Kalata Yopita kwa Aheberi 4:1-16

  • Kuopsa kosalowa mumpumulo wa Mulungu (1-10)

  • Anawalimbikitsa kuti alowe mumpumulo wa Mulungu (11-13)

    • Mawu a Mulungu ndi amoyo (12)

  • Yesu, mkulu wa ansembe wapamwamba (14-16)

4  Choncho, popeza lonjezo lolowa mumpumulo wake lidakalipo, samalani kuopera kuti wina wa inu angalephere kukwaniritsa zofunika kuti akalowe mu mpumulowo.+  Uthenga wabwino unalengezedwa kwa ife,+ ngati mmenenso anaulengezera kwa makolo athu. Koma mawu amene iwo anamva sanapindule nawo, chifukwa analibe chikhulupiriro chofanana ndi cha amene anamvera mawuwo.  Ife amene tasonyeza chikhulupiriro tikulowadi mumpumulowo. Ponena za mpumulo umenewu iye anati: “Choncho ndinalumbira nditakwiya kuti, ‘Sadzalowa mumpumulo wanga,’”+ ngakhale kuti anali atamaliza ntchito zake pa nthawi imene dziko linkakhazikitsidwa.*+  Ponena za tsiku la 7, penapake anati: “Ndipo Mulungu anapuma pa ntchito zake zonse pa tsiku la 7.”+  Panonso akunena kuti: “Sadzalowa mumpumulo wanga.”+  Choncho, popeza mwayi wolowa mumpumulowo udakalipo, ndipo amene anali oyamba kumva uthenga wabwino sanalowemo chifukwa cha kusamvera,+  patapita nthawi, Mulungu ananena mu salimo la Davide, ngati mmene tanenera kale mu kalatayi kuti: “Lero anthu inu mukamva mawu a Mulungu, musaumitse mitima yanu.”+ Choncho wapatula tsiku limene akulitchula kuti “Lero.”  Chifukwa Yoswa+ akanawalowetsa mʼmalo ampumulo, Mulungu sakananenanso pambuyo pake za tsiku lina.  Choncho mpumulo wa sabata udakalipo kwa anthu a Mulungu.+ 10  Munthu amene walowa mumpumulo wa Mulungu, ndiye kuti wapumanso pa ntchito zake, ngati mmene Mulungu anapumira pa ntchito zake.+ 11  Choncho, tiyeni tichite zonse zimene tingathe kuti tilowe mumpumulo umenewo, nʼcholinga choti wina asakhale wosamvera ngati makolo athuwo.+ 12  Chifukwa mawu a Mulungu ndi amoyo komanso amphamvu,+ ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse.+ Amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo ndi mzimu komanso mafupa* ndi mafuta amʼmafupa. Mawu a Mulungu amathanso kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake. 13  Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino moti ifeyo tidzayankha kwa Mulunguyo pa zochita zathu.+ 14  Choncho, popeza tili ndi mkulu wa ansembe wapamwamba, Yesu Mwana wa Mulungu,+ amene anapita kumwamba, tiyeni tipitirize kulengeza zoti timamukhulupirira.+ 15  Chifukwa mkulu wa ansembe amene tili nayeyu, si mkulu wa ansembe amene sangatimvere chisoni pa zofooka zathu.+ Koma ndi mkulu wa ansembe amene anayesedwa pa zinthu zonse ngati ifeyo, ndipo anakhalabe wopanda uchimo.+ 16  Choncho, tiyeni tizifika kumpando wachifumu wa Mulungu ndipo tizipemphera ndi ufulu wa kulankhula+ kuti atichitire chifundo komanso kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi yoyenera.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “kuponya mbewu pansi.” Mbewuzo zikutanthauza ana a Adamu ndi Hava.
Mʼchilankhulo choyambirira, “malo amene mafupa amalumikizana.”