Yobu 37:1-24

  • Mphamvu zamʼchilengedwe zimasonyeza kuti Mulungu ndi wamkulu (1-24)

    • Mulungu angaimitse zochita za anthu (7)

    • ‘Ganizirani ntchito zodabwitsa za Mulungu’ (14)

    • Anthu sangathe kumumvetsa Mulungu (23)

    • Munthu aliyense asamadzione kuti ndi wanzeru (24)

37  “Chifukwa cha zimenezi, mtima wanga ukugunda kwambiri,Ukungokhala ngati uchoka mʼmalo mwake.  2  Mvetserani mwatcheru mawu amphamvu a Mulungu,Komanso mabingu ochokera mʼkamwa mwake.  3  Amene amamveka pansi ponse pa thambo,Ndipo amatumiza mphezi yake+ kumalekezero a dziko lapansi.  4  Pambuyo pake pamamveka phokoso.Iye amabangula ndi mawu amphamvu,+Ndipo mphezi zimakhala zikuwala iye akamalankhula.  5  Mulungu amabangula ndi mawu ake+ mochititsa chidwi kwambiri.Amachita zinthu zazikulu zimene sitingathe kuzimvetsa.+  6  Chifukwa amauza matalala kuti, ‘Gwerani padziko lapansi,’+ Ndipo mvula amaiuza kuti, ‘Igwa mwamphamvu kwambiri.’+  7  Mulungu amaimitsa chilichonse chimene anthu akuchita,*Kuti munthu aliyense adziwe ntchito Yake.  8  Nyama zakutchire zimapita mʼnyumba zawo,Ndipo zimakhalabe mʼmalo amene zimakhala.  9  Mphepo yamkuntho imaomba kuchokera kumalo ake,+Ndipo kuzizira kumachokera mumphepo yakumpoto.+ 10  Pogwiritsa ntchito mpweya wake Mulungu amapangitsa kuti madzi aundane,+Komanso kuti madzi aundane chifukwa cha kuzizira.+ 11  Iye amachititsa kuti mitambo ilemedwe ndi chinyontho.Amamwaza mphezi+ zake mʼmitambo. 12  Mitamboyo imayenda mozungulira ndipo iye amailamula kuti ipite kumene akufuna.Imachita chilichonse chimene iye walamula+ panthaka yapadziko lapansi.* 13  Amagwiritsa ntchito mitamboyo kuti apereke chilango,*+ kuti anyowetse dziko,Komanso kuti asonyeze chikondi chokhulupirika.+ 14  Mvetserani izi inu a Yobu,Imani ndi kuganizira mozama ntchito zodabwitsa za Mulungu.+ 15  Kodi mukudziwa zimene Mulungu amachita kuti alamulire mitamboKomanso zimene amachita kuti mphezi ziziwala mʼmitambo yake? 16  Kodi mukudziwa chimene chimachititsa kuti mitambo izikhala mʼmalere?+ Zimenezi ndi ntchito zodabwitsa za Mulungu amene amadziwa chilichonse.+ 17  Nʼchifukwa chiyani zovala zanu zimatentha,Pamene mphepo yakumʼmwera yachititsa dziko lapansi kuti likhale bata?+ 18  Kodi inuyo limodzi ndi iyeyo mungatambasule kuthambo,+Nʼkukumenyamenya kuti kukhale kolimba ngati chitsulo chonyezimira?* 19  Tiuzeni zoti timuuze.Sitingathe kuyankha chifukwa tili mumdima. 20  Kodi auzidwe kuti ndikufuna kulankhula? Kapena kodi munthu wina wanena zinazake zimene akufunika kuti auzidwe?+ 21  Iwo sangathe nʼkomwe kuona kuwala,*Ngakhale kuti kuthambo nʼkowala,Mpaka mphepo itadutsa nʼkuchotsa mitambo. 22  Ulemerero wonyezimira ngati golide umachokera kumpoto.Ulemerero wa Mulungu+ ndi wochititsa mantha. 23  Wamphamvuyonse sitingathe kumumvetsa.+Iye ali ndi mphamvu zazikulu,+Ndipo sachita zinthu zosemphana ndi chilungamo+ chake komanso kulungama kwake kodabwitsa.+ 24  Choncho anthu azimuopa.+ Chifukwa sakondera aliyense amene amadziona kuti ndi wanzeru.”*+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “amaika chidindo padzanja la munthu aliyense.”
Kapena kuti, “panthaka yachonde yapadziko lapansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ngati chikwapu.”
Kapena kuti, “ngati galasi lachitsulo.”
Kumene ndi kuwala kwa dzuwa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene ali ndi mtima wanzeru.”