Yobu 11:1-20
11 Zofari+ wa ku Naama anayankha kuti:
2 “Kodi ukuganiza kuti mawu ako onsewa angakhale osayankhidwa?Kapena kodi kulankhula kwambiri kungachititse kuti munthu akhale wosalakwa?*
3 Kodi zolankhula zako zopanda pake zingachititse kuti anthu akhale chete?
Kodi sipapezeka wokudzudzula chifukwa cha mawu ako onyoza?+
4 Chifukwa ukunena kuti, ‘Zimene ndimaphunzitsa ndi zoyera,+Ndipo Mulungu amandiona kuti ndine woyera.’+
5 Koma zikanakhala bwino Mulungu akanalankhula yekhaNʼkukutsegulira pakamwa pake.+
6 Bwenzi atakuululira chinsinsi cha nzeru,Chifukwa pali zambiri zofunika kuziphunzira zokhudza nzeru yeniyeni.
Bwenzi utazindikira kuti Mulungu walola kuti zolakwa zako zina ziiwalike.
7 Kodi ungazindikire zinthu zozama za Mulungu,Kapena kodi ungadziwe chilichonse chokhudza* Wamphamvuyonse?
8 Zili kutali kuposa kumwamba. Iwe sungathe kuzipeza.
Nʼzozama kuposa Manda.* Ungadziwe chiyani iwe?
9 Nʼzazitali kuposa dziko lapansiNdipo nʼzazikulu kuposa nyanja.
10 Iye akadutsa nʼkugwira winawake nʼkumupititsa kukhoti,Ndi ndani angatsutsane naye?
11 Iye amadziwa anthu akamachita zachinyengo.
Akaona anthu akuchita zoipa, kodi iye sizimamukhudza?
12 Koma munthu wopanda nzeru angamvetsePokhapokha ngati bulu wamʼtchire atabereka munthu.
13 Zikanakhala bwino ukanakonza mtima wakoNʼkutambasula manja ako kwa iye.
14 Ngati ukuchita chinachake cholakwika, usiyiretu kuchichita,Ndipo usalole kuti mʼmatenti ako mukhale zinthu zopanda chilungamo.
15 Ukatero, udzadzutsa nkhope yako osachita manyazi,Udzakhala wolimba ndipo sudzaopa chilichonse.
16 Ukatero udzaiwala mavuto ako,Udzawaiwala ngati madzi amene adutsa pafupi ndi iwe.
17 Masiku a moyo wako adzakhala owala kuposa masana,Ngakhale usiku udzakhala ngati mʼmawa.
18 Udzalimba mtima chifukwa chakuti pali chiyembekezo.Udzayangʼana paliponse ndipo udzagona mopanda mantha.
19 Udzagona popanda aliyense wokuopseza,Ndipo anthu ambiri adzafuna kuti uwachitire chifundo.
20 Koma maso a anthu oipa sadzaonanso,Ndipo sadzapeza malo othawirako,Chiyembekezo chawo chidzakhala imfa* basi.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Kapena kodi munthu wodzitama angakhale wosalakwa?”
^ Kapena kuti, “ungadziwe malire a kukula kwa.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “kutha kwa moyo.”