Yeremiya 39:1-18

  • Kuwonongedwa kwa Yerusalemu (1-10)

    • Zedekiya anathawa koma anamugwira (4-7)

  • Yeremiya ankayenera kulonderedwa (11-14)

  • Ebedi-meleki anapulumutsidwa (15-18)

39  Mʼchaka cha 9 cha ulamuliro wa Mfumu Zedekiya ya Yuda, mʼmwezi wa 10, Mfumu Nebukadinezara* ya Babulo ndi asilikali ake onse anafika ku Yerusalemu nʼkuzungulira mzindawo.+  Mʼchaka cha 11 cha ulamuliro wa Zedekiya, mʼmwezi wa 4, pa tsiku la 9, anaboola mpanda wa mzindawo.+  Ndiyeno akalonga onse a mfumu ya Babulo analowa mumzindawo nʼkukhala pansi pa Geti la Pakati.+ Mayina awo anali Nerigali-sarezera amene anali Samugari, Nebo-sarisekimu amene anali Rabisarisi,* Nerigali-sarezera amene anali Rabimagi* ndi akalonga ena onse a mfumu ya Babulo.  Mfumu Zedekiya ya Yuda ndi asilikali onse ataona adaniwo, anathawira+ kunja kwa mzinda usiku. Iwo anadzera njira yakumunda wa mfumu nʼkukadutsa pageti limene linali pakati pa makoma awiri ndipo anapitiriza kuthawa kulowera ku Araba.+  Koma asilikali a Akasidi anawathamangitsa ndipo Zedekiya anamupeza mʼchipululu cha Yeriko.+ Anamugwira nʼkupita naye kwa Mfumu Nebukadinezara* ya Babulo ku Ribila,+ mʼdziko la Hamati,+ kumene Nebukadinezara anamuweruza.  Zitatero mfumu ya Babulo inapha ana aamuna a Zedekiya ku Ribila, Zedekiyayo akuona. Inaphanso anthu onse olemekezeka a ku Yuda.+  Mfumu ya Babulo inachititsa khungu maso a Zedekiya ndipo kenako inamumanga mʼmaunyolo akopa* kuti apite naye ku Babulo.+  Kenako Akasidi anawotcha nyumba ya mfumu ndi nyumba za anthu+ ndipo anagwetsa mpanda wa Yerusalemu.+  Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu, anatenga anthu ena onse otsala mumzindamo, anthu amene anathawira kwa mfumu ya Babulo ndi anthu ena onse amene anapulumuka nʼkupita nawo ku ukapolo ku Babulo. 10  Koma Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu, anasiya mʼdziko la Yuda ena mwa anthu amene anali osauka kwambiri omwe analibe kalikonse. Pa tsiku limenelo anawapatsanso minda ndi minda ya mpesa kuti azilima.*+ 11  Mfumu Nebukadinezara* ya Babulo inapereka lamulo kwa Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu lokhudza Yeremiya kuti: 12  “Mutenge uzimuyangʼanira ndipo usamuchitire choipa chilichonse. Koma uzimupatsa chilichonse chimene iye wapempha.”+ 13  Choncho Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu ndi Nebusazibani amene anali Rabisarisi,* Nerigali-sarezera amene anali Rabimagi* ndi akuluakulu onse a mfumu ya Babulo anatuma anthu. 14  Iwo anatuma anthuwo kuti akatenge Yeremiya mʼBwalo la Alonda+ nʼkumupereka kwa Gedaliya+ mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani,+ kuti apite naye kunyumba kwake. Choncho Yeremiya anayamba kukhala ndi anthu. 15  Pa nthawi imene Yeremiya anatsekeredwa mʼBwalo la Alonda,+ Yehova analankhula naye kuti: 16  “Pita kwa Ebedi-meleki+ wa ku Itiyopiya ndipo ukamuuze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Taona! Ndikukwaniritsa mawu anga akuti mzinda uwu ndidzaugwetsera tsoka osati zinthu zabwino ndipo pa tsikulo iweyo udzaona zimenezi zikuchitika.”’ 17  ‘Koma pa tsikulo iweyo ndidzakupulumutsa ndipo sudzaperekedwa mʼmanja mwa anthu amene ukuwaopa,’ akutero Yehova. 18  ‘Chifukwa ine ndidzakupulumutsa ndithu ndipo sudzaphedwa ndi lupanga. Udzapulumuka+ chifukwa chakuti wandikhulupirira,’+ akutero Yehova.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “Nerigali-sarezera, Samugari-nebo, Sarisekimu, Rabisarisi,” potengera kagawidwe kena ka mawu a Chiheberi.
Kapena kuti, “mkulu wa azamatsenga (wolosera zamʼtsogolo).”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “amkuwa.”
Mabaibulo ena amati, “azigwiramo ntchito yokakamiza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “nduna yaikulu.”
Kapena kuti, “mkulu wa azamatsenga (wolosera zamʼtsogolo).”