Kwa Agalatiya 6:1-18

  • Muzinyamulirana zinthu zolemera (1-10)

    • Timakolola zimene tafesa (7, 8)

  • Mdulidwe wopanda phindu (11-16)

    • Kulengedwa mwatsopano (15)

  • Mawu omaliza (17, 18)

6  Abale, ngati munthu wapatuka nʼkuyamba kulowera njira yolakwika mosazindikira, inu amene ndi oyenerera mwauzimu, yesani kuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.+ Koma pamene mukuchita zimenezi musamale,+ kuopera kuti inunso mungayesedwe.+  Pitirizani kunyamulirana zinthu zolemera.+ Mukamachita zimenezi mudzakhala mukukwaniritsa chilamulo cha Khristu.+  Chifukwa ngati wina akudziona kuti ndi wofunika pamene si wotero,+ akudzinamiza yekha.  Koma aliyense payekha ayese zochita zake kuti aone kuti ndi zotani.+ Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi zimene akuchitazo, osati modziyerekezera ndi munthu wina.+  Chifukwa aliyense ayenera kunyamula katundu wake.*+  Komanso, aliyense amene akuphunzitsidwa mawuwo agawane zinthu zonse zabwino ndi amene akumuphunzitsayo.+  Musadzinamize, Mulungu sapusitsika. Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.+  Chifukwa amene akufesa nʼcholinga chopindulitsa thupi lake, adzakolola chiwonongeko kuchokera mʼthupi lakelo, koma amene akutsatira mzimu wa Mulungu adzakolola moyo wosatha kuchokera ku mzimuwo.+  Choncho tisasiye kuchita zabwino, chifukwa pa nthawi yake tidzakolola tikapanda kutopa.*+ 10  Ndiye ngati tingathe, tiyeni tichitire onse zabwino, koma makamaka abale ndi alongo athu mʼchikhulupiriro. 11  Taonani zilembo zikuluzikulu zimene ndakulemberani ndi dzanja langali. 12  Onse amene akufuna kuti azioneka ngati abwino pamaso pa anthu ndi amene akukuumirizani kuti mudulidwe. Iwo akuchita zimenezi kuti asazunzidwe chifukwa cha mtengo wozunzikirapo* wa Khristu. 13  Chifukwa ngakhale amene akudulidwawo sikuti amasunga Chilamulo,+ koma akufuna kuti inuyo mudulidwe nʼcholinga choti azidzitama chifukwa cha zimene zachitika pathupi lanu. 14  Ineyo sindikufuna kudzitama pa chifukwa china chilichonse, kupatulapo chifukwa cha mtengo wozunzikirapo* wa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ Kwa ine, dziko linaweruzidwa kuti liphedwe* kudzera mwa iye, koma malinga nʼkuona kwa dzikoli, ineyo ndinaweruzidwa kuti ndiphedwe kudzera mwa iye. 15  Chifukwa kudulidwa kapena kusadulidwa nʼkosafunika,+ koma chofunika ndi kukhala wolengedwa mwatsopano.+ 16  Koma onse amene amatsatira lamulo limeneli la mmene tiyenera kukhalira, amene ndi Isiraeli wa Mulungu,+ akhale ndi mtendere ndipo Mulungu awasonyeze chifundo. 17  Kuyambira tsopano, pasapezeke munthu wondivutitsa, chifukwa thupi langali lili ndi zidindo zosonyeza kuti ndine kapolo wa Yesu.+ 18  Abale, kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu kukhale nanu chifukwa cha mzimu umene mumasonyeza. Ame.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “katundu yemwe ndi udindo wake.”
Kapena kuti, “kusiya.”
Kapena kuti, “lipachikidwe pamtengo.”