Zekariya 11:1-17

  • Zotsatira za kukana mʼbusa weniweni wa Mulungu (1-17)

    • “Weta nkhosa zimene zinayenera kuphedwa” (4)

    • Ndodo ziwiri: Wosangalatsa komanso Mgwirizano (7)

    • Malipiro a mʼbusa: Ndalama 30 zasiliva (12)

    • Ndalama zinaponyedwa mosungira chuma (13)

11  “Iwe Lebanoni, tsegula zitseko zako,Kuti moto uwotcheretu mitengo yako ya mkungudza.  2  Lira mofuula, iwe mtengo wa junipa,* chifukwa mtengo wa mkungudza wagwa.Mitengo ikuluikulu yawonongedwa. Lirani mofuula, inu mitengo ya thundu* ya ku Basana,Chifukwa nkhalango yowirira kwambiri ija yawonongedwa.  3  Tamverani! Abusa akulira mofuula,Chifukwa ulemerero wawo watha. Tamverani! Mikango yamphamvu ikubangula,Chifukwa nkhalango zowirira za mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodano zawonongedwa. 4  Yehova Mulungu wanga wanena kuti, ‘Weta nkhosa zimene zinayenera kuphedwa.+ 5  Amene anazigula amazipha,+ koma saimbidwa mlandu. Amene akuzigulitsa+ akunena kuti: “Yehova atamandike chifukwa ndilemera.” Ndipo abusa ake sazichitira chifundo.’+ 6  ‘Sindidzachitiranso chifundo anthu okhala mʼdzikoli,’ watero Yehova. ‘Choncho ine ndidzachititsa kuti aliyense aziponderezedwa ndi mnzake ndiponso mfumu yake. Iwo adzawononga dzikoli, ndipo ine sindidzawapulumutsa mʼmanja mwawo.’” 7  Ine ndinayamba kuweta nkhosa zimene zinayenera kuphedwa+ ndipo ndinachita zimenezi chifukwa cha inu, anthu ovutika a mʼgulu la nkhosali. Choncho ndinatenga ndodo ziwiri. Ina ndinaipatsa dzina lakuti Wosangalatsa ndipo inayo ndinaipatsa dzina lakuti Mgwirizano.+ Ndiyeno ndinayamba kuweta gulu la nkhosalo. 8  Ndinachotsa abusa atatu mʼmwezi umodzi chifukwa sindinathenso kuwalezera mtima ndipo iwonso ananyansidwa nane. 9  Ndipo ndinanena kuti: “Sindikuwetaninso. Amene akufa afe ndipo amene akuwonongeka, awonongeke. Otsalawo adyane.” 10  Choncho ndinatenga ndodo yanga yotchedwa Wosangalatsa+ ija nʼkuiduladula. Ndinachita izi kuti ndithetse pangano limene ndinachita ndi anthu a mtundu wanga. 11  Panganolo linaswedwa tsiku limenelo ndipo nkhosa zovutika zimene zinaona ndikuchita zimenezi, zinadziwa kuti zimene ndachitazo nʼzimene Yehova ananena. 12  Kenako ndinawauza kuti: “Ngati mukuona kuti nʼzoyenera, ndipatseni malipiro anga. Koma ngati mukuona kuti nʼzosayenera musandipatse.” Iwo anandilipira* ndalama 30 zasiliva.+ 13  Kenako Yehova anandiuza kuti: “Kaziponye mosungiramo chuma. Zimenezi ndi ndalama zochepa zimene aona kuti angandilipire.”+ Choncho ndinatenga ndalama 30 zasilivazo nʼkukaziponya mosungiramo chuma panyumba ya Yehova.+ 14  Kenako ndinathyola ndodo yanga yachiwiri ija yotchedwa Mgwirizano,+ pothetsa ubale wa Yuda ndi Isiraