Yobu 7:1-21

  • Yankho la Yobu likupitirira (1-21)

    • Moyo uli ngati ntchito yokakamiza (1, 2)

    • “Nʼchifukwa chiyani mukulimbana ndi ine?” (20)

7  “Kodi moyo wa munthu padziko lapansi suli ngati ntchito yokakamiza?Ndipo kodi masiku ake sali ngati masiku a munthu waganyu?+   Mofanana ndi kapolo, iye amalakalaka mthunzi,Ndipo mofanana ndi munthu waganyu, iye amadikirira malipiro ake.+   Choncho kwa miyezi yambiri moyo wanga wakhala wachabechabeNdipo usiku wambiri ndimakhala ndikuvutika.+   Ndikagona ndimafunsa kuti, ‘Kodi kucha nthawi yanji?’+ Usikuwo umatalika ndipo ndimangotembenukatembenuka mpaka mʼbandakucha.   Mnofu wanga wakutidwa ndi mphutsi komanso fumbi,+Khungu langa langʼambika nʼkumatuluka mafinya.+   Masiku anga akuthamanga kuposa mashini owombera nsalu,+Atha mofulumira ndipo ine ndilibe chiyembekezo.+   Kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mphepo,+Ndiponso kuti diso langa silidzaonanso zinthu zosangalatsa.*   Diso limene likundiona panopa silidzandionanso,Mudzandifunafuna, koma ine kudzakhala kulibe.+   Mofanana ndi mtambo umene umazimiririka nʼkutha,Munthu amene wapita ku Manda,* sabwerera.+ 10  Iye sadzabwereranso kunyumba yake,Ndipo anthu a pamalo ake sadzamukumbukiranso.+ 11  Choncho, ine sinditseka pakamwa panga. Ndilankhula chifukwa cha ululu umene ndikumva mumtima mwanga,Ndidandaula mopwetekedwa mtima.+ 12  Kodi ine ndine nyanja, kapena chilombo cha mʼnyanja,Kuti mundiikire mlonda? 13  Ndikanena kuti, ‘Bedi langa linditonthoza,Bedi langa lindithandiza kuchepetsako chisoni changa,’ 14  Inuyo mumandiopseza ndi maloto,Ndipo mumandichititsa mantha ndi masomphenya. 15  Choncho ndikulakalaka kufa chifukwa chobanika,Kulibwino ndife kusiyana nʼkuti thupi langa likhale chonchi.+ 16  Moyo wanga ndikunyansidwa nawo,+ sindikufuna kupitirizanso kukhala ndi moyo. Ndisiyeni, chifukwa masiku anga ali ngati mpweya wotuluka mʼmphuno.+ 17  Kodi munthu ndi ndani kuti muzida naye nkhawa,Nʼkumamuganizira?*+ 18  Nʼchifukwa chiyani mumamuyendera mʼmawa uliwonse,Nʼkumamuyesa nthawi zonse?+ 19  Nʼchifukwa chiyani simukusiya kundiyangʼana,Nʼkundipatsa nthawi yokwanira kuti ndingomezako malovu?+ 20  Ngati ndachimwa, kodi zimakukhudzani bwanji, Inu amene mumayangʼanitsitsa anthu?+ Nʼchifukwa chiyani mukulimbana ndi ine? Kodi ndakhala mtolo wolemera kwa inu? 21  Nʼchifukwa chiyani simukundikhululukira machimo anga,Nʼkunyalanyaza zolakwa zanga? Chifukwa posachedwapa ndigona mʼfumbi,+Ndipo mudzandifunafuna koma ine kudzakhala kulibe.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “zabwino.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkuika mtima wanu pa iye?”