Yeremiya 4:1-31

  • Kulapa kumabweretsa madalitso (1-4)

  • Tsoka lidzachokera kumpoto (5-18)

  • Yeremiya anamva kupweteka mumtima chifukwa cha tsoka limene linkabwera (19-31)

4  Yehova wanena kuti: “Ngati ungabwerere, iwe Isiraeli,Ngati ungabwerere kwa ineNdipo ngati ungachotse mafano ako onyansa pamaso panga,Sudzakhalanso moyo wothawathawa.+   Ndipo ngati ungalumbire,Mʼchoonadi komanso mwachilungamo kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo,’Ndiye kuti mitundu ya anthu idzapeza madalitso kudzera mwa iyeNdipo idzauza ena za iye monyadira.”+  Zimene Yehova wanena kwa anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu ndi izi: “Limani minda panthaka yabwino,Ndipo musapitirize kudzala mbewu pakati pa minga.+   Chitani mdulidwe pamaso pa Yehova,Chitani mdulidwe wa mitima yanu,+Inu anthu a ku Yuda komanso anthu amene mukukhala mu Yerusalemu,Kuti mkwiyo wanga usayake ngati moto,Usayake popanda aliyense wowuzimitsa,Chifukwa cha zochita zanu zoipa.”+   Nenani zimenezi mu Yuda ndipo zilengezeni mu Yerusalemu. Fuulani ndi kuliza lipenga la nyanga ya nkhosa mʼdziko lonse.+ Fuulani ndipo nenani kuti: “Sonkhanani pamodzi,Tiyeni tithawire mʼmizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+   Kwezani chizindikiro choloza njira ya ku Ziyoni. Thawirani kumalo otetezeka, musangoima,” Chifukwa ndikubweretsa tsoka kuchokera kumpoto,+ tsoka lalikulu kwambiri.   Mofanana ndi mkango umene ukutuluka paziyangoyango pamene umakhala,+Amene akuwononga mitundu ya anthu wanyamuka.+ Wachoka mʼmalo ake kuti adzasandutse dziko lanu chinthu chochititsa mantha. Mizinda yanu idzakhala mabwinja ndipo palibe munthu aliyense amene adzakhalemo.+   Choncho valani ziguduli,+Dzigugudeni pachifuwa ndi kulira mofuula,Chifukwa mkwiyo woyaka moto wa Yehova sunatichokere.   Yehova wanena kuti: “Pa tsiku limenelo mfumu sidzalimba mtima,+Chimodzimodzinso akalonga ake.Ansembe adzagwidwa ndi mantha ndipo aneneri adzadabwa.”+ 10  Kenako ndinanena kuti: “Mayo ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Kunena zoona, mwapusitsa kwambiri anthu awa+ ndiponso Yerusalemu ponena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’+ pamene lupanga lili pakhosi pathu.”* 11  Pa nthawi imeneyo anthu awa komanso Yerusalemu adzauzidwa kuti: “Mphepo yotentha imene ikuchokera mʼmapiri opanda kanthu amʼchipululu,Idzaomba pamwana wamkazi wa anthu anga.Mphepo imeneyi sikubwera kuti idzauluze mankhusu* kapena kudzayeretsa tirigu. 12  Mphepo yamphamvu ikubwera kuchokera mʼmalo amenewa chifukwa choti ine ndalamula. Tsopano ndipereka ziweruzo kwa anthu anga. 13  Taonani! Mdani adzabwera ngati mitambo yamvula,Ndipo magaleta ake ali ngati mphepo yamkuntho.+ Mahatchi ake ndi aliwiro kuposa ziwombankhanga.+ Tsoka latigwera chifukwa tawonongedwa. 14  Tsuka mtima wako nʼkuchotsa zoipa zonse, iwe Yerusalemu, kuti upulumuke.+ Kodi udzakhala ndi maganizo oipa mpaka liti? 15  Chifukwa mawu olengeza uthenga akumveka kuchokera ku Dani,+Ndipo akulengeza za tsoka kuchokera kumapiri a ku Efuraimu. 16  Nenani zimenezi kwa anthu a mitundu ina.Lengezani kuti zimenezi zidzachitikira Yerusalemu.” “Akazitape* akubwera kuchokera kudziko lakutaliNdipo adzalengeza mofuula zimene zidzachitikire mizinda ya Yuda. 17  Iwo aukira Yerusalemu kuchokera mbali zonse ngati alonda a kunja kwa mzinda,+Chifukwa iye wandipandukira,”+ akutero Yehova. 18  “Udzalipira chifukwa cha khalidwe lako ndi zochita zako.+ Chilango chimenechi chidzakhala chowawa,Chifukwa zochita zako zakhazikika mumtima mwako.” 19  Mayo ine,* mayo ine! Ndikumva kupweteka kwambiri mumtima mwanga. Mtima wanga ukugunda kwambiri. Sindingathe kukhala chete,Chifukwa ndamva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa,Chizindikiro chochenjeza cha nkhondo.*+ 20  Ndikumva uthenga wa masoka otsatizanatsatizana,Chifukwa dziko lonse lawonongedwa. Mwadzidzidzi matenti anga awonongedwaMʼkanthawi kochepa nsalu za matenti anga zawonongedwa.+ 21  Kodi ndipitiriza kuona chizindikirocho,Ndi kumva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosako mpaka liti?+ 22  “Anthu anga ndi opusa.+Iwo saganizira za ine. Ndi ana opusa ndipo samvetsa zinthu. Amaoneka ochenjera* akamachita zoipa,Koma sadziwa kuchita zabwino.” 23  Ndinaliona dzikolo ndipo linali lopanda kanthu komanso linangosiyidwa.+ Ndinayangʼana kumwamba ndipo sikunkawala.+ 24  Ndinaona mapiri ndipo ankagwedezeka,Ndipo zitunda zinkanjenjemera.+ 25  Ndinayangʼana koma panalibe munthu aliyense,Ndipo mbalame zonse zinali zitathawa.+ 26  Ndinayangʼana ndipo ndinaona kuti munda wa zipatso unali utasanduka thengo,Komanso mizinda yake yonse inali itagwetsedwa.+ Zimenezi zinachitika chifukwa cha Yehova,Chifukwa cha mkwiyo wake woyaka moto. 27  Yehova wanena kuti: “Dziko lonseli lidzakhala bwinja,+Koma sindidzaliwonongeratu. 28  Pachifukwa chimenechi dzikolo lidzalira,+Ndipo kumwamba kudzachita mdima.+ Izi zili choncho chifukwa ndanena, ndasankha kuchita zimenezi,Ndipo sindidzasintha maganizo anga* kapena kulephera kuchita zimenezi.+ 29  Chifukwa cha phokoso la asilikali okwera pamahatchi ndiponso oponya mivi ndi uta,Mzinda wonse wathawa.+ Alowa paziyangoyango,Ndipo akwera mʼmatanthwe.+ Mumzinda uliwonse anthu athawamoNdipo palibe munthu amene akukhalamo.” 30  Popeza tsopano wawonongedwa, ndiye utani? Unkakonda kuvala zovala zamtengo wapatali,*Kudzikongoletsa ndi zokongoletsera zagolideNdiponso kukongoletsa mʼmaso mwako ndi penti wakuda. Koma unkangotaya nthawi yako pachabe podzikongoletsa.+Amene ankakufuna akukanaNdipo tsopano akufuna kukupha.+ 31  Ine ndamva mawu angati a mkazi amene akumva ululu,Ndamva ngati kubuula kwa mkazi amene akubereka mwana wake woyamba,Koma ndi mawu a mwana wamkazi wa Ziyoni* amene akupuma movutikira. Iye akutambasula manja ake nʼkunena kuti:+ “Mayo ine, ndatopa ndi anthu amene akufuna kundipha!”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “pamene lupanga latibaya mumtima.”
“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Oona zochitika.” Amenewa ndi anthu amene ankaona zimene zikuchitika mumzinda kuti adziwe nthawi yoyenera kuukira mzindawo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mʼmatumbo mwanga ine.”
Mabaibulo ena amati, “Mfuwu ya nkhondo.”
Kapena kuti, “anzeru.”
Kapena kuti, “Ndipo sindidzamva chisoni.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zovala zofiira,” kutanthauza zovala zofiira zamtengo wapatali.
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.