Kalata Yopita kwa Aheberi 13:1-25

  • Malangizo omaliza ndiponso kupereka moni (1-25)

    • Musaiwale kuchereza alendo (2)

    • Ukwati ukhale wolemekeza (4)

    • Muzimvera amene akukutsogolerani (7, 17)

    • Kupereka nsembe zotamanda Mulungu (15, 16)

13  Pitirizani kukonda abale.+  Musaiwale kuchereza alendo,*+ chifukwa pochita zimenezi, ena anachereza angelo mosadziwa.+  Muzikumbukira amene ali mʼndende+ ngati kuti mwamangidwa nawo limodzi.+ Muzikumbukiranso amene akuzunzidwa, popeza inunso ndinu anthu.*  Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posadetsedwa,+ chifukwa Mulungu adzaweruza achiwerewere* ndiponso achigololo.+  Musamakonde ndalama,+ koma muzikhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.+ Chifukwa Mulungu anati: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pangʼono.”+  Tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: “Yehova* ndi amene amandithandiza. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?”+  Muzikumbukira amene akukutsogolerani.+ Amenewa anakuphunzitsani mawu a Mulungu. Ndipo pamene mukuganizira zotsatira zabwino za khalidwe lawo, tsanzirani chikhulupiriro chawo.+  Yesu Khristu sanasinthe kuyambira dzulo mpaka lero ndipo sadzasintha mpaka kalekale.  Musasocheretsedwe ndi ziphunzitso zosiyanasiyana zachilendo. Kukoma mtima kwa Mulungu nʼkumene kungakuthandizeni kukhala olimba,* osati zakudya. Chifukwa anthu amene amangoganizira za zakudya,* siziwapindulitsa.+ 10  Ife tili ndi guwa lansembe limene ochita utumiki wopatulika kuchihema alibe ulamuliro wodya zapaguwapo.+ 11  Chifukwa nyama zimene magazi ake, mkulu wa ansembe amalowa nawo mʼmalo oyera ngati nsembe ya machimo, amakaziwotcha kunja kwa msasa.+ 12  Choncho nayenso Yesu anakavutikira kunja kwa geti la mzinda+ kuti ayeretse anthu ndi magazi ake.+ 13  Tiyeni timutsatire kunja kwa msasako, tikunyozedwa ngati mmene iye ananyozedwera.+ 14  Chifukwa panopa tilibe mzinda wokhazikika, koma tikufunitsitsa mzinda umene ukubwerawo.+ 15  Tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu kudzera mwa Yesu.+ Kuchita zimenezi kuli ngati nsembe imene tikupereka kwa Mulungu ndipo timagwiritsa ntchito milomo yathu+ polengeza dzina lake.+ 16  Komanso musaiwale kuchita zabwino ndi kugawira ena zomwe muli nazo,+ chifukwa Mulungu amasangalala ndi nsembe zoterozo.+ 17  Muzimvera amene akukutsogolerani+ ndipo muziwagonjera+ chifukwa iwo amayangʼanira miyoyo yanu ndipo adzayankha mlandu.+ Muzichita zimenezi kuti azigwira ntchito yawo mosangalala osati modandaula, chifukwa akatero sizingakuyendereni bwino. 18  Pitirizani kutipempherera, chifukwa tikukhulupirira kuti tili ndi chikumbumtima choyera* ndipo tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.+ 19  Koma makamaka ndikukulimbikitsani kundipempherera, kuti ndibwerere kumeneko mwamsanga. 20  Tsopano, Mulungu wamtendere amene anaukitsa mʼbusa wamkulu+ wa nkhosa amene ali ndi magazi a pangano losatha, Ambuye wathu Yesu, 21  akupatseni zinthu zonse zofunika kuti muchite chifuniro chake. Ndipo kudzera mwa Yesu Khristu, atithandize kuchita zinthu zomusangalatsa. Mulungu alandire ulemerero mpaka kalekale. Ame. 22  Tsopano abale, ndikukupemphani kuti mumvetsere moleza mtima mawu olimbikitsawa, chifukwa kalata imene ndakulemberaniyi si yaitali. 23  Dziwani kuti mʼbale wathu Timoteyo wamasulidwa ndipo ngati angabwere posachedwapa, ndibwera naye limodzi podzakuonani. 24  Mundiperekere moni kwa anthu onse amene akukutsogolerani ndiponso kwa oyera ena onse. Abale a ku Italy+ kuno akukupatsani moni. 25  Kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kukhale nanu nonsenu.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kukomera mtima anthu osawadziwa.”
Mabaibulo ena amati, “ngati kuti inunso mukuvutika nawo limodzi.”
Kutanthauza malamulo okhudza zakudya.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kungalimbitse mtima wanu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chabwino.”