Yeremiya 47:1-7

  • Ulosi wokhudza Afilisiti (1-7)

47  Yehova anauza mneneri Yeremiya mawu okhudza Afilisiti,+ Farao asanagonjetse mzinda wa Gaza.  Yehova wanena kuti: “Taonani! Madzi akubwera kuchokera kumpoto. Madzi ake adzakhala mtsinje wosefukira. Ndipo adzakokolola dziko ndi zonse zimene zili mmenemo.Adzakokololanso mzinda ndi onse amene akukhala mmenemo. Amuna adzalira,Ndipo aliyense amene akukhala mʼdzikolo adzalira mofuula.   Abambo adzathawa osayangʼana mʼmbuyo kuti apulumutse ana awo.Adzachita zimenezi chifukwa manja awo adzafooka,Akadzamva mgugu wa mahatchi a adani awo,Akadzamva phokoso la magaleta ankhondo a adani awoKomanso kulira kwa mawilo ake,   Chifukwa tsiku limene likubweralo lidzawononga Afilisiti+ onse.Lidzawononga aliyense wotsala amene akuthandiza Turo+ ndi Sidoni.+ Chifukwa Yehova adzawononga Afilisiti,Amene ndi otsala ochokera pachilumba cha Kafitori.*+   Gaza adzameta mpala chifukwa cha chisoni. Asikeloni amukhalitsa chete.+ Inu otsala amʼchigwa cha Gaza ndi Asikeloni,Kodi mupitiriza kudzichekacheka mpaka liti?+   Aa! iwe lupanga la Yehova.+ Kodi sukhala chete mpaka liti? Bwerera mʼchimake. Upume ndipo ukhale chete.   “Kodi lingakhale bwanji cheteYehova atalilamula? Walituma kuti likawononge Asikeloni ndi mʼmphepete mwa nyanja.+Iye walituma kuti lipite kumeneko.”

Mawu a M'munsi

Kutanthauza, “Kerete.”