Yeremiya 45:1-5

  • Uthenga wa Yehova wopita kwa Baruki (1-5)

45  Awa ndi mawu amene mneneri Yeremiya anauza Baruki+ mwana wa Neriya pa nthawi imene Baruki ankalemba mʼbuku mawu amene Yeremiya+ ankamuuza, mʼchaka cha 4 cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda. Yeremiya anati:  “Ponena za iwe Baruki, Yehova, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti,  ‘Iwe wanena kuti: “Mayo ine! Yehova wawonjezera chisoni pa zopweteka zanga. Ndatopa ndi kubuula ndipo malo ampumulo sindikuwapeza.”’  Umuuze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Taona! Zimene ndamanga ndikuzigwetsa ndipo zimene ndadzala ndikuzizula. Ndichita zimenezi mʼdziko lonse.+  Koma iwe ukufunafuna* zinthu zazikulu. Leka kufunafuna zinthu zimenezo.”’ ‘Chifukwa ndatsala pangʼono kubweretsa tsoka pa anthu onse+ ndipo iwe ndidzakupatsa moyo wako* kuti ukhale mphoto yako kulikonse kumene ungapite,’+ akutero Yehova.”

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “iwe ukuyembekezera.”
Kapena kuti, “iwe ndidzakulola kuti upulumutse moyo wako.”