Yeremiya 14:1-22
14 Mawu amene Yehova anauza Yeremiya pa nkhani ya chilala ndi awa:+
2 Yuda akulira maliro+ ndipo mageti ake agwa.
Agwa pansi nʼkumalira momvetsa chisoni,Ndipo anthu a ku Yerusalemu akulira.
3 Anthu awo olemekezeka amatuma antchito awo kuti akatunge madzi.
Antchitowo amapita kuzitsime koma sapezako madzi.
Amabwerako ndi ziwiya zopanda kanthu.
Iwo achita manyazi ndipo akhumudwa,Moti aphimba mitu yawo.
4 Alimi ataya mtima ndipo aphimba mitu yawoChifukwa chakuti mʼdzikomo simunagwe mvula+Ndipo nthaka yangʼambikangʼambika.
5 Ngakhale mbawala yaikazi yasiya mwana wake wobadwa kumene mʼthengoChifukwa kulibe msipu.
6 Abulu amʼtchire angoima mʼmapiri opanda kanthu.
Akupuma mwawefuwefu ngati mimbulu.Maso awo achita mdima chifukwa kulibe msipu.+
7 Ngakhale kuti machimo athu akuchitira umboni kuti ndife olakwa,Inu Yehova, chitanipo kanthu chifukwa cha dzina lanu.+
Chifukwa zochita zathu zosonyeza kusakhulupirika nʼzambiri,+Ndipo takuchimwirani.
8 Inu chiyembekezo cha Isiraeli, Mpulumutsi wake+ pa nthawi yamavuto,Nʼchifukwa chiyani mukukhala ngati mlendo mʼdzikoli?Nʼchifukwa chiyani mukukhala ngati munthu wapaulendo amene waima kuti agone usiku umodzi wokha?
9 Nʼchifukwa chiyani mukukhala ngati munthu wothedwa nzeru,Ndiponso ngati munthu wamphamvu amene sangathe kupulumutsa anthu ake?
Komatu inu Yehova muli pakati pathu,+Ndipo ife timadziwika ndi dzina lanu.+
Musatisiye.
10 Ponena za anthu awa Yehova wanena kuti: “Iwo amakonda kumangoyendayenda+ ndipo samatha kudziletsa kuti asamayendeyende.+ Choncho Yehova sakusangalala nawo.+ Tsopano iye akumbukira zolakwa zawo ndipo awalanga chifukwa cha machimo awo.”+
11 Kenako Yehova anandiuza kuti: “Usapempherere anthu awa kuti zinthu ziwayendere bwino.+
12 Akamasala kudya, ine sindimvetsera kuchonderera kwawo.+ Akamapereka nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zambewu, ine sindisangalala nazo+ ndipo ndiwawononga ndi lupanga, njala yaikulu ndiponso mliri.”*+
13 Nditamva zimenezi ndinanena kuti: “Mayo ine! Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Aneneri akuuza anthuwo kuti, ‘Simudzawonongedwa ndi lupanga ndipo njala yaikulu sidzakugwerani, koma Mulungu adzakupatsani mtendere weniweni mʼmalo ano.’”+
14 Ndiyeno Yehova anandiyankha kuti: “Aneneriwo akulosera zinthu zabodza mʼdzina langa.+ Ine sindinawatume, kuwalamula kapena kulankhula nawo.+ Maulosi amene akukuuzaniwo ndi masomphenya abodza, maulosi opanda pake ndi chinyengo chamumtima mwawo.+
15 Choncho Yehova wanena kuti: ‘Ponena za aneneri amene akulosera mʼdzina langa ngakhale kuti sindinawatume, amenenso akunena kuti lupanga kapena njala sizidzafika mʼdziko lino, ine ndikuti aneneri amenewo adzaphedwa ndi lupanga ndiponso njala yaikulu.+
16 Anthu amene akuwauza maulosi awowo, adzafa ndi njala komanso lupanga ndipo mitembo yawo idzatayidwa mʼmisewu ya Yerusalemu. Sipadzakhala wowaika mʼmanda,+ iwowo, akazi awo, ana awo aamuna kapena ana awo aakazi chifukwa ndidzawatsanulira tsoka limene akuyenera kulandira.’+
17 Anthu awa uwauze kuti,‘Maso anga atulutse misozi usiku ndi masana ndipo asasiye,+Chifukwa mwana wamkazi wa anthu anga, yemwe ndi namwali, waphwanyidwa kotheratu+Ndipo ali ndi bala lalikulu kwambiri.
18 Ndikapita kunja kwa mzinda,Ndikuona anthu ophedwa ndi lupanga.+
Ndipo ndikalowa mumzinda,+Ndikuona matenda obwera chifukwa cha njala.
Aneneri komanso ansembe, onse apita kudziko lachilendo limene sakulidziwa.’”+
19 Kodi Yuda mwamukaniratu, kapena kodi mukunyansidwa ndi Ziyoni?+
Nʼchifukwa chiyani mwatilanga chonchi moti sitingathenso kuchira?+
Timayembekezera mtendere, koma palibe chabwino chilichonse chimene chachitika.Timayembekezera kuchiritsidwa, koma tikungoona zinthu zochititsa mantha.+
20 Inu Yehova, ife tikuvomereza zinthu zoipa zimene tachitaKomanso kulakwa kwa makolo athu,Chifukwa takuchimwirani.+
21 Koma chifukwa cha dzina lanu, musatikane.+Musachititse manyazi mpando wanu wachifumu waulemerero.
Kumbukirani pangano limene munachita ndi ife ndipo musaliphwanye.+
22 Kodi pa mafano opanda pake a mitundu ya anthu pali fano lililonse limene lingagwetse mvula?Kapena kodi kumwamba pakokha kungagwetse mvula yamvumbi?
Kodi si inu nokha, Yehova Mulungu wathu, amene mumachititsa zimenezi?+
Chiyembekezo chathu chili mwa inuChifukwa inu nokha ndi amene mumachita zonsezi.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “matenda.”