Yobu 16:1-22
16 Yobu anayankha kuti:
2 “Ndamvapo zinthu zambiri ngati zimenezi.
Nonsenu ndinu otonthoza obweretsa mavuto!+
3 Kodi simusiya kulankhula mawu opanda pakewa?*
Chikukupwetekani nʼchiyani kuti muziyankha chonchi?
4 Inenso ndikanatha kulankhula ngati mmene mukuchitiramu.
Mukanakhala kuti mukukumana ndi mavuto ngati angawa,*Ndikanalankhula mawu ambiri okudzudzulaniKomanso kukupukusirani mutu.+
5 Koma sindikanatero, mʼmalomwake ndikanakulimbikitsani ndi mawu amʼkamwa mwanga,Ndipo mawu otonthoza apakamwa panga akanakulimbikitsani.+
6 Ndikalankhula, ululu wanga sukuchepa,+Ndipo ndikasiya kulankhula, ululu wanga sukutha.
7 Koma tsopano Mulungu wanditopetsa.+Wawononga onse amene amakhala mʼnyumba yanga.*
8 Komanso iye wandigwira ndipo anthu ena akuona zimenezi,Moti kuwonda kwangaku ndi umboni wonditsutsa.
9 Mkwiyo wa Mulungu wandikhadzula ndipo akundisungira chidani.+
Iye akundikukutira mano.
Mdani wanga akundiyangʼana mokwiya nʼcholinga choti andivulaze.+
10 Anthu atsegula kukamwa kwawo kuti andimeze.+Ndipo andimenya mbama pofuna kundichititsa manyazi.Iwo asonkhana ambirimbiri kuti alimbane nane.+
11 Mulungu wandipereka kwa tianyamata,Ndipo wandiponya mʼmanja mwa oipa.+
12 Ine ndinali pa mtendere koma iye wandiphwanya.+Wandigwira kumbuyo kwa khosi nʼkundimenyetsa pansi,Kenako wandiponyera mivi yake.
13 Anthu ake oponya mivi ndi uta andizungulira.+Iye waboola impso zanga+ ndipo sakumva chisoni,Wakhuthulira ndulu yanga pansi.
14 Iye akungokhalira kundiboola ngati khoma.Akundithamangira ngati msilikali.
15 Ndasoka ziguduli kuti ndibise khungu langa,+Ndipo ndakwirira ulemu wanga* mufumbi.+
16 Nkhope yanga yafiira chifukwa cholira,+Ndipo pazikope zanga pali mdima wandiweyani,*
17 Ngakhale kuti manja anga sanachite zachiwawa,Ndipo pemphero langa ndi loyera.
18 Iwe dziko lapansi, usabise magazi anga.+
Alole kuti alire mʼmalo mwa ine.
19 Ngakhale panopa, mboni yanga ili kumwamba,Amene angandichitire umboni ali mʼmwamba.
20 Anzanga akundinyoza+Pamene ndikupemphera kwa Mulungu ndikugwetsa misozi.+
21 Wina aweruze pakati pa munthu ndi Mulungu,Ngati mmene angaweruzire pakati pa munthu ndi mnzake.+
22 Chifukwa ndangotsala ndi zaka zochepa,Ndipo ndidzayenda mʼnjira imene sindidzabwereranso.”+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Kodi simusiya kulongololaku?”
^ Kapena kuti, “Moyo wanu ukanakhala ngati mmene moyo wanga ulili.”
^ Kapena kuti, “onse osonkhana nane.”
^ Kapena kuti, “mphamvu yanga.” Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga yanga.”
^ Kapena kuti, “pali mthunzi wa imfa.”