Yeremiya 21:1-14

  • Yehova anakana zimene Zedekiya anapempha (1-7)

  • Anthu ayenera kusankha pakati pa moyo ndi imfa (8-14)

21  Yeremiya analandira mawu ochokera kwa Yehova pamene Mfumu Zedekiya+ inatumiza Pasuri+ mwana wa Malikiya ndi Zefaniya+ mwana wa Maaseya, wansembe, kuti akamupemphe kuti:  “Chonde tifunsire kwa Yehova chifukwa Nebukadinezara,* mfumu ya ku Babulo, akufuna kuchita nafe nkhondo.+ Mwina Yehova atichitira imodzi mwa ntchito zake zodabwitsa moti Nebukadinezarayo atichokera.”+  Yeremiya anawauza kuti: “Mukauze Zedekiya kuti,  ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ine ndichititsa zida zankhondo zimene zili mʼmanja mwanu kukutembenukirani. Zimenezi ndi zida zimene mukugwiritsa ntchito pomenyana ndi mfumu ya Babulo+ ndi Akasidi amene akuzungulirani kunja kwa mpanda wanu. Ndipo ine ndidzasonkhanitsa zidazo pakati pa mzindawu.  Ine ndidzamenyana nanu+ ndi mkono wotambasula ndiponso dzanja lamphamvu. Ndidzachita zimenezi nditakwiya, nditapsa mtima komanso ndili ndi ukali waukulu.+  Ndidzapha onse okhala mumzindawu, anthu komanso nyama. Adzafa ndi mliri waukulu.”’*+  ‘Yehova wanena kuti: “Kenako Zedekiya mfumu ya Yuda, atumiki ake ndi anthu amumzindawu, onse amene adzapulumuke ku mliri, lupanga ndi njala yaikulu, ndidzawapereka mʼmanja mwa Mfumu Nebukadinezara* ya ku Babulo. Ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo komanso mʼmanja mwa amene akufuna kuchotsa moyo wawo.+ Nebukadinezara adzawapha ndi lupanga ndipo sadzawamvera chisoni, kuwakomera mtima kapena kuwachitira chifundo.”’+  Ndipo anthu awa uwauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Ine ndikuika njira ya moyo ndi njira ya imfa pamaso panu.  Anthu amene adzatsale mumzindawu adzafa ndi lupanga, njala ndiponso mliri. Koma aliyense amene adzatuluke nʼkupita kukadzipereka mʼmanja mwa Akasidi amene akuzungulirani, adzakhalabe ndi moyo. Iye adzapulumutsa moyo wake.”’+ 10  ‘“Ndatsimikiza kubweretsa tsoka pamzinda uwu, osati zinthu zabwino,”*+ akutero Yehova. “Mzindawu udzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya Babulo+ ndipo adzauwotcha ndi moto.”+ 11  A mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ukawauze kuti: Imvani zimene Yehova wanena. 12  Inu a mʼnyumba ya Davide, Yehova wanena kuti: “Mʼmawa uliwonse muziweruza mwachilungamoNdipo muzipulumutsa munthu amene akuberedwa mʼmanja mwa anthu akuba mwachinyengo,+Kuti mkwiyo wanga usayake ngati moto.+Usayake popanda aliyense wouzimitsaChifukwa cha zinthu zoipa zimene mukuchita.”’+ 13  ‘Iwe amene umakhala mʼchigwa, ine ndakuukira,Iwe thanthwe limene lili pamalo afulati,’ akutero Yehova. ‘Koma inu amene mukunena kuti: “Kodi ndi ndani amene adzabwere kuno kuti atiukire? Ndipo ndi ndani amene adzabwere mʼmalo athu okhala?” 14  Ndidzakupatsani chilangoMogwirizana ndi zochita zanu,’+ akutero Yehova. ‘Ndipo ndidzayatsa moto munkhalango za mzindawu,Moti udzapsereza zinthu zonse zimene zili pafupi ndi mzindawu.’”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “matenda aakulu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nkhope yanga ili pa mzinda uwu kuti ndiuwononge.”