Yeremiya 44:1-30

  • Ananeneratu za tsoka limene lidzagwere Ayuda ku Iguputo (1-14)

  • Anthu anakana kumvera zimene Mulungu anawachenjeza (15-30)

    • Ankalambira “Mfumukazi Yakumwamba” (17-19)

44  Mulungu anauza Yeremiya uthenga woti akauze Ayuda onse amene ankakhala mʼdziko la Iguputo,+ mʼmadera a Migidoli,+ Tahapanesi,+ Nofi*+ ndi Patirosi.+ Uthengawo unali wakuti:  “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Inu mwaona masoka onse amene ndinagwetsera Yerusalemu+ ndi mizinda yonse ya Yuda. Lero mizinda imeneyi ndi mabwinja okhaokha ndipo palibe amene akukhalamo.+  Izi zinachitika chifukwa cha zinthu zoipa zimene ankachita nʼkundikhumudwitsa nazo. Iwo ankapitiriza kupereka nsembe+ ndi kutumikira milungu ina imene inuyo, iwowo kapena makolo anu simunkaidziwa.+  Ine ndinkakutumizirani mobwerezabwereza* atumiki anga onse amene ndi aneneri. Ndinkawatuma uthenga wakuti: “Chonde, musachite zinthu zonyansazi zimene ndimadana nazo.”+  Koma sanamvere kapena kutchera khutu lawo kuti asiye kuchita zinthu zoipa zomwe ndi kupereka nsembe kwa milungu ina.+  Choncho ndinasonyeza mkwiyo wanga ndi ukali wanga ndipo unayaka mʼmizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya Yerusalemu moti mizinda imeneyi inakhala mabwinja komanso malo owonongeka ngati mmene zilili lero.’+  Tsopano Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mukudziitanira tsoka lalikulu? Kodi simukudziwa kuti muphetsa amuna, akazi, ana ndi ana aangʼono mu Yuda, moti sipapezeka aliyense wotsala?  Nʼchifukwa chiyani mukufuna kundikhumudwitsa ndi ntchito za manja anu popereka nsembe kwa milungu ina mʼdziko la Iguputo kumene mwapita kuti muzikakhala? Muwonongedwa ndipo aliyense azidzakutembererani ndi kukunyozani pakati pa anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi.+  Kodi mwaiwala zoipa zimene makolo anu, mafumu a Yuda+ komanso akazi awo ankachita?+ Kodi mwaiwala zinthu zoipa zimene inuyo ndi akazi anu+ munkachita mʼdziko la Yuda ndi mʼmisewu ya ku Yerusalemu? 10  Iwo sanadzichepetse* mpaka lero, sanasonyeze mantha aliwonse+ kapena kutsatira malamulo ndi malangizo anga amene ndinapatsa inu ndi makolo anu.’+ 11  Choncho Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ine ndatsimikiza kukugwetserani tsoka, kuti ndiwononge anthu onse a mu Yuda. 12  Ine ndigwira anthu amene anatsala ku Yuda omwe anatsimikiza mtima kuti apite mʼdziko la Iguputo nʼkumakakhala kumeneko, moti onsewo adzafera mʼdziko la Iguputo.+ Iwo adzaphedwa ndi lupanga komanso adzafa ndi njala. Kuyambira munthu wamba ndi wolemekezeka yemwe, onse adzaphedwa ndi lupanga komanso adzafa ndi njala. Iwo adzakhala otembereredwa, chinthu chochititsa mantha, chinthu chonyozeka ndi chochititsa manyazi.+ 13  Ndidzalanga anthu onse okhala mʼdziko la Iguputo ngati mmene ndinalangira Yerusalemu. Ndidzawalanga ndi lupanga, njala ndi mliri.*+ 14  Ndipo anthu otsala a ku Yuda amene apita kukakhala mʼdziko la Iguputo sadzathawa kapena kupulumuka kuti abwerere kudziko la Yuda. Adzafunitsitsa kubwerera kuti akakhale kumeneko koma sadzabwerera kupatulapo anthu ochepa amene adzathawe.’” 15  Ndiyeno amuna onse amene ankadziwa kuti akazi awo ankapereka nsembe kwa milungu ina, akazi onse amene anaimirira nʼkupanga gulu lalikulu komanso anthu onse amene ankakhala ku Iguputo+ mʼdera la Patirosi,+ anayankha Yeremiya kuti: 16  “Ife sitimvera mawu amene watiuza mʼdzina la Yehova. 17  Mʼmalomwake tichitadi zonse zimene tanena. Tipereka nsembe komanso tithira nsembe zachakumwa kwa Mfumukazi Yakumwamba.*+ Tichita zimenezi mofanana ndi mmene ife, makolo athu, mafumu athu ndi akalonga athu anachitira mʼmizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya Yerusalemu pamene tinkadya mkate nʼkukhuta ndipo zinthu zinkatiyendera bwino, moti sitinaone tsoka lililonse. 18  Ndipotu kungoyambira nthawi imene tinasiya kupereka nsembe ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa Mfumukazi Yakumwamba,* tikusowa chilichonse ndipo tawonongeka ndi lupanga komanso njala.” 