Yobu 14:1-22

  • Yankho la Yobu likupitirira (1-22)

    • Munthu amakhala ndi moyo waufupi komanso wodzaza ndi mavuto (1)

    • “Ngakhale mtengo umakhala ndi chiyembekezo” (7)

    • ‘Zikanakhala bwino mukanandibisa mʼManda’ (13)

    • “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?” (14)

    • Mulungu adzalakalaka ntchito ya manja ake (15)

14  “Munthu wobadwa kwa mkazi,Amakhala ndi moyo waufupi+ komanso wodzaza ndi mavuto.+   Amaphuka ngati duwa kenako nʼkufota.+Amathawa ngati mthunzi ndipo saonekanso.+   Inde, mukumuyangʼanitsitsa ndi diso lanu,Ndipo inu mukumuzenga* mlandu.+   Kodi munthu wochimwa angabereke munthu wosachimwa?*+ Ayi nʼzosatheka.   Masiku a munthu ndi odziwika,Ndipo chiwerengero cha miyezi yake chili mʼmanja mwanu.Mwamuikira malire kuti asapitirire.+   Siyani kumuyangʼanitsitsa kuti apume,Mpaka atamaliza tsiku lake ngati mmene amachitira waganyu.+   Ngakhale mtengo umakhala ndi chiyembekezo. Ukadulidwa umaphukanso,Ndipo nthambi zake zidzapitiriza kukula.   Ngati muzu wake wakalamba mʼnthaka,Ndipo chitsa chake chafa mʼdothi,   Ukadzangomva fungo la madzi udzaphukira,Ndipo udzaphuka nthambi ngati mtengo watsopano. 10  Koma munthu amafa ndipo mphamvu zake zonse zimatha.Munthu akafa, kodi amapita kuti?+ 11  Madzi amatha mʼnyanja,Ndipo mtsinje umaphwa nʼkuuma. 12  Munthu nayenso amagona pansi ndipo sadzuka.+ Sadzadzuka mpaka kumwamba kutachoka,Sadzadzutsidwa ku tulo take.+ 13  Zikanakhala bwino mukanandibisa mʼManda,*+Mukanandibisa mpaka mkwiyo wanu utadutsa,Zikanakhala bwino mukanandiikira nthawi nʼkudzandikumbukira.+ 14  Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?+ Ndidzadikira masiku onse a ntchito yanga yokakamiza,Mpaka mpumulo wanga utafika.+ 15  Inu mudzaitana ndipo ine ndidzakuyankhani.+ Mudzalakalaka ntchito ya manja anu. 16  Koma panopa mukungokhalira kuwerenga paliponse pamene mapazi anga aponda,Mukungoyangʼana machimo anga basi. 17  Kulakwa kwanga mwakutsekera mʼthumba,Ndipo mwamata machimo anga ndi zomatira. 18  Phiri limagwa nʼkugumukagumuka,Ndipo thanthwe limasuntha pamalo ake. 19  Madzi amaperepesa miyalaNdipo mitsinje yake imakokolola dothi lapadziko lapansi.Inunso mwawononga chiyembekezo cha munthu. 20  Mukupitiriza kumugonjetsa mpaka atatheratu.+Mwasintha maonekedwe ake nʼkumuthamangitsa. 21  Ana ake amalemekezedwa, koma iye sadziwa zimenezo.Iwo amakhala onyozeka, koma iye sazindikira zimenezo.+ 22  Amamva kuwawa pa nthawi yokhayo imene ali ndi moyo,Iye amalira pa nthawi yokhayo imene ali moyo.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mukundizenga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Kodi munthu woyera angabadwe kwa munthu wodetsedwa?”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.