Yeremiya 18:1-23

  • Dongo mʼdzanja la wowumba (1-12)

  • Yehova adzafulatira Isiraeli (13-17)

  • Chiwembu chimene anakonzera Yeremiya komanso kuchonderera kwake (18-23)

18  Mawu amene Yehova anauza Yeremiya ndi awa:  “Nyamuka, upite kunyumba ya woumba mbiya+ ndipo ndikakuuza mawu anga kumeneko.”  Choncho ndinapita kunyumba ya woumba mbiya, ndipo ndinamupeza akugwira ntchito yake pamalo oumbira mbiya.  Koma chiwiya chimene woumba mbiyayo ankapanga ndi dongo chinawonongeka mʼmanja mwake. Choncho iye anasintha nʼkupanga chiwiya china ndi dongo lomwelo, malinga ndi zimene anaona kuti nʼzabwino.  Kenako Yehova anandiuza kuti:  “‘Inu a nyumba ya Isiraeli, kodi sindingakuchiteni zofanana ndi zimene woumba mbiyayu anachita?’ akutero Yehova. ‘Tamverani! Mofanana ndi dongo limene lili mʼmanja mwa woumba mbiya, ndi mmene inunso mulili kwa ine, inu nyumba ya Isiraeli.+  Nthawi iliyonse imene ndinganene kuti ndizula, kugwetsa ndi kuwononga mtundu uliwonse wa anthu kapena ufumu,+  ndiyeno mtundu wa anthuwo nʼkusiya zoipa zimene ndinawadzudzula nazo, inenso ndidzasintha maganizo anga okhudza tsoka limene ndimafuna kuwagwetsera.+  Koma nthawi iliyonse imene ndinganene kuti ndimanga ndi kudzala mtundu wa anthu kapena ufumu, 10  ndiyeno mtundu wa anthuwo nʼkumachita zoipa pamaso panga ndiponso osamvera mawu anga, inenso ndidzasintha maganizo anga okhudza zinthu zabwino zimene ndinkafuna kuwachitira.’ 11  Tsopano uza anthu a mu Yuda ndi anthu okhala mu Yerusalemu kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Inetu ndikukukonzerani tsoka ndipo ndikuganizira njira yokulangirani. Chonde, bwererani nʼkusiya njira zanu zoipa. Sinthani zochita zanu ndi makhalidwe anu.”’”+ 12  Koma iwo anati: “Zimenezo ayi!+ Ife titsatira maganizo athu, ndipo aliyense wa ife adzachita zinthu mouma khosi, mogwirizana ndi mtima wake woipa.”+ 13  Choncho Yehova wanena kuti: “Funsafunsani pakati pa mitundu ya anthu. Ndi ndani amene anamvapo zoterezi? Namwali wa Isiraeli wachita chinthu choopsa kwambiri.+ 14  Kodi sinowo wamʼmapiri a ku Lebanoni amasungunuka* nʼkuchoka pamiyala yake? Kapena kodi madzi ozizira bwino amene akuyenda kuchokera kutali adzauma? 15  Koma anthu anga andiiwala.+ Chifukwa akupereka nsembe* kwa chinthu chopanda pake+Ndipo akuchititsa kuti anthu amene akuyenda mʼnjira zawo, mʼnjira zakale, apunthwe,+Akuwachititsa kuti ayende mʼnjira zolakwika zomwe ndi zokumbikakumbika.* 16  Choncho dziko lawo lidzakhala chinthu chochititsa mantha+Komanso chimene anthu azidzachiimbira mluzu mpaka kalekale.+ Aliyense wodutsa pafupi ndi dzikoli adzaliyangʼanitsitsa mwamantha ndipo adzapukusa mutu wake.+ 17  Ndidzawamwaza pamaso pa adani awo ngati mmene mphepo yochokera kumʼmawa imamwazira fumbi. Sindidzawaonetsa nkhope yanga, koma ndidzawafulatira pa tsiku la tsoka lawo.”+ 18  Iwo ananena kuti: “Tabwerani, tiyeni timukonzere chiwembu Yeremiya,+ chifukwa ansembe adzapitiriza kutiphunzitsa chilamulo.* Anthu athu anzeru sadzasiya kutipatsa malangizo ndipo aneneri adzapitiriza kutiuza mawu a Mulungu. Bwerani, tiyeni titsutsane naye* ndipo tisamvere zimene akunena.” 19  Ndimvereni, inu Yehova,Ndipo imvani zimene adani anga akunena. 20  Kodi akuyenera kubwezera zinthu zoipa pa zinthu zabwino? Iwo akumba dzenje kuti achotse moyo wanga.+ Kumbukirani kuti ndinkaima pamaso panu nʼkumalankhula zabwino zokhudza anthu amenewa,Kuti muwachotsere mkwiyo wanu. 21  Choncho lolani kuti ana awo afe ndi njala,Komanso aphedwe ndi lupanga.+ Akazi awo akhale amasiye ndipo ana a akaziwo afe.+ Amuna awo afe ndi mliri woopsaNdipo anyamata awo aphedwe ndi lupanga pankhondo.+ 22  Mʼnyumba zawo mumveke kuliraMukawabweretsera magulu achifwamba mwadzidzidzi. Chifukwa akumba dzenje kuti andigwireNdipo atchera misampha kuti akole mapazi anga.+ 23  Koma inu Yehova,Mukudziwa bwino ziwembu zawo zonse zimene andikonzera kuti andiphe.+ Musawakhululukire cholakwa chawo,Ndipo musafafanize tchimo lawo pamaso panu. Iwo apunthwe pamaso panu+Pamene mukuwapatsa chilango mutakwiya.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “chipale chofewa chamʼmapiri a ku Lebanoni chimasungunuka.”
Kapena kuti, “nsembe zautsi.”
Kapena kuti, “zosalimidwa.”
Kapena kuti, “malangizo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “tiyeni timumenye ndi lilime.”