Yobu 2:1-13

  • Satana anakaikira kachiwiri zolinga za Yobu (1-5)

  • Satana analoledwa kuti abweretse mavuto pa thupi la Yobu (6-8)

  • Mkazi wa Yobu ananena kuti: “Tukwanani Mulungu mufe!” (9, 10)

  • Anzake a Yobu atatu anabwera (11-13)

2  Pambuyo pa zimenezi, linafika tsiku limene ana a Mulungu woona*+ anapita kukaonekera pamaso pa Yehova,+ ndipo Satana nayenso anapita kukaonekera pamaso pa Yehova.+  Kenako Yehova anafunsa Satana kuti: “Kodi ukuchokera kuti iwe?” Satanayo anayankha Yehova kuti: “Ndimazungulira mʼdziko lapansi komanso kuyendayendamo.”+  Ndiyeno Yehova anafunsanso Satana kuti: “Kodi mtima wako uli pa mtumiki wanga Yobu? Padziko lapansi palibe wina wofanana naye. Iye ndi munthu wokhulupirika amene amachita zoyenera,*+ amaopa Mulungu ndiponso amapewa zoipa. Iye akupitirizabe kukhala wokhulupirika+ ngakhale kuti iweyo ukufuna kuti ndimuwononge*+ popanda chifukwa.”  Koma Satana anayankha Yehova kuti: “Khungu kusinthanitsa ndi khungu. Munthu angapereke chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.  Koma panopa mutambasule dzanja lanu nʼkuwononga thupi lake,* ndipo akutukwanani mʼmaso muli gwa!”+  Ndiyeno Yehova anauza Satana kuti: “Chabwino, iye ali mʼmanja mwako. Koma usachotse moyo wake.”  Choncho Satana anachoka pamaso pa Yehova nʼkukachititsa kuti Yobu azunzike ndi zilonda zopweteka,+ kuyambira kuphazi mpaka kumutu.  Ndiyeno Yobu anatenga phale loti azidzikandira ndipo ankakhala paphulusa.+  Patapita nthawi, mkazi wake anamufunsa kuti: “Kodi mukupitirizabe kukhala wokhulupirika? Tukwanani Mulungu mufe!” 10  Koma Yobu anamuyankha kuti: “Ukulankhula ngati mmene amalankhulira akazi opusa. Kodi tizingolandira zabwino zokhazokha kuchokera kwa Mulungu woona osalandiranso zoipa?”+ Ngakhale kuti anakumana ndi zonsezi, Yobu sananene chilichonse cholakwika.*+ 11  Anzake atatu a Yobu anamva za masoka onse amene anamugwera ndipo aliyense wa iwo anabwera kuchokera kwawo. Mayina awo anali Elifazi+ wa ku Temani, Bilidadi+ wa ku Shuwa+ ndi Zofari+ wa ku Naama. Iwo anapangana kuti akumane kuti apite akatonthoze Yobu ndi kumulimbikitsa. 12  Atamuona ali chapatali, sanamuzindikire. Kenako anayamba kulira mokweza mawu ndipo anangʼamba zovala zawo nʼkumawaza fumbi mʼmwamba komanso pamutu pawo.+ 13  Kenako anakhala pansi limodzi ndi Yobuyo kwa masiku 7 masana ndi usiku. Palibe amene analankhula naye chilichonse chifukwa anaona kuti ululu wake unali waukulu kwambiri.+

Mawu a M'munsi

Mawu okuluwika a Chiheberi onena za angelo omwe ndi ana a Mulungu.
Kapena kuti, “munthu wopanda cholakwa komanso wamtima wowongoka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndimumeze.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkuwononga fupa ndi mnofu wake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Yobu sanachimwe ndi milomo yake.”