Deuteronomo 32:1-52

  • Nyimbo ya Mose (1-47)

    • Yehova ndi Thanthwe (4)

    • Aisiraeli anaiwala Thanthwe lawo (18)

    • “Kubwezera ndi kwanga” (35)

    • “Inu anthu a mitundu ina, sangalalani limodzi ndi anthu ake” (43)

  • Mose akafera mʼphiri la Nebo (48-52)

32  “Tamverani kumwamba inu, ndipo ine ndilankhula,Dziko lapansi limve mawu a pakamwa panga.  2  Malangizo anga adzagwa ngati mvula,Mawu anga adzatsika ngati mame,Ngati mvula yowaza pa udzu,Ngatinso mvula yamphamvu pazomera.  3  Chifukwa ndidzalengeza dzina la Yehova.+ Anthu inu, lengezani za ukulu wa Mulungu wathu!+  4  Iye ndi Thanthwe, ndipo ntchito yake ndi yangwiro,+Njira zake zonse ndi zolungama.+ Mulungu wokhulupirika,+ amene sachita zinthu zopanda chilungamo.+Iye ndi wolungama ndi wowongoka.+  5  Iwo ndi amene achita zinthu zoipa.+ Iwo si ana ake, ali ndi vuto ndi iwowo.+ Iwo ndi mʼbadwo wopotoka maganizo komanso wachinyengo!+  6  Kodi Yehova mukuyenera kumuchitira zimenezi,+Anthu opusa ndi opanda nzeru inu?+ Kodi iye si Atate wanu amene anakulengani,+Amene anakupangani ndi kukukhazikitsani monga mtundu?  7  Kumbukirani masiku akale,Ganizirani zaka za mibadwo ya mʼmbuyo. Funsani bambo anu ndipo akuuzani,+Amuna achikulire pakati panu, ndipo akufotokozerani.  8  Pamene Wamʼmwambamwamba anapereka cholowa ku mitundu ya anthu,+Pamene analekanitsa ana a Adamu,*+Anaika malire a anthu ena onse+Poganizira chiwerengero cha ana a Isiraeli.+  9  Pakuti anthu a Yehova ndi gawo lake.+Yakobo ndiye cholowa chake.+ 10  Anamupeza mʼdziko lachipululu,+Mʼchipululu chopanda kanthu, molira zilombo.+ Anamuzungulira kuti amuteteze, anamusamalira,+Ndipo anamuteteza ngati mwana wa diso lake.+ 11  Monga mmene chiwombankhanga chimagwedezera chisa chake,Mmene chimaulukira pamwamba pa ana ake,Mmene chimatambasulira mapiko ake, kuti chitenge anawo,Nʼkuwanyamula pamapiko ake,+ 12  Ndi Yehova yekha amene anapitiriza kumutsogolera,*+Panalibe mulungu wachilendo amene anali naye.+ 13  Anamuyendetsa pamapiri a dziko lapansi,+Moti anadya zokolola za mʼmunda.+ Anamudyetsa uchi wochokera mʼthanthwe,Ndi mafuta ochokera mʼmwala wa nsangalabwi. 14  Anamudyetsanso mafuta a mkaka wa ngʼombe ndi mkaka wa nkhosa,Pamodzi ndi nkhosa zabwino kwambiri,*Komanso nkhosa zamphongo za ku Basana ndi mbuzi zamphongo,Pamodzi ndi tirigu wabwino koposa.*+Ndipo munamwa vinyo wochokera mʼmagazi a mphesa.* 15  Yesuruni* atanenepa, anapandukira mbuye wake. Iwe wanenepa, wakula thupi, wakhuta mopitirira muyezo.+ Choncho iye anasiya Mulungu amene anamupanga,+Ndipo ananyoza Thanthwe la chipulumutso chake. 16  Anamukwiyitsa ndi milungu yachilendo.+Ankamukhumudwitsa ndi zinthu zonyansa.+ 17  Iwo ankapereka nsembe kwa ziwanda, osati kwa Mulungu.+Anapereka nsembe kwa milungu imene sankaidziwa,Kwa milungu yatsopano yongobwera kumene,Komanso kwa milungu imene makolo anu sankaidziwa. 18  Munaiwala Thanthwe+ limene linakuberekani,Ndipo simunakumbukire Mulungu amene anakuberekani.