Yeremiya 42:1-22

  • Anthu anapempha Yeremiya kuti afunsire malangizo kwa Mulungu (1-6)

  • Yehova anawauza kuti: “Musapite ku Iguputo” (7-22)

42  Kenako akuluakulu onse a asilikali, Yohanani+ mwana wa Kareya, Yezaniya mwana wa Hoshaya ndi anthu onse kuyambira anthu wamba mpaka anthu olemekezeka, anapita  kwa mneneri Yeremiya nʼkumuuza kuti: “Chonde, tikomere mtima ndipo utipempherere kwa Yehova Mulungu wako. Pempherera anthu onse amene atsalawa chifukwa poyamba tinalipo ambiri koma pano tatsala ochepa+ ngati mmene ukuoneramu.  Yehova Mulungu wako atiuze njira yoti tiyendemo ndi zoti tichite.”  Mneneri Yeremiya anawayankha kuti: “Ndamva zimene mwanenazo. Ndipemphera kwa Yehova Mulungu wanu malinga ndi zimene mwapempha. Ndipo mawu aliwonse amene Yehova angakuyankheni ndidzakuuzani. Sindidzakubisirani chilichonse.”  Iwo anayankha Yeremiya kuti: “Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika, ndipo atilange ngati sitidzachita ndendende mogwirizana ndi malangizo amene Yehova Mulungu wako angatipatse kudzera mwa iwe.  Ife tikukutuma kwa Yehova Mulungu wathu, kaya mawu ake ndi otikomera kapena otiipira, tidzamverabe mawuwo. Tidzachita zimenezi kuti zinthu zitiyendere bwino chifukwa chomvera mawu a Yehova Mulungu wathu.”  Ndiye patadutsa masiku 10, Yehova analankhula ndi Yeremiya.  Choncho Yeremiya anaitana Yohanani mwana wa Kareya, pamodzi ndi akuluakulu onse a asilikali amene anali naye. Anaitananso anthu onse, anthu wamba ndi anthu olemekezeka omwe.+  Iye anawauza kuti: “Inu munandituma kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli kukamupempha kuti akukomereni mtima. Ndiye zimene iye wanena ndi izi: 10  ‘Ngati mungakhalebe mʼdziko lino, ndidzakumangani osati kukugwetsani, ndidzakudzalani osati kukuzulani, popeza ndidzakumverani chisoni chifukwa cha tsoka limene ndakugwetserani.+ 11  Musachite mantha ndi mfumu ya Babulo imene mukuiopayo.’+ ‘Mfumu imeneyi musachite nayo mantha, chifukwa ine ndili ndi inu kuti ndikupulumutseni ndi kukulanditsani mʼmanja mwake,’ akutero Yehova. 12  ‘Ndidzakuchitirani chifundo+ moti mfumuyo idzakumverani chifundo nʼkukubwezerani kudziko lanu. 13  Koma inu mukanena kuti: “Ayi! Ife sitikhala mʼdziko lino,” ndipo mukapanda kumvera mawu a Yehova Mulungu wanu 14  ponena kuti, “Ayi, mʼmalomwake tipita kudziko la Iguputo,+ kumene sitidzaona nkhondo kapena kumva kulira kwa lipenga komanso kumene sitidzasowa chakudya. Ife tizikakhala kumeneko,” 15  imvani mawu a Yehova, inu otsala a Yuda. Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ngati mwatsimikiza mtima kuti mupite ku Iguputo ndipo mukapitadi nʼkukakhala* kumeneko, 16  ndiye kuti lupanga limene mukuliopa lidzakupezani ku Iguputo komweko ndipo njala imene mukuiopa idzakutsatirani ku Iguputoko moti mudzafera komweko.+ 17  Ndipo amuna onse amene atsimikiza mtima kupita ku Iguputo kuti akakhale kumeneko adzafa ndi lupanga, njala ndi mliri.* Palibe amene adzapulumuke kapena kuthawa tsoka limene ndidzawagwetsere.”’ 18  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: ‘Mofanana ndi mmene ndinasonyezera anthu okhala mu Yerusalemu+ mkwiyo ndi ukali wanga, inunso ndidzakusonyezani mkwiyo wanga ngati mutapita ku Iguputo. Mudzakhala otembereredwa, chinthu chochititsa mantha, chinthu chonyozeka+ ndi chochititsa manyazi ndipo malo ano simudzawaonanso.’ 19  Yehova wakuuzani inu otsala a Yuda, kuti musapite ku Iguputo. Dziwani ndithu kuti ine ndakuchenjezani lero 20  kuti zolakwa zanu zidzakuphetsani. Zili choncho chifukwa inu munandituma kwa Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Tipempherere kwa Yehova Mulungu wathu ndipo udzatiuze zilizonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanene ndipo ife tidzachita zomwezo.’+ 21  Ndipo ine ndakuuzani lero, koma inu simumvera mawu a Yehova Mulungu wanu kapena kuchita chilichonse chimene wandituma kuti ndidzakuuzeni.+ 22  Choncho dziwani ndithu kuti mudzafa ndi lupanga, njala ndi mliri mʼdziko limene mukulakalaka kupita kuti muzikakhalako.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “nʼkukakhala kwa kanthawi.”
Kapena kuti, “matenda.”