Yeremiya 52:1-34

  • Zedekiya anagalukira mfumu ya Babulo (1-3)

  • Nebukadinezara anazungulira Yerusalemu (4-11)

  • Kuwonongedwa kwa mzinda komanso kachisi (12-23)

  • Anthu anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo (24-30)

  • Yehoyakini anatulutsidwa mʼndende (31-34)

52  Zedekiya+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 21 ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Libina ndipo dzina lawo linali Hamutali+ mwana wa Yeremiya.  Zedekiya anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene Yehoyakimu anachita.+  Zinthu zimenezi zinachitika ku Yerusalemu ndi ku Yuda chifukwa Yehova anakwiya kwambiri mpaka anawachotsa pamaso pake.+ Kenako Zedekiya anagalukira mfumu ya Babulo.+  Mʼchaka cha 9 cha ufumu wa Zedekiya, mʼmwezi wa 10, pa tsiku la 10 la mweziwo, Nebukadinezara* mfumu ya Babulo anabwera ku Yerusalemu pamodzi ndi asilikali ake onse. Anabwera kudzamenyana ndi anthu amumzindawo ndipo anamanga msasa komanso mpanda kuzungulira mzinda wonsewo.+  Mzindawo unazunguliridwa mpaka chaka cha 11 cha Mfumu Zedekiya.  Mʼmwezi wa 4, pa tsiku la 9,+ njala inafika poipa kwambiri mumzindawo ndipo anthu analibiretu chakudya.+  Pamapeto pake, mpanda wa mzindawo unabooledwa ndipo asilikali onse anathawa mumzindawo usiku kudzera pageti limene linali pakati pa makoma awiri, pafupi ndi munda wa mfumu. Akasidi anali atazungulira mzindawo ndipo iwo anapitiriza kuthawa kulowera cha ku Araba.+  Koma asilikali a Akasidi anayamba kuthamangitsa Zedekiya+ ndipo anamupeza mʼchipululu cha Yeriko. Zitatero asilikali onse a mfumuyo anabalalika nʼkuisiya yokha.  Kenako Akasidiwo anagwira mfumuyo nʼkupita nayo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo mʼdziko la Hamati ndipo anaipatsa chigamulo. 10  Ndipo mfumu ya Babulo inapha ana aamuna a Zedekiya, iye akuona. Inaphanso akalonga onse a ku Yuda ku Ribila komweko. 11  Kenako mfumu ya Babulo inachititsa khungu Zedekiya,+ inamumanga ndi maunyolo akopa* nʼkupita naye ku Babulo ndipo inamuika mʼndende mpaka tsiku la imfa yake. 12  Mʼmwezi wa 5, pa tsiku la 10 la mweziwo, chomwe chinali chaka cha 19 cha Mfumu Nebukadinezara* ya ku Babulo, Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu, amene anali mtumiki wa mfumu ya Babulo, anabwera ku Yerusalemu.+ 13  Iye anatentha nyumba ya Yehova,+ nyumba ya mfumu, nyumba iliyonse yaikulu komanso nyumba zonse za mu Yerusalemu. 14  Kenako asilikali onse a Akasidi, omwe anali ndi mkulu wa asilikali olondera mfumu uja, anagwetsa mpanda wonse wa Yerusalemu.+ 15  Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anatenga ena mwa anthu onyozeka ndiponso anthu ena onse amene anatsala mumzindawo. Anatenganso anthu amene anathawira kwa mfumu ya Babulo komanso amisiri onse aluso nʼkupita nawo ku ukapolo.+ 16  Ena mwa anthu osauka kwambiri amʼdzikolo, Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anawasiya kuti akhale olima minda ya mpesa ndi anthu ogwira ntchito mokakamizidwa.+ 17  Akasidi anaphwanyaphwanya zipilala zakopa+ zapanyumba ya Yehova, zotengera zokhala ndi mawilo+ ndiponso thanki yakopa yosungira madzi+ zimene zinali mʼnyumba ya Yehova nʼkutenga kopa yense kupita naye ku Babulo.+ 18  Akasidiwo anatenganso ndowa, mafosholo, zozimitsira nyale, mbale zolowa,+ makapu+ ndi ziwiya zonse zakopa zimene ansembe ankagwiritsa ntchito potumikira mʼkachisi. 19  Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenga mabeseni,+ zopalira moto, mbale zolowa, ndowa zochotsera phulusa, zoikapo nyale,+ makapu ndi mbale zinanso zolowa zomwe zinali zagolide komanso zasiliva weniweni.+ 20  Koma zinali zosatheka kuyeza kulemera kwa kopa wa zipilala ziwiri zija, thanki yosungira madzi, ngʼombe zakopa 12+ zimene zinali pansi pa thanki yosungira madzi ndiponso zotengera zokhala ndi mawilo zimene Mfumu Solomo anapanga kuti zizigwira ntchito panyumba ya Yehova chifukwa anali wochuluka kwambiri. 21  Ponena za zipilalazo, chipilala chilichonse chinali chachitali mamita 8* ndipo chinkatha kuzunguliridwa ndi chingwe chachitali mamita 5.*+ Chipilala chilichonse chinali ndi mphako mkati ndipo kuchindikala kwake kunali masentimita 7.* 22  Mutu wa chipilala chilichonse unali wakopa. Mutuwo unali wautali mamita awiri*+ ndipo maukonde ndi makangaza* amene anazungulira mutuwo, onse anali akopa. Chipilala chachiwiri chinali chofanana ndi choyambacho, chimodzimodzinso makangaza ake. 23  Makangaza amene anali mʼmbali mwa zipilalazo analipo 96 ndipo makangaza onse amene anazungulira maukondewo analipo 100.+ 24  Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenganso Seraya+ wansembe wamkulu, Zefaniya+ wansembe wachiwiri ndi alonda atatu apakhomo.+ 25  Mumzindawo anatengamonso nduna imodzi yapanyumba ya mfumu imene inkayangʼanira asilikali. Anatenganso anzake 7 a mfumu amene anawapeza mumzindawo. Komanso anatenga mlembi wa mkulu wa asilikali yemwe ankasonkhanitsa anthu ndiponso amuna 60 mwa anthu wamba amene anawapeza mumzindawo. 26  Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anatenga anthuwa nʼkupita nawo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo. 27  Mfumu ya Babuloyo inapha anthuwo ku Ribila+ mʼdziko la Hamati. Choncho Ayuda anatengedwa kudziko lawo nʼkupita nawo ku ukapolo.+ 28  Chiwerengero cha anthu amene Nebukadinezara* anawatenga kupita nawo ku ukapolo ndi ichi: mʼchaka cha 7 cha ulamuliro wake, anatenga Ayuda 3,023.+ 29  Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Nebukadinezara,*+ anthu 832 anatengedwa kuchokera ku Yerusalemu. 30  Mʼchaka cha 23 cha ulamuliro wa Nebukadinezara,* Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anatenga Ayuda 745 kupita nawo ku ukapolo.+ Anthu onse amene anatengedwa kupita ku ukapolo anali 4,600. 31  Kenako mʼchaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakini+ mfumu ya Yuda, Evili-merodaki anakhala mfumu ya Babulo. Ndiyeno mʼchaka chomwecho mʼmwezi wa 12, pa tsiku la 25 la mweziwo, iye anamasula* Yehoyakini mfumu ya Yuda nʼkumutulutsa mʼndende.+ 32  Ankalankhula naye mokoma mtima ndipo anakweza mpando wake wachifumu kuposa mipando ya mafumu ena amene anali naye ku Babulo. 33  Choncho Yehoyakini anavula zovala zake zakundende ndipo ankadya limodzi ndi mfumuyo masiku onse a moyo wake. 34  Tsiku lililonse ankapatsidwa chakudya kuchokera kwa mfumu ya Babulo, kwa moyo wake wonse mpaka tsiku limene anafa.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “amkuwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 18.” Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 12.” Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mphipi ya zala 4.” Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 5.” Onani Zakumapeto B14.
“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anatukula mutu wa.”