Esitere 3:1-15

  • Hamani anakwezedwa ndi mfumu (1-4)

  • Hamani anakonza chiwembu chopha Ayuda (5-15)

3  Kenako Mfumu Ahasiwero anakweza pa udindo Hamani+ mwana wa Hamedata mbadwa ya Agagi,+ ndipo anamupatsa mpando wapamwamba kuposa akalonga ena onse a mfumuyo.+ 2  Choncho atumiki onse a mfumu amene ankakhala pageti la mfumu ankaweramira Hamani ndiponso kumugwadira chifukwa mfumu ndi imene inalamula kuti azimuchitira zimenezi. Koma Moredikayi ankakana kumuweramira kapena kumugwadira. 3  Choncho atumiki a mfumu amene ankakhala pagetiwo anafunsa Moredikayi kuti: “Nʼchifukwa chiyani sukutsatira lamulo la mfumu?” 4  Ankamufunsa zimenezi tsiku ndi tsiku koma iye sankawamvera. Kenako anthuwo anauza Hamani kuti aone ngati khalidwe la Moredikayi lingalekereredwe+ popeza iye anali atawauza kuti anali Myuda.+ 5  Hamani ataona kuti Moredikayi sankamuweramira ndiponso kumugwadira, anakwiya kwambiri.+ 6  Koma Hamani anaona kuti nʼzosakwanira kupha Moredikayi yekha chifukwa anthu anali atamuuza za anthu a mtundu wa Moredikayi. Choncho Hamani anaganiza zoti aphe Ayuda onse, anthu a mtundu wa Moredikayi mʼmadera onse amene Ahasiwero ankalamulira. 7  Ndiyeno mʼmwezi woyamba, umene ndi mwezi wa Nisani,* mʼchaka cha 12+ cha Mfumu Ahasiwero, anthu anachita Puri+ kapena kuti maere pamaso pa Hamani kuti adziwe tsiku ndi mwezi woyenerera. Maerewo anagwera mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara.*+ 8  Kenako Hamani anauza Mfumu Ahasiwero kuti: “Pali mtundu wina wa anthu+ umene ukupezeka paliponse mʼzigawo zonse za ufumu wanu.+ Malamulo awo ndi osiyana ndi malamulo a anthu ena onse ndipo sakutsatira malamulo anu. Choncho ngati mungawasiye anthu amenewa, zinthu sizikuyenderani bwino mfumu. 9  Ngati mungakonde mfumu, palembedwe lamulo loti anthu amenewa aphedwe. Ine ndidzapereka ndalama zokwana matalente* 10,000 asiliva kwa akuluakulu ogwira ntchito kunyumba ya mfumu kuti akaziike mosungiramo chuma cha mfumu.”* 10  Zitatero mfumu inavula mphete yake yodindira+ nʼkuipereka kwa Hamani+ mwana wa Hamedata, mbadwa ya Agagi,+ yemwe ankadana kwambiri ndi Ayuda. 11  Ndiyeno mfumu inauza Hamani kuti: “Siliva* komanso anthuwo ndakupatsa ndipo uchite nawo zilizonse zimene ukufuna.” 12  Kenako pa tsiku la 13 la mwezi woyamba, alembi a mfumu+ anaitanidwa. Ndipo alembiwo analemba+ zonse zimene Hamani analamula masatarapi* a mfumu, abwanamkubwa a mʼzigawo zosiyanasiyana ndiponso akalonga a anthu osiyanasiyana. Chigawo chilichonse anachilembera mogwirizana ndi kalembedwe ka anthu a kumeneko ndiponso chilankhulo chawo. Makalatawa anawalemba mʼdzina la Mfumu Ahasiwero ndipo anawadinda ndi mphete yodindira ya mfumuyo.+ 13  Makalatawo anawatumiza kuzigawo zonse za mfumu kudzera mwa anthu operekera makalata. Anachita izi kuti tsiku limodzi, tsiku la 13 la mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara,+ aphe Ayuda onse, kaya ndi achinyamata, amuna achikulire, ana ndiponso akazi nʼkutenga zinthu zawo.+ 14  Lamulo lopita kuzigawo zonse, limene analilemba mʼmakalatawo, linafalitsidwa kwa anthu a mitundu yonse kuti akonzekere tsiku limeneli. 15  Mfumu inalamula kuti operekera makalatawo apite mwamsanga.+ Lamuloli linaperekedwa mʼnyumba ya mfumu ya ku Susani*+ yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. Kenako mfumu ndi Hamani, anakhala pansi nʼkumamwa vinyo, koma mumzinda wa Susani munali chipwirikiti.

Mawu a M'munsi

^ Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.
^ Mabaibulo ena amati, “Ine ndidzapereka ndalama zokwana matalente 10,000 asiliva kuti akaziike mosungiramo chuma cha mfumu zoti zipite kwa anthu amene adzagwire ntchitoyi.”
^ Nʼkutheka kuti amanena za siliva amene akatenge akakapha Ayuda.
^ Limeneli ndi dzina laudindo la anthu oteteza ufumu.
^ Kapena kuti, “Susa.”