19  Akaziwo anawonjezera kuti: “Ndipo pamene tinkapereka nsembe ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa Mfumukazi Yakumwamba,* kodi amuna athu sanavomereze kuti tipangire Mfumukaziyo makeke oti tikapereke nsembe opangidwa mʼchifanizo chake ndiponso kuti tipereke kwa iye nsembe zachakumwazo?” 20  Kenako Yeremiya anauza anthu onse, amuna ndi akazi awo komanso anthu onse amene ankalankhula naye kuti: 21  “Nsembe zimene inuyo, makolo anu, mafumu anu, akalonga anu ndi anthu amʼdzikolo ankapereka mʼmizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya Yerusalemu,+ Yehova anazikumbukira ndipo zinalowa mumtima mwake. 22  Kenako Yehova sakanathanso kulekerera zinthu zoipa komanso zonyansa zimene munkachita ndipo dziko lanu linasanduka bwinja, chinthu chochititsa mantha ndi chotembereredwa, dziko lopanda munthu wokhalamo ngati mmene ziliri lero.+ 23  Masoka onsewa akugwerani ngati mmene ziliri lero chifukwa chakuti munkapereka nsembe zimenezi komanso chifukwa chakuti munachimwira Yehova. Munachita zimenezi polephera kumvera mawu a Yehova, kutsatira malamulo ake, malangizo ndi zikumbutso zake.”+ 24  Ndiyeno Yeremiya anapitiriza kuuza anthu onse ndi akazi onse kuti: “Tamverani mawu a Yehova inu nonse a ku Yuda amene muli ku Iguputo kuno. 25  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Zimene inu ndi akazi anu mwanena mwazikwaniritsadi ndi manja anu chifukwa munanena kuti: “Ife tidzakwaniritsa malonjezo athu akuti tidzapereka nsembe kwa Mfumukazi Yakumwamba* ndi kuti tidzapereka nsembe yachakumwa kwa iye.”+ Akazi inu muchitadi zimene mwalonjeza ndipo mukwaniritsadi malonjezo anu.’ 26  Choncho imvani mawu a Yehova, inu nonse a ku Yuda amene mukukhala mʼdziko la Iguputo. Yehova wanena kuti: “Ine ndikulumbira pa dzina langa lalikulu kuti mʼdziko lonse la Iguputo simudzapezeka munthu aliyense wa ku Yuda+ wolumbira mʼdzina langa kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo, Ambuye Wamkulu Koposa!’+ 27  Ine ndine wokonzeka kuwabweretsera tsoka, osati zinthu zabwino.+ Anthu onse a ku Yuda amene ali mʼdziko la Iguputo adzafa ndi lupanga ndiponso njala mpaka atatheratu.+ 28  Anthu ochepa okha adzathawa lupanga mʼdziko la Iguputo nʼkubwerera kudziko la Yuda.+ Ndipo pa nthawiyo, anthu amene anatsala mu Yuda amene anabwera mʼdziko la Iguputo kuti azikhalamo adzadziwa kuti mawu amene akwaniritsidwa ndi a ndani, mawu anga kapena mawu awo.”’” 29  “Yehova wanena kuti: ‘Ndikupatsani chizindikiro chosonyeza kuti ndidzakulangani mʼdziko lino kuti mudziwe kuti mawu anga akuti ndidzakubweretserani tsoka adzakwaniritsidwadi. 30  Yehova wanena kuti: “Ine ndikupereka Farao Hofira, mfumu ya Iguputo, mʼmanja mwa adani ake ndiponso mʼmanja mwa amene akufuna kuchotsa moyo wake, mofanana ndi mmene ndinaperekera Zedekiya mfumu ya Yuda mʼmanja mwa Nebukadinezara* mfumu ya Babulo, amene anali mdani wake komanso amene ankafuna kumupha.”’”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Memfisi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ine ndinkadzuka mʼmawa kwambiri nʼkutumiza.”
Kapena kuti, “Iwo sanadzimvere chisoni.”
Kapena kuti, “matenda.”
Limeneli ndi dzina laulemu la mulungu wamkazi amene Aisiraeli opanduka ankamulambira. Iwo ankakhulupirira kuti ameneyu ndi mulungu amene ankathandiza akazi kuti azibereka.
Limeneli ndi dzina laulemu la mulungu wamkazi amene Aisiraeli opanduka ankamulambira. Iwo ankakhulupirira kuti ameneyu ndi mulungu amene ankathandiza akazi kuti azibereka.
Limeneli ndi dzina laulemu la mulungu wamkazi amene Aisiraeli opanduka ankamulambira. Iwo ankakhulupirira kuti ameneyu ndi mulungu amene ankathandiza akazi kuti azibereka.
Limeneli ndi dzina laulemu la mulungu wamkazi amene Aisiraeli opanduka ankamulambira. Iwo ankakhulupirira kuti ameneyu ndi mulungu amene ankathandiza akazi kuti azibereka.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.