Yesaya 66:1-24

  • Kulambira koona komanso kwabodza (1-6)

  • Ziyoni ndi ana ake amuna (7-17)

  • Anthu adzasonkhana mu Yerusalemu kuti alambire (18-24)

66  Yehova wanena kuti: “Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu ndipo dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga.+ Ndiye kodi mungandimangire nyumba yotani,+Ndipo malo oti ine ndingapumulirepo ali kuti?”+   “Dzanja langa ndi limene linapanga zinthu zonsezi,Ndipo izi ndi zimene zinachitika kuti zonsezi zikhalepo,” akutero Yehova.+ “Choncho ine ndidzayangʼana munthu ameneyu,Ndidzayangʼana munthu wodzichepetsa ndiponso wosweka mtima amene amadera nkhawa mawu anga.+   Munthu amene akupha ngʼombe yamphongo ali ngati amene akupha munthu.+ Amene akupereka nsembe ya nkhosa ali ngati amene akuthyola khosi la galu.+ Munthu amene akupereka mphatso ali ngati amene akupereka magazi a nkhumba.+ Amene akupereka nsembe yachikumbutso ya lubani+ ali ngati munthu amene akupereka dalitso pogwiritsa ntchito mawu onenerera zamatsenga.*+ Anthuwo asankha njira zawozawo,Ndipo amasangalala ndi zinthu zonyansa.   Choncho ndidzasankha njira zowalangira,+Ndipo ndidzawabweretsera zinthu zimene amachita nazo mantha. Chifukwa nditaitana, palibe amene anayankha.Nditalankhula, palibe amene anamvetsera.+ Iwo anapitiriza kuchita zinthu zoipa pamaso pangaNdipo anasankha kuchita zinthu zimene sizinandisangalatse.”+   Imvani mawu a Yehova, inu amene mumadera nkhawa mawu ake: “Abale anu amene akudana nanu ndipo amakusalani chifukwa cha dzina langa anati, ‘Alemekezeke Yehova!’+ Koma Mulungu adzaonekera nʼkukuchititsani kuti musangalale,Ndipo iwowo ndi amene adzachititsidwe manyazi.”+   Mumzinda mukumveka phokoso lachipwirikiti, phokoso lochokera kukachisi. Limeneli ndi phokoso losonyeza kuti Yehova akubwezera adani ake chilango chowayenerera.   Mkazi anabereka asanayambe kumva zowawa za pobereka.+ Asanayambe kumva ululu wa pobereka, iye anabereka mwana wamwamuna.   Ndi ndani anamvapo zinthu ngati zimenezi? Ndi ndani anaonapo zinthu zoterezi? Kodi dziko lingabadwe tsiku limodzi? Kapena kodi mtundu wa anthu ungabadwe nthawi imodzi? Koma Ziyoni atangoyamba kumva zowawa za pobereka, anabereka ana aamuna.   “Kodi ine ndingachititse kuti mwana atsale pangʼono kubadwa koma nʼkumulepheretsa kuti abadwe?” akutero Yehova. “Kapena kodi ndingachititse kuti mwana ayambe kubadwa kenako nʼkutseka chiberekero?” akutero Mulungu wanu. 10  Sangalalani ndi Yerusalemu ndipo kondwerani naye,+ inu nonse amene mumamukonda.+ Sangalalani naye kwambiri, inu nonse amene mukumulirira, 11  Chifukwa mudzayamwa bere lake lotonthoza ndipo mudzakhuta kwambiri,Komanso mudzamwa mkaka wake mokwanira ndipo mudzasangalala kwambiri ndi ulemerero wake. 12  Chifukwa Yehova wanena kuti: “Ndikumupatsa mtendere ngati mtsinje+Komanso ulemerero wa mitundu ya anthu ngati mtsinje wosefukira.+ Inu mudzayamwa komanso adzakunyamulani mʼmanja,Ndipo adzakudumphitsani pamiyendo. 13  Mofanana ndi mayi amene amatonthoza mwana wake,Inenso ndidzapitiriza kukutonthozani.+Ndipo mudzatonthozedwa chifukwa cha Yerusalemu.+ 14  Mudzaona zimenezi ndipo mtima wanu udzasangalala.Mafupa anu adzakhala ndi mphamvu ngati udzu wobiriwira. Ndipo dzanja la* Yehova lidzadziwika kwa atumiki ake,Koma iye adzakwiyira adani ake.”+ 15  “Chifukwa Yehova adzabwera ngati moto,+Ndipo magaleta ake ali ngati mphepo yamkuntho,+Kuti adzawabwezere atakwiya kwambiri,Ndiponso kuti adzawadzudzule ndi malawi a moto.+ 16  Yehova adzapereka chiweruzo pogwiritsa ntchito moto,Inde adzagwiritsa ntchito lupanga lake poweruza anthu onse,Ndipo anthu ophedwa ndi Yehova adzakhala ambiri. 17  Anthu amene akudzipatula nʼkudziyeretsa potsatira fano limene lili pakati pa mundawo,*+ amene akudya nyama ya nkhumba,+ zinthu zonyansa komanso mbewa,+ onsewo adzathera limodzi,” akutero Yehova. 18  “Popeza ndikudziwa ntchito zawo ndi maganizo awo, ine ndikubwera kudzasonkhanitsa pamodzi anthu a mitundu yonse ndi zilankhulo zonse ndipo iwo adzabwera nʼkuona ulemerero wanga. 19  Ndidzaika chizindikiro pakati pawo ndipo ena mwa anthu amene adzapulumuke ndidzawatumiza ku mitundu ya anthu. Ndidzawatumiza kwa anthu aluso lokoka uta omwe ndi a ku Tarisi,+ ku Puli ndi ku Ludi.+ Ndidzawatumizanso kwa anthu a ku Tubala ndi ku Yavani+ komanso akuzilumba zakutali amene sanamvepo zokhudza ine kapena kuona ulemerero wanga. Iwo adzalengeza za ulemerero wanga pakati pa mitundu ya anthu.+ 20  Adzabweretsa abale anu onse kuchokera ku mitundu yonse+ ngati mphatso kwa Yehova. Adzawabweretsa atakwera mahatchi, ngolo, ngolo zotseka pamwamba, nyulu* ndi ngamila zothamanga, mpaka kukafika kuphiri langa loyera, ku Yerusalemu. Adzachita zimenezi ngati mmene Aisiraeli amabweretsera mphatso mʼnyumba ya Yehova, ataiika mʼchiwiya choyera,” akutero Yehova. 21  “Ndidzatenganso anthu ena kuti akhale ansembe ndi Alevi,” akutero Yehova. 22  “Chifukwa kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano+ zimene ndikupanga zidzapitiriza kukhala pamaso panga. Mofanana ndi zimenezi, ana anu* ndi dzina lanu zidzapitiriza kukhalapo,”+ akutero Yehova. 23  “Kuyambira tsiku limene mwezi watsopano waoneka mpaka tsiku limene mwezi wina watsopano udzaoneke ndiponso sabata lililonse,Anthu onse adzabwera kudzagwada* pamaso panga,”+ akutero Yehova. 24  “Iwo adzapita kukaona mitembo ya anthu amene anandipandukira.Chifukwa mphutsi zodya mitemboyo sizidzafa.Komanso moto umene ukuiwotcha sudzazimitsidwa,+Ndipo idzakhala chinthu chonyansa kwa anthu onse.”

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “amene amapembedza fano.”
Kapena kuti, “mphamvu za.”
Umenewu ndi munda wapadera umene ankaugwiritsa ntchito polambira mafano.
“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zanu.”
Kapena kuti, “kudzalambira.”