Yobu 26:1-14
26 Yobu anayankha kuti:
2 “Komatu ndiye wathandiza munthu wopanda mphamvu!
Wapulumutsa munthu wa manja ofooka.+
3 Waperekadi malangizo othandiza kwa munthu wopanda nzeru.+
Komanso wachititsa kuti anthu ambiri adziwe nzeru zothandiza.
4 Kodi ukuuza ndani,Ndipo ndi ndani amene wakuuzira zimene ukunenazi?*
5 Akufa alibe mphamvu ndipo amanjenjemera pamaso pa Mulungu.Iwo ali pansi kwambiri kuposa madzi ndi zonse zimene zimakhala mmenemo.
6 Manda* ali maliseche pamaso pa Mulungu,+Ndipo malo achiwonongeko* amakhala osavundikira.
7 Iye anatambasula thambo lakumpoto* pamwamba pa malo opanda kanthu,+Ndipo dziko lapansi analiika mʼmalere.
8 Iye anakulunga madzi mʼmitambo yake,+Mʼnjira yoti mitamboyo isaphulike chifukwa cha kulemera kwa madziwo.
9 Anaphimba mpando wake wachifumu kuti usamaoneke,Anauphimba ndi mtambo wake.+
10 Anaika malire pakati pa thambo ndi nyanja,+Anaika malire pakati pa kuwala ndi mdima.
11 Zipilala zakumwamba zimanjenjemera,Zimachita mantha ndi kudzudzula kwa Mulungu.
12 Ndi mphamvu zake amavundula nyanja,+Ndipo ndi kuzindikira kwake amaduladula chilombo cha mʼnyanja.*+
13 Ndi mpweya umene wapuma,* amapangitsa kuti kumwamba kukhale koyera.Dzanja lake limabaya njoka yothamanga.
14 Komatu zimenezi ndi kambali kakangʼono chabe ka zochita zake,+Ndipo tangomva kunongʼona kwapansipansi kwa mphamvu zake.
Ndiye ndi ndani amene angamvetse mabingu ake amphamvu?”+
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Kodi mpweya (mzimu) umene watuluka mwa iwe ndi wandani?”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “Ndipo Abadoni.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anatambasula kumpoto.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amaduladula Rahabi.”
^ Kapena kuti, “mphepo.”