Rute 3:1-18

  • Naomi anapereka malangizo kwa Rute (1-4)

  • Rute ndi Boazi kopunthira mbewu (5-15)

  • Rute anabwerera kwa Naomi (16-18)

3  Tsopano Naomi, apongozi ake a Rute, anamuuza kuti: “Mwana wanga, kodi sindiyenera kukupezera nyumba,*+ kuti zikuyendere bwino? 2  Pajatu Boazi ndi wachibale wathu.+ Ndipo atsikana ake antchito wakhala ukugwira nawo ntchito. Usiku walero iye akhala akupeta balere pamalo ake opunthira. 3  Choncho samba nʼkudzola mafuta komanso utchene ndipo upite kumalo opunthirawo. Koma ukaonetsetse kuti iye asakadziwe kuti wafika mpaka atamaliza kudya ndi kumwa. 4  Ndiyeno akamakagona, ukaone kuti wagona pati. Kenako ukapite pamene wagonapo ndipo ukamuvundukule mapazi nʼkugona pomwepo. Iye akakuuza zochita.” 5  Rute anayankha kuti: “Ndikachita zonse zimene mwanena.” 6  Choncho anapita kopunthirako nʼkuchita zonse zimene apongozi ake anamuuza. 7  Boazi anadya ndi kumwa ndipo anali wosangalala kwambiri. Kenako anapita kukagona kumapeto kwa mulu wa balere. Ndiyeno Rute anayenda mwakachetechete ndipo anavundukula mapazi a Boazi nʼkugona. 8  Pakati pa usiku Boazi anayamba kunjenjemera ndipo anadzuka nʼkukhala tsonga. Koma anadabwa kuona kuti mkazi wagona kumapazi ake. 9  Choncho anafunsa kuti: “Ndiwe ndani?” Rute anayankha kuti: “Ndine Rute kapolo wanu. Ndifunditseni chovala chanu ine kapolo wanu, chifukwa ndinu wotiwombola.”+ 10  Atatero, Boazi anati: “Yehova akudalitse mwana wanga. Chikondi chokhulupirika chimene wasonyeza panopa chikuposa choyamba chija,+ chifukwa sunafune anyamata, kaya osauka kapena olemera. 11  Ndiye tamvera mwana wanga, usachite mantha. Ndikuchitira zonse zimene wanena,+ chifukwa aliyense mumzindawu akudziwa kuti ndiwe mkazi wabwino kwambiri. 12  Ngakhale kuti ndinedi wokuwombolani,+ koma pali wachibale wina wapafupi kwambiri kuposa ine amene angakuwombole.+ 13  Gona pompano lero. Ngati iye angakuwombole mawa, zili bwino akuwombole.+ Koma ngati sakufuna kukuwombola, ineyo ndikuwombola. Ndithudi, pali Yehova Mulungu wamoyo, ndikuwombola. Gona mpaka mʼmawa.” 14  Choncho anagonabe kumapazi a Boazi mpaka mʼmamawa. Kenako anadzuka kudakali mdima chifukwa Boazi sanafune kuti anthu adziwe kuti kopunthira mbewuko kunabwera mkazi. 15  Ndiyeno anamuuza kuti: “Bweretsa nsalu wafundayo ndipo uitambasule.” Iye anaitambasuladi ndipo Boazi anathirapo miyezo 6* ya balere nʼkumusenza pamutu. Kenako Boazi analowa mumzinda. 16  Tsopano Rute anabwerera kwa apongozi ake, ndipo iwo anamufunsa kuti: “Wayendako bwanji* mwana wanga?” Iye anawafotokozera zonse zimene Boazi anamuchitira. 17  Anafotokozanso kuti: “Wandipatsa balere uyu wokwana miyezo 6 nʼkundiuza kuti, ‘Usapite kwa apongozi ako chimanjamanja.’” 18  Atatero, Naomi anayankha kuti: “Tiye tingodikira mwana wanga, mpaka utadziwa mmene nkhaniyi ithere. Chifukwa iye sakhala pansi mpaka ataithetsa nkhaniyi lero.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mpumulo.”
Nʼkutheka kuti inali miyezo 6 ya seya kapena malita pafupifupi 44. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndiwe ndani?”