Kalata Yopita kwa Aheberi 10:1-39

  • Nsembe za nyama zinali zosakwanira (1-4)

    • Chilamulo chinkachitira chithunzi zinthu zabwino (1)

  • Nsembe ya Khristu ndi yothandiza mpaka kalekale (5-18)

  • Njira yatsopano komanso yamoyo (19-25)

    • Tisaleke kusonkhana pamodzi (24, 25)

  • Anawachenjeza zokhudza kuchimwa mwadala (26-31)

  • Tizikhala olimba mtima komanso achikhulupiriro kuti tipirire (32-39)

10  Popeza Chilamulo chimangochitira chithunzi+ zinthu zabwino zimene zikubwera+ ndipo si zinthu zenizenizo, sichingachititse* amene amalambira Mulungu kukhala angwiro pogwiritsa ntchito nsembe zimene amapereka mosalekeza chaka chilichonse.+  Zikanakhala choncho, kodi nsembezo sakanasiya kuzipereka? Akanasiya chifukwa zikanakhala kuti anthu ochita utumiki wopatulikawo ayeretsedwa, sakanakhalanso ndi chikumbumtima chakuti ndi ochimwa.  Koma mosiyana ndi zimenezo, chaka chilichonse nsembe zimenezi zimawakumbutsa za machimo awo.+  Chifukwa nʼzosatheka kuti magazi a ngʼombe zamphongo ndi mbuzi achotseretu machimo.  Choncho atabwera padzikoli iye anati: “‘Nsembe zanyama komanso nsembe zina simunazifune, koma munandikonzera thupi.  Nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zamachimo simunazivomereze.’+  Ndiyeno ine ndinati, ‘Taonani! Ine ndabwera (mumpukutu munalembedwa za ine) kudzachita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.’”+  Atanena kuti: “Nsembe zanyama, nsembe zopsereza zathunthu, nsembe zamachimo ndiponso nsembe zina simunazifune kapena kuzivomereza,” zomwe ndi nsembe zoperekedwa mogwirizana ndi Chilamulo.  Ananenanso kuti: “Taonani! Ine ndabwera kudzachita chifuniro chanu.”+ Akuchotsa dongosolo loyambalo kuti akhazikitse lachiwiri. 10  Tayeretsedwa ndi “chifuniro” chimenecho,+ kudzera mʼthupi la Yesu Khristu limene analipereka nsembe kamodzi kokha.+ 11  Komanso, wansembe aliyense amaima pamalo ake kuti achite utumiki wopatulika+ ndiponso kuti apereke nsembe zimodzimodzizo mobwerezabwereza,+ zimene sizingachotseretu machimo.+ 12  Koma munthu ameneyu anapereka nsembe imodzi yamachimo yothandiza mpaka kalekale, ndipo anakhala kudzanja lamanja la Mulungu.+ 13  Kuyambira nthawi imeneyo, akudikira mpaka pamene adani ake adzaikidwe kuti akhale chopondapo mapazi ake.+ 14  Kudzera mu nsembe imodzi yokha, iye akuchititsa anthu amene akuyeretsedwa kukhala angwiro+ mpaka kalekale. 15  Nawonso mzimu woyera ukuchitira umboni kwa ife, chifukwa unanena kuti: 16  “‘Pangano limene ndidzapangane nawo pambuyo pa masiku amenewo ndi ili: Ndidzaika malamulo anga mʼmitima yawo ndipo ndidzawalemba mʼmaganizo awo,’+ akutero Yehova.”* 17  Kenako unanenanso kuti: “Ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo komanso zochita zawo zosonyeza kusamvera malamulo.”+ 18  Ndiyeno zimenezi zikakhululukidwa, nsembe yamachimo sikhalanso yofunika. 19  Choncho abale, timalimba mtima kulowa mʼmalo oyera+ chifukwa cha magazi a Yesu. 20  Iye ndi amene anatitsegulira njira imeneyi yomwe ndi yatsopano komanso yamoyo ndipo imadutsa katani yotchingira,+ imene ndi thupi lake. 21  Popeza tili ndi wansembe wamkulu kwambiri woyangʼanira nyumba ya Mulungu,+ 22  tiyeni tifike kwa Mulungu ndi mtima wonse komanso tili ndi chikhulupiriro chonse, chifukwa mitima yathu yayeretsedwa* kuti tisakhalenso ndi chikumbumtima choipa,+ ndipo matupi athu asambitsidwa mʼmadzi oyera.+ 23  Tiyeni tipitirize kulengeza poyera chiyembekezo chathu ndipo tisagwedezeke,+ chifukwa amene watilonjeza ndi wokhulupirika. 24  Ndipo tiyeni tiganizirane* kuti tilimbikitsane pa nkhani yosonyezana chikondi ndiponso kuchita zabwino.+ 25  Tisasiye kusonkhana pamodzi,+ ngati mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane+ ndipo tizichita zimenezi kwambiri, makamaka panopa pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.+ 26  Ngati tikuchita machimo mwadala pambuyo podziwa choonadi molondola,+ palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.+ 27  Koma pali chiyembekezo china choopsa cha chiweruzo, ndiponso mkwiyo woyaka moto umene udzawononge otsutsawo.+ 28  Munthu aliyense amene wanyalanyaza Chilamulo cha Mose amafa popanda kumuchitira chifundo, ngati anthu awiri kapena atatu apereka umboni.+ 29  Ndiye kuli bwanji munthu amene wapondaponda Mwana wa Mulungu, amene akuona magazi a pangano amene anayeretsedwa nawo ngati chinthu wamba,+ amenenso wanyoza mzimu umene Mulungu amasonyezera kukoma mtima kwakukulu?+ Munthu ameneyu akuyenera kulandira chilango chachikulu kwambiri. 30  Popeza tikumudziwa amene anati: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzabwezera ndine.” Amenenso anati: “Yehova* adzaweruza anthu ake.”+ 31  Kupatsidwa chilango ndi Mulungu wamoyo nʼkoopsa. 32  Komabe, pitirizani kukumbukira masiku akale. Paja mutalandira kuwala kochokera kwa Mulungu,+ munakumana ndi mavuto aakulu. 33  Nthawi zina munkanyozedwa ndiponso kuzunzidwa pagulu* ndipo nthawi zina munkathandiza anthu ena amene ankakumana ndi mavuto ngati amenewa. 34  Munkachitira chifundo anthu amene anali mʼndende, ndipo munkasangalalabe ngakhale katundu wanu akulandidwa,+ podziwa kuti muli ndi chuma chabwino kwambiri ndiponso chokhalitsa.+ 35  Choncho, musasiye kukhala olimba mtima* chifukwa mudzalandira mphoto yaikulu kwambiri.+ 36  Mukufunika kukhala opirira+ komanso kuchita chifuniro cha Mulungu kuti mudzalandire zimene Mulunguyo walonjeza. 37  “Kwatsala kanthawi kochepa”+ ndipo “amene akubwerayo afika ndithu, sachedwa.”+ 38  “Koma wolungama wanga adzakhala ndi moyo chifukwa cha chikhulupiriro chake,”+ ndipo “ngati angabwerere mʼmbuyo, ine sindikondwera naye.”+ 39  Ife sitili mʼgulu la anthu obwerera mʼmbuyo kupita kuchiwonongeko,+ koma ndife anthu okhala ndi chikhulupiriro chomwe chingatithandize kudzapeza moyo.

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “anthu sangachititse.”
Mʼchilankhulo choyambirira “yawazidwa,” kutanthauza kuti yawazidwa magazi a Yesu.
Kapena kuti, “tiziderana nkhawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kukhala ngati chionetsero mʼbwalo la masewera.”
Kapena kuti, “musataye ufulu wanu wa kulankhula.”