Yobu 34:1-37

  • Elihu ananena kuti Mulungu amachita zinthu mwachilungamo (1-37)

    • Yobu ananena kuti Mulungu sanamuchitire zinthu mwachilungamo (5)

    • Mulungu woona sachita zoipa (10)

    • Yobu sankadziwa zinthu zina (35)

34  Elihu anapitiriza kulankhula kuti:   “Mvetserani mawu anga, anthu anzeru inu.Ndimvetsereni, inu anthu amene mukudziwa zambiri.   Chifukwa khutu limasiyanitsa mawu,Ngati mmene lilime limasiyanitsira* kakomedwe ka chakudya.   Tiyeni tifufuze tokha zimene zili zoyenera.Tisankhe tokha zimene zili zabwino.   Chifukwa Yobu wanena kuti, ‘Ndine wosalakwa,+Koma Mulungu sanafune kundichitira chilungamo.+   Kodi ndinganame za mmene chiweruzo changa chimayenera kukhalira? Chilonda changa sichikupola ngakhale kuti sindinachimwe.’+   Kodi pali munthu wina wofanana ndi Yobu,Amene amamwa mawu onyoza ngati madzi?   Iye akuganiza ngati anthu ochita zoipa,Ndipo akugwirizana ndi anthu oipa.+   Chifukwa wanena kuti, ‘Munthu sapindula chilichonseAkamayesetsa kuchita zosangalatsa Mulungu.’+ 10  Choncho ndimvetsereni, inu amuna omvetsa zinthu:* Nʼzosatheka kuti Mulungu woona achite zoipa,+Kapena kuti Wamphamvuyonse achite zinthu zolakwika.+ 11  Chifukwa iye amapereka mphoto kwa munthu mogwirizana ndi zimene amachita,+Ndipo amamusiya kuti akumane ndi mavuto chifukwa cha zochita zake. 12  Ndithudi, Mulungu sachita zoipa,+Ndipo Wamphamvuyonse sakhotetsa chilungamo.+ 13  Ndi ndani anamupatsa udindo woyangʼanira dziko lapansi?Ndipo ndi ndani anamusankha kuti azilamulira dziko lonse? 14  Iye akakwiyira anthu,Nʼkutenga mphamvu ya moyo* komanso mpweya wawo,+ 15  Anthu onse amafera limodzi,Ndipo anthuwo amabwerera kufumbi.+ 16  Choncho ngati mumamvetsa zinthu, mvetserani izi,Mvetserani mosamala zimene ndinene. 17  Kodi amene amadana ndi chilungamo angakhale wolamulira,Kapena kodi munthu wamphamvu amene ndi wolungama, mungamunene kuti ndi woipa? 18  Kodi mungauze mfumu kuti, ‘Ndinu wopanda pake,’ Kapena anthu olemekezeka kuti, ‘Ndinu oipaʼ?+ 19  Pali wina amene sakondera akalonga,Komanso sakondera anthu olemera kuposa osauka,*+Chifukwa onsewo anapangidwa ndi manja ake.+ 20  Iwo angafe mwadzidzidzi,+ pakati pa usiku.+Amaphupha nʼkufa.Ngakhale anthu amphamvu amawonongedwa, koma osati ndi manja a anthu.+ 21  Maso a Mulungu amayangʼanitsitsa njira za munthu,+Ndipo amaona chilichonse chimene akuchita. 22  Kulibe mdima wandiweyaniKumene anthu ochita zoipa angathe kubisala.+ 23  Chifukwa Mulungu sanaikiretu nthawi yoti munthu aliyenseAkaonekere pamaso pake kuti aweruzidwe. 24  Iye amaphwanya amphamvu ndipo safunikira kufufuza,Ndipo pamalo awo amaikapo anthu ena.+ 25  Chifukwa iye akudziwa zimene iwo akuchita.+Iye amawagonjetsa usiku ndipo iwo amaphwanyika.+ 26  Amawamenya anthu onse akuona,Chifukwa choti ndi oipa,+ 27  Chifukwa asiya kumutsatira,+Ndipo salemekeza chilichonse chimene iye akuchita,+ 28  Iwo amachititsa kuti osauka amulilire,Moti amamva kulira kwa anthu ovutika.+ 29  Ngati Mulungu atakhala chete, ndi ndani angamudzudzule? Ngati atabisa nkhope yake, ndi ndani angamuone? Kaya abisire nkhope yake mtundu wa anthu kapena munthu mmodzi, zotsatira zake nʼchimodzimodzi. 30  Kuti munthu woipa* asalamulire+Kapena kutchera anthu misampha. 31  Kodi munthu angauze Mulungu kuti,‘Ndalandira chilango ngakhale kuti sindinalakwe chilichonse.+ 32  Ndiphunzitseni zimene sindikudziwa,Ngati ndachita cholakwika chilichonse, sindidzachitanso?’ 33  Kodi ukufuna kuti akupatse mphoto mogwirizana ndi mmene iweyo ukuonera, pamene ukukana chiweruzo chake? Iweyo usankhe wekha, osati ine. Choncho ndiuze zimene ukuzidziwa bwino. 34  Anthu omvetsa zinthu* adzandiuza,Munthu aliyense wanzeru amene akundimvetsera adzandiuza kuti, 35  ‘Yobu sadziwa zimene akunena,+Ndipo mawu ake amasonyeza kuti ndi wosazindikira.’ 36  Yobu ayesedwe mpaka pamapetoChifukwa akuyankha ngati mmene anthu oipa amayankhira. 37  Chifukwa pa tchimo lake akuwonjezerapo kupanduka.+Amawomba mʼmanja monyogodola ife tikuonaNdipo amachulukitsa zonena zotsutsana ndi Mulungu woona.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼkamwa mumasiyanitsira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “inu amuna a mtima.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nʼkutenga mzimu.”
Kapena kuti, “olemekezeka kuposa onyozeka.”
Kapena kuti, “wampatuko.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Anthu a mtima.”