Yobu 8:1-22
8 Bilidadi+ wa ku Shuwa+ anayankha kuti:
2 “Kodi ukhala ukulankhula chonchi mpaka liti?+
Mawu a mʼkamwa mwako ali ngati mphepo yamphamvu.
3 Kodi Mulungu angapotoze chilungamo?Kapena kodi Wamphamvuyonse angapotoze zinthu zimene ndi zolungama?
4 Ngati ana ako anamuchimwira,Iye anawalanga chifukwa cha kupanduka kwawo,*
5 Koma ngati iweyo utayangʼana kwa Mulungu,+Nʼkuchonderera Wamphamvuyonse kuti akuchitire chifundo,
6 Ndipo ngati ukanakhaladi woyera komanso ngati umachitadi zoyenera,+Iye akanakumvera*Ndipo akanakubwezeretsa mmene unalili poyamba.
7 Ndipo ngakhale kuti chiyambi chako chinali chachingʼono,Tsogolo lako likanakhala lalikulu.+
8 Tafunsa mʼbadwo wakale,Ndipo ganizira zinthu zimene makolo awo anapeza.+
9 Chifukwa ife tabadwa dzulodzuloli, ndipo sitikudziwa kalikonse,Chifukwa masiku athu padziko lapansi ali ngati mthunzi.
10 Kodi iwo sadzakulangizaNdipo sadzakuuza zimene akudziwa?*
11 Kodi gumbwa* angamere pamalo pamene si padambo?
Ndipo kodi bango lingakule popanda madzi?
12 Lidakali ndi maluwa, lisanadulidwe nʼkomwe,Lidzauma zomera zonse zisanaume.
13 Zimenezi ndi zimene zidzachitikire* anthu onse amene aiwala Mulungu,Chifukwa chiyembekezo cha anthu oipa* chidzatha,
14 Anthu amene amadalira zinthu zosathandiza,Amene amadalira zinthu zosalimba ngati ulusi wa kangaude.*
15 Iye adzatsamira nyumba yake, koma idzagwa.Adzayesetsa kuigwira, koma sidzalimba.
16 Iye ali ngati chomera chothiriridwa chimene chili padzuwa.Ndipo nthambi zake zimakula mʼmunda.+
17 Mizu yake imapiringizana pamulu wa miyala.Iye amaona kuti miyalayo ndi nyumba yake.
18 Koma akazulidwa* pamalo akewo,Malowo adzamukana nʼkunena kuti, ‘Ine sindinayambe ndakuonapo.’+
19 Umu ndi mmene adzathere,*+Kenako zomera zina zidzamera kuchokera mufumbi.
20 Ndithudi, Mulungu sadzakana anthu okhulupirika,*Kapena kuthandiza* anthu ochita zoipa.
21 Chifukwa adzakupangitsa kuti useke,Ndipo udzafuulanso chifukwa chosangalala.
22 Anthu odana nawe adzachita manyazi,Ndipo tenti ya anthu oipa kudzakhala kulibe.”
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Iye anawapereka mʼmanja mwa kupanduka kwawo.”
^ Kapena kuti, “Iye akanadzuka kuti akumvere.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “sadzatulutsa mawu kuchokera mʼmitima yawo?”
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mmenemu ndi mmene zilili njira za.”
^ Kapena kuti, “ampatuko.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “nyumba ya kangaude.”
^ Kapena kuti, “akamezedwa.”
^ Kapena kuti, “Umu ndi mmene njira yake idzathere.”
^ Kapena kuti, “anthu opanda cholakwa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “kugwira dzanja la.”