Zekariya 1:1-21

  • Kuuza anthu kuti abwerere kwa Yehova (1-6)

    • ‘Bwererani kwa ine ndipo ine ndidzabwerera kwa inu’ (3)

  • Masomphenya Oyamba: Okwera pamahatchi ataima pamitengo ya mchisu (7-17)

    • “Yehova adzalimbikitsanso Ziyoni” (17)

  • Masomphenya Achiwiri: Nyanga 4 ndi amisiri 4 (18-21)

1  Mʼmwezi wa 8, mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo,+ Yehova analankhula ndi mneneri Zekariya*+ mwana wa Berekiya, mwana wa Ido, kuti: 2  “Yehova anakwiyira kwambiri makolo anu.+ 3  Uwauze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Bwererani kwa ine,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, “ndipo ine ndidzabwerera kwa inu,”+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.’” 4  “‘Musakhale ngati makolo anu amene aneneri akale anawauza kuti: “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Chonde, siyani njira zanu zoipa ndiponso zochita zanu zoipa.’”’+ ‘Koma iwo sanamvere ndipo sanatsatire mawu anga,’+ watero Yehova. 5  ‘Kodi makolo anuwo ali kuti pano? Ndipo “kodi aneneriwo anakhalabe ndi moyo mpaka kalekale?” 6  Ndinauza makolo anu malamulo oti azitsatira ndipo ndinatumiza atumiki anga aneneri kuti akawachenjeze zimene zidzawachitikire ngati sangatsatire malamulowo. Kodi zonse zimene ndinanena kuti zidzawachitikirazo sizinawachitikire?’+ Choncho iwo anabwerera kwa ine nʼkunena kuti: ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba watichitira zimene anakonza mogwirizana ndi njira zathu ndi zochita zathu.’”+ 7  Pa tsiku la 24 la mwezi wa 11 womwe ndi mwezi wa Sebati,* mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo,+ Yehova analankhula ndi mneneri Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido. Anamuuza kuti anene kuti: 8  “Ndinaona masomphenya usiku. Ndinaona munthu atakwera pahatchi* yomwe inaima pakati pa mitengo ya mchisu imene inali mʼchigwa. Kumbuyo kwake kunali mahatchi ofiira kwambiri, ofiirira ndi oyera.”* 9  Choncho ndinafunsa kuti: “Kodi amenewa ndi ndani mbuyanga?” Mngelo amene ankalankhula nane anandiyankha kuti: “Ndikuuza kuti amenewa ndi ndani.” 10  Kenako munthu amene anaima pakati pa mitengo ya mchisu uja anati: “Amenewa atumizidwa ndi Yehova kuti ayendeyende padziko lapansi.” 11  Ndiyeno iwo anauza mngelo wa Yehova amene anaima pakati pa mitengo ya mchisu uja kuti: “Ife tayendayenda padziko lonse lapansi ndipo taona kuti pali bata komanso palibe chosokoneza.”+ 12  Choncho mngelo wa Yehova anati: “Inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, kodi Yerusalemu ndiponso mizinda ya Yuda+ imene munaikwiyira kwa zaka 70 zimenezi,+ simuichitira chifundo mpaka liti?” 13  Yehova anayankha mngelo amene ankalankhula nane uja mokoma mtima komanso ndi mawu olimbikitsa. 14  Ndiyeno mngelo amene ankalankhula nane uja anandiuza kuti: “Fuula kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Ndatsimikiza mtima kuti nditeteze Yerusalemu ndi Ziyoni.+ 15  Ndakwiyira kwambiri anthu a mitundu ina amene akukhala mosatekeseka.+ Ndawakwiyira chifukwa chakuti ine ndinangokwiyira anthu anga pangʼono,+ koma anthu amenewa anakulitsa kwambiri mavuto a anthu angawo.”’+ 16  Choncho Yehova wanena kuti, ‘“Ndidzabwerera ku Yerusalemu nʼkuchitira chifundo mzinda umenewu+ ndipo nyumba yanga idzamangidwa mumzindawu.+ Chingwe choyezera chidzatambasulidwa pa Yerusalemu,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.’ 17  Fuulanso kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Mizinda yanga idzasefukiranso ndi zinthu zabwino. Yehova adzalimbikitsanso Ziyoni+ ndipo adzasankhanso Yerusalemu.”’”+ 18  Kenako nditakweza maso, ndinaona nyanga 4.+ 19  Choncho ndinafunsa mngelo amene ankalankhula nane uja kuti: “Kodi nyangazi zikuimira chiyani?” Iye anandiyankha kuti: “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda,+ Isiraeli+ ndi Yerusalemu.”+ 20  Kenako Yehova anandionetsa amisiri 4. 21  Ndiyeno ndinafunsa kuti: “Kodi awa abwera kudzatani?” Mngeloyo anayankha kuti: “Zimenezi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda moti panalibe amene anatha kudzutsa mutu wake. Amisiriwa adzabwera kudzaopseza nyangazi ndipo adzawononga nyanga za mitundu ina ya anthu amene anakweza nyanga* zawo poukira dziko la Yuda kuti abalalitse anthu ake.”

Mawu a M'munsi

^ Kutanthauza “Yehova Wakumbukira.”
^ Ena amati “hosi.”
^ Nʼkuthekanso kuti panali hatchi yofiira kwambiri, yofiirira ndi yoyera.
^ Kapena kuti, “mphamvu.”