Yobu 1:1-22

  • Kukhulupirika kwa Yobu komanso chuma chake (1-5)

  • Satana anakaikira zolinga za Yobu (6-12)

  • Chuma cha Yobu chinawonongeka ndipo ana ake anafa (13-19)

  • Yobu sanaimbe Mulungu mlandu (20-22)

1  Mʼdziko la Uzi munali munthu wina dzina lake Yobu.*+ Iye anali munthu wokhulupirika amene ankachita zoyenera,*+ ankaopa Mulungu ndiponso ankapewa zoipa.+  Yobu anali ndi ana aamuna 7 komanso ana aakazi atatu.  Iye anali ndi nkhosa 7,000, ngamila 3,000, ngʼombe 1,000 ndi abulu 500.* Analinso ndi antchito ambiri, moti anali munthu wolemekezeka kwambiri pa anthu onse a Kumʼmawa.  Mwana wake aliyense wamwamuna ankakonza phwando kunyumba kwake pa tsiku limene wasankha.* Iwo ankaitana azichemwali awo atatu kuti adzadye ndi kumwera limodzi.  Akamaliza kuchita maphwando kunyumba zawo zonse, Yobu ankawaitana kuti adzawayeretse. Kenako iye ankadzuka mʼmamawa kwambiri nʼkuperekera mwana aliyense nsembe zopsereza.+ Chifukwa iye ankati: “Mwina ana anga achimwa ndipo anyoza Mulungu mumtima mwawo.” Izi ndi zimene Yobu ankachita nthawi zonse.+  Tsopano linafika tsiku limene ana a Mulungu woona*+ anapita kukaonekera pamaso pa Yehova,+ ndipo Satana+ nayenso anafika pakati pawo.+  Kenako Yehova anafunsa Satana kuti: “Kodi ukuchokera kuti iwe?” Satanayo anayankha Yehova kuti: “Ndimazungulira mʼdziko lapansi komanso kuyendayendamo.”+  Ndiyeno Yehova anafunsanso Satana kuti: “Kodi mtima wako uli pa mtumiki wanga Yobu? Padziko lapansi palibe wina wofanana naye. Iye ndi munthu wokhulupirika amene amachita zoyenera,*+ amaopa Mulungu ndiponso amapewa zoipa.”  Ndiyeno Satana anayankha Yehova kuti: “Kodi mukuganiza kuti Yobu amangoopa Mulungu popanda chifukwa?+ 10  Kodi inuyo simwamuteteza pomuikira mpanda?+ Mwatetezanso nyumba yake ndi zinthu zonse zimene ali nazo. Mwadalitsa ntchito ya manja ake+ ndipo ziweto zake zachuluka kwambiri mʼdzikoli. 11  Koma panopa mutambasule dzanja lanu nʼkuwononga zinthu zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani mʼmaso muli gwa!” 12  Kenako Yehova anauza Satana kuti: “Chabwino, chilichonse chimene ali nacho chili mʼmanja mwako. Koma dzanja lako lisakhudze munthuyo.” Zitatero Satana anachoka pamaso pa Yehova.+ 13  Tsopano pa tsiku limene ana a Yobu, aamuna ndi aakazi, ankadya komanso kumwa vinyo mʼnyumba ya mchimwene wawo wamkulu,+ 14  kunabwera munthu kwa Yobu kudzanena uthenga wakuti: “Ngʼombe zimalima ndipo abulu amadya msipu chapambali pake. 15  Kenako Asabeya anabwera nʼkutiukira ndipo analanda ziweto nʼkupha atumiki anu ndi lupanga. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka, choncho ndabwera kudzakuuzani uthengawu.” 16  Asanamalize kulankhula, munthu wina anabwera nʼkunena kuti: “Moto wa Mulungu unatsika* kuchokera kumwamba, ndipo unayaka pakati pa nkhosa ndi atumiki anu moti nkhosa komanso atumiki anuwo apsa. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka, choncho ndabwera kudzakuuzani uthengawu.” 17  Asanamalize kulankhula, munthu winanso anabwera nʼkudzanena kuti: “Akasidi+ anapanga magulu atatu ndipo anaukira ngamila zanu nʼkuzitenga, komanso apha atumiki anu ndi lupanga. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka, choncho ndabwera kudzakuuzani uthengawu.” 18  Asanamalize kulankhula, kunabwera munthu winanso kudzanena kuti: “Ana anu aamuna ndi aakazi amadya komanso kumwa vinyo mʼnyumba ya mchimwene wawo wamkulu. 19  Mwadzidzidzi kunabwera chimphepo kuchokera mʼchipululu ndipo chinawomba makona 4 a nyumbayo, moti nyumbayo yagwera ana anu nʼkuwapha. Ine ndekha ndi amene ndapulumuka, choncho ndabwera kudzakuuzani uthengawu.” 20  Yobu atamva zimenezi anaimirira nʼkungʼamba chovala chake ndiponso kumeta tsitsi kumutu kwake. Kenako anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi 21  nʼkunena kuti: “Ndinatuluka mʼmimba mwa mayi anga ndili wamaliseche,Ndipo ndidzabwerera ndilinso wamaliseche.+ Yehova wapereka,+ ndipo Yehova yemweyo watenga. Dzina la Yehova lipitirize kutamandidwa.” 22  Ngakhale kuti anakumana ndi zinthu zonsezi, Yobu sanachimwe kapena kuimba Mulungu mlandu woti wachita zinthu zoipa.*

Mawu a M'munsi

Nʼkutheka kuti dzinali limatanthauza “Munthu Wodedwa.”
Kapena kuti, “munthu wopanda cholakwa komanso wamtima wowongoka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “abulu aakazi 500.”
Kapena kuti, “kunyumba kwa aliyense tsiku lake likafika.”
Mawu okuluwika a Chiheberi onena za angelo omwe ndi ana a Mulungu.
Kapena kuti, “munthu wopanda cholakwa komanso wamtima woongoka.”
Mabaibulo ena amati, “Mphezi inatsika.”
Kapena kuti, “kapena kunena kuti Mulungu wachita zosayenera.”