+ 19  Yehova ataona zimenezi anawakana+Chifukwa chakuti ana ake aamuna ndi aakazi anamukhumudwitsa. 20  Choncho iye anati, ‘Ndiwabisira nkhope yanga,+Ndione kuti ziwathera bwanji. Chifukwa iwo ndi mʼbadwo wokonda zoipa,+Ana osakhulupirika.+ 21  Iwo andikwiyitsa* ndi milungu yabodza.+Andikhumudwitsa ndi mafano awo opanda pake.+ Choncho ine ndiwachititsa nsanje ndi anthu opanda pake,+Ndiwakhumudwitsa ndi mtundu wopusa.+ 22  Mkwiyo wanga wayatsa moto+Umene udzayaka mpaka kukafika pansi penipeni pa Manda,*+Ndipo udzapsereza dziko lapansi ndi zokolola zake,Komanso udzayatsa maziko a mapiri. 23  Ndidzawonjezera masoka awo,Mivi yanga yonse ndidzaigwiritsa ntchito pa iwo. 24  Adzalefuka ndi njala+Ndipo adzavutika ndi kutentha thupi koopsa komanso adzawonongedwa nʼkutheratu.+ Ndidzawatumizira zilombo za mano ataliatali+Komanso njoka zapoizoni za mʼfumbi. 25  Kunja, lupanga lidzawasandutsa anamfedwa.+Mʼnyumba, anthu adzagwidwa ndi mantha+Zimenezi zidzachitikira mnyamata, namwali,Mwana wamngʼono ndi munthu wa imvi.+ 26  Ndikanatha kunena kuti: “Ndidzawabalalitsa,Ndidzachititsa kuti anthu asakumbukirenso za iwo,” 27  Koma ndinkaopa zimene mdani anganene,+Chifukwa adaniwo angaganize molakwika.+ Iwo anganene kuti: “Tapambana chifukwa cha mphamvu zathu,+Si Yehova amene wachita zonsezi.” 28  Chifukwa iwo ndi mtundu wopanda nzeru,*Ndipo ndi osazindikira.+ 29  Zikanakhala bwino ngati akanakhala anzeru,+ chifukwa akanaganizira mozama zimenezi.+ Akanaganizira kuti ziwathera bwanji.+ 30  Kodi munthu mmodzi angathamangitse bwanji anthu 1,000,Kapena anthu awiri angathamangitse bwanji anthu 10,000?+ Nʼzosatheka, pokhapokha Thanthwe lawo litawagulitsa,+Komanso ngati Yehova atawapereka. 31  Chifukwa thanthwe lawo si lofanana ndi Thanthwe lathu,+Ndipo adani athu akudziwa bwino zimenezi.+ 32  Mtengo wawo wa mpesa ndi wochokera ku mtengo wa mpesa wa ku Sodomu,Ndi kuminda ya mʼmapiri a ku Gomora.+ Zipatso zawo za mphesa ndi zapoizoniNdipo ndi zowawa.+ 33  Vinyo wawo ndi poizoni wa njoka,Ndi poizoni woopsa wa mamba. 34  Kodi ine sindinasunge zimenezi,Nʼkuziikira chidindo mʼnyumba yanga yosungira zinthu?+ 35  Kubwezera ndi kwanga, chilangonso ndi changa.+Zimenezi zidzachitika pa nthawi yoikidwiratu phazi lawo likadzaterereka,+Chifukwa tsiku la tsoka lawo layandikira,Ndipo zowagwera zifika mofulumira.’ 36  Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake,+Ndipo adzamvera chisoni atumiki ake+Akadzaona kuti mphamvu zawo zatha,Komanso kuti kwangotsala anthu ovutika ndi ofooka. 37  Ndiyeno iye adzanena kuti, ‘Ili kuti milungu yawo,+Thanthwe limene anathawirako, 38  Milungu imene inkadya mafuta a nsembe zawo,*Ndi kumwa vinyo wa nsembe zawo zachakumwa?+ Ibwere kudzakuthandizani. Ikhale malo anu othawirako. 39  Onani tsopano kuti ndine Mulungu,+Ndipo palibe Mulungu wina koma ine ndekha.+ Ndimapha komanso ndimapereka moyo.+ Ndimavulaza,+ ndipo ndidzachiritsa,+Palibe aliyense amene angapulumutse munthu mʼdzanja langa.+ 40  Ndakweza dzanja langa kumwambaNdipo ndikulumbira kuti: “Ine, Mulungu wamuyaya, ndikulumbira pa dzina langa,”+ 41  Ndikanola lupanga langa lonyezimira,Nʼkukonzekeretsa dzanja langa kuti lipereke chiweruzo,+Ndidzabwezera adani anga,+Ndipo ndidzapereka chilango kwa amene amadana nane. 42  Ndidzaledzeretsa mivi yanga ndi magazi,Ndipo lupanga langa lidzadya nyama,Ndi magazi a anthu ophedwa komanso ogwidwa,Ndiponso mitu ya atsogoleri a adani.’ 43  Inu anthu a mitundu ina, sangalalani limodzi ndi anthu ake,+Chifukwa adzabwezera magazi a atumiki ake,+Ndipo adzabwezera chilango kwa adani ake,+Komanso adzaphimba machimo a dziko la anthu ake.”* 44  Ndiyeno Mose anabwera nʼkulankhula mawu onse a nyimbo iyi anthu onse akumva,+ iye pamodzi ndi Hoshiya*+ mwana wa Nuni. 45  Mose atamaliza kulankhula mawu onsewa kwa Aisiraeli onse, 46  anawauza kuti: “Ganizirani mofatsa mawu onse okuchenjezani amene ndikulankhula nanu lero,+ kuti muuze ana anu kuti azionetsetsa kuti akuchita zimene mawu onse a Chilamulo ichi akunena.+ 47  Chifukwa amenewa si mawu opanda pake kwa inu, koma angakuthandizeni kukhala ndi moyo.+ Mukamatsatira mawu amenewa mudzakhala ndi moyo wautali mʼdziko limene mukuwoloka Yorodano kuti mukalitenge kukhala lanu.” 48  Yehova analankhula ndi Mose pa tsiku lomweli kuti: 49  “Kwera mʼphiri ili la Abarimu,+ phiri la Nebo,+ limene lili mʼdziko la Mowabu, moyangʼanizana ndi Yeriko, ndipo uone dziko la Kanani limene ndikupereka kwa Aisiraeli kuti likhale lawo.+ 50  Kenako ukafera paphiri limene ukufuna kukwerali nʼkuikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ako,* mofanana ndi Aroni mʼbale wako amene anafera paphiri la Hora+ nʼkuikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ake. 51  Izi zili choncho chifukwa awirinu simunakhale okhulupirika kwa ine pakati pa Aisiraeli kumadzi a pa Meriba+ ku Kadesi, mʼchipululu cha Zini, chifukwa simunandilemekeze pamaso pa Aisiraeli.+ 52  Iwe udzaona dzikolo uli patali, koma sudzalowa mʼdziko limene ndikupereka kwa Aisiraeli.”+

Mawu a M'munsi

^ Mabaibulo ena amati, “mitundu ya anthu.”
^ Apa akunena Yakobo.
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mafuta a nkhosa zamphongo.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mafuta apaimpso a tirigu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “madzi a zipatso za mphesa.”
^ Kutanthauza “Wolungama.” Limeneli ndi dzina laulemu la Isiraeli.
^ Kapena kuti, “anandichititsa nsanje.”
^ Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Mabaibulo ena amati, “wosafuna kumva malangizo.”
^ Kapena kuti, “imene inkadya nsembe zawo zabwino kwambiri.”
^ Kapena kuti, “adzayeretsa dziko la anthu ake.”
^ Dzina lakale la Yoswa. Hoshiya ndi chidule cha dzina lakuti Hoshaiya limene limatanthauza kuti, “Wopulumutsidwa ndi Ya; Ya Wapulumutsa.”
^ Awa ndi mawu okuluwika otanthauza imfa.