onse a mitundu yosiyanasiyana amene ali pakati pawoNdipo adzakhala ngati akazi.+ Lupanga lidzawononga chuma chake ndipo anthu ena adzachitenga.+ 38  Madzi ake adzawonongedwa ndipo adzauma.+ Dziko limeneli ndi la zifaniziro zogoba,+Ndipo anthu ake amachita zinthu ngati amisala chifukwa cha masomphenya awo ochititsa mantha. 39  Choncho nyama zamʼchipululu zidzakhala mmenemo pamodzi ndi nyama zolira mokuwa,Ndipo nthiwatiwa zidzakhala mmenemo.+ Mumzindawo simudzakhalanso munthu aliyense,Ndipo sudzakhala malo oti munthu nʼkukhalamo ku mibadwo yonse.”+ 40  “Mofanana ndi mmene Mulungu anawonongera Sodomu ndi Gomora+ komanso midzi imene anali nayo pafupi,+ ndi mmenenso zidzakhalire ndi Babulo. Palibe aliyense amene adzakhalenso mumzindawo,”+ akutero Yehova. 41  “Taona! Mtundu wa anthu ukubwera kuchokera kumpoto.Mtundu wamphamvu ndi mafumu akuluakulu+ adzakonzekera kuukiraKuchokera kumadera akutali kwambiri a dziko lapansi.+ 42  Iwo amadziwa kuponya mivi ndi uta komanso nthungo.+ Amenewo ndi anthu ankhanza ndipo sadzakumvera chifundo.+ Phokoso lawo lili ngati phokoso la nyanja imene ikuchita mafunde.+Amachita phokosoli akakwera pamahatchi. Mogwirizana, iwo ayalana pokonzekera kumenyana nawe, iwe mwana wamkazi wa Babulo.*+ 43  Mfumu ya Babulo yamva za iwo,+Ndipo manja ake alefuka chifukwa chotaya mtima.+ Ikuda nkhawaNdipo ikumva zowawa ngati mkazi amene akubereka. 44  Taona! Wina adzabwera ngati mkango kuchokera munkhalango zowirira zamʼmphepete mwa Yorodano. Adzabwera kudzaukira malo otetezeka odyetserako ziweto, koma mʼkanthawi kochepa ndidzawathamangitsa* pamalowo. Ndidzaika pamalopo mtsogoleri amene ndamusankha.+ Chifukwa ndi ndani amene angafanane ndi ine ndipo ndi ndani angatsutsane nane? Kodi pali mʼbusa amene angakane kuchita zimene ine ndikufuna?+ 45  Tsopano amuna inu, tamverani zimene Yehova wasankha* kuchitira Babulo+ ndiponso zimene waganiza kuti achitire dziko la Akasidi. Ndithudi, chilombo chidzakokera kutali ana a nkhosa. Adzachititsa kuti malo awo okhala asanduke bwinja chifukwa cha zimene anthuwo anachita.+ 46  Phokoso limene lidzamveke Babulo akadzagwidwa lidzachititsa kuti dziko lapansi ligwedezeke,Ndipo kulira kudzamveka pakati pa mitundu ya anthu.”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake a Chiheberi amatanthauzanso “ndowe,” ndipo amagwiritsidwa ntchito ngati mawu onyoza.
Mawu akuti “kumemesa” amatanthauza zimene nyama yamphongo imachita ikafuna kukwera.
Mʼchilankhulo choyambirira, “wapereka dzanja lake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzakhalitsidwa chete.”
Kapena kuti, “lidzawononga aneneri abodza.”
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Babulo” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Babulo kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Zikuoneka kuti akunena Ababulo.
Kapena kuti, “akufuna.”