Yeremiya 30:1-24

  • Malonjezo okhudza kubwezeretsedwa mwakale komanso kuchiritsidwa (1-24)

30  Mawu amene Yehova anauza Yeremiya ndi awa:  “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Lemba mʼbuku mawu onse amene ndikukuuza.  “Taona! masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzasonkhanitsa Isiraeli ndi Yuda,+ anthu anga amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina,” akutero Yehova. “Iwo ndidzawabwezeretsa kudziko limene ndinapatsa makolo awo ndipo adzalitenga kuti likhalenso lawo.”’”+  Awa ndi mawu amene Yehova anauza Isiraeli ndi Yuda.   Yehova wanena kuti: “Ife tamva phokoso la anthu amene akunjenjemera.Iwo agwidwa ndi mantha ndipo palibe mtendere.   Tafunsani, kodi mwamuna angabereke mwana? Nanga nʼchifukwa chiyani ndikuona mwamuna aliyense wamphamvu atagwira manja pamimba* pakeNgati mkazi amene akubereka?+ Nʼchifukwa chiyani aliyense nkhope yake yafooka?   Mayo ine! Chifukwa tsiku limenelo lidzakhala lochititsa mantha.*+ Ndipo palibe lofanana nalo.Tsiku limenelo lidzakhala lamavuto kwa Yakobo. Koma adzapulumutsidwa mʼmavuto amenewa.  Pa tsiku limenelo ndidzathyola goli limene lili mʼkhosi lanu. Ndidzadula pakati zingwe zimene akumangani nazo, moti anthu achilendo sadzachititsanso kuti Yakobo akhale kapolo wawo,” akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.  “Inu mudzatumikira Yehova Mulungu wanu ndi Davide mfumu yanu imene ndidzakupatseni.+ 10  Koma iwe Yakobo mtumiki wanga usachite mantha,” akutero Yehova,“Ndipo iwe Isiraeli usaope.+ Chifukwa ndidzakupulumutsa kuchokera kutaliNdidzapulumutsanso ana ako kuchokera kudziko limene anatengedwa kukakhala akapolo.+ Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala mosatekeseka komanso mopanda zosokoneza.Sipadzakhala wowaopseza.+ 11  Chifukwa ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse,” akutero Yehova. “Ndidzawononga anthu a mitundu yonse yakumene ndinakubalalitsirani.+Koma iweyo sindidzakuwononga.+ Ndidzakulanga* pamlingo woyenera,Ndipo sindidzakusiya osakupatsa chilango.”+ 12  Yehova wanena kuti: “Kuwonongeka kwako ndi kosachiritsika.+ Ndiponso bala lako ndi losachiritsika. 13  Palibe woti akuchonderere pa mlandu wako.Palibe njira iliyonse yochiritsira bala lako. Ndipo palibe mankhwala amene angakuchiritse. 14  Onse amene ankakukonda kwambiri akuiwala.+ Iwo sakukufunafunanso. Ndakumenya ngati mmene angakumenyere mdani,+Ndipo ndakulanga ngati mmene angakulangire munthu wankhanza,Chifukwa cha kulakwa kwako kwakukulu ndi kuchuluka kwa machimo ako.+ 15  Kodi pali chifukwa choti udandaulire ndi chilango chimene wapatsidwa? Ululu wako ndi wosachiritsika. Chifukwa cha kulakwa kwako kwakukulu ndi kuchuluka kwa machimo ako,+Ine ndakuchitira zimenezi. 16  Choncho onse okuwononga adzawonongedwa,+Ndipo adani ako onse nawonso adzatengedwa kupita ku ukapolo.+ Amene akulanda katundu wako nawonso adzalandidwa katundu wawo.Ndipo anthu onse amene akulanda zinthu zako ndidzawapereka mʼmanja mwa olanda zinthu.+ 17  Ndidzakuchititsa kuti ukhalenso wathanzi ndipo ndidzapoletsa mabala ako,”+ akutero Yehova.“Ngakhale kuti anakana kukulandira ndipo anakutchula kuti: ‘Ziyoni amene palibe amene akumufunafuna.’”+ 18  Yehova wanena kuti: “Ndikusonkhanitsa anthu amʼmatenti a Yakobo amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina,+Ndipo ndidzamvera chisoni malo okhala a Yakobo. Mzinda udzamangidwanso pamalo amene unali poyamba,+Ndipo nsanja yokhala ndi mpanda wolimba idzakhala pamalo ake oyenerera. 19  Kwa iwo kudzamveka mawu oyamikira ndi phokoso la kuseka kwa anthu.+ Ndidzawachulukitsa moti sadzakhala ochepa.+Ndidzawachititsa kuti akhale ambiri,*Ndipo sadzakhala anthu ochepa.+ 20  Ana ake aamuna zinthu zidzawayendera bwino ngati mmene zinalili poyamba,Ndipo ndidzawapangitsa kuti akhale anthu amphamvu pamaso panga.+ Ndidzalanga anthu onse amene amamupondereza.+ 21  Mtsogoleri wake adzachokera pakati pa anthu ake,Ndipo wolamulira wake adzachokera pakati pa mbadwa zake. Ndidzamulola kuti andiyandikire ndipo adzabwera kwa ine. Chifukwa ndi ndani amene angalimbe mtima kuti andiyandikire?” akutero Yehova. 22  “Inu mudzakhala anthu anga+ ndipo ine ndidzakhala Mulungu wanu.”+ 23  Taonani! Mkwiyo wa Yehova udzawomba ngati mphepo yamkuntho,+Udzawomba ngati kamvulumvulu wamphamvu pamitu ya anthu oipa. 24  Mkwiyo woyaka moto wa Yehova sudzabwereraMpaka atachita komanso kukwaniritsa zofuna za mtima wake.+ Mʼmasiku otsiriza, mudzamvetsa zimenezi.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “mʼchiuno.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “lidzakhala lalikulu.”
Kapena kuti, “Ndidzakulangiza.”
Mabaibulo ena amati, “Ndidzawapatsa ulemerero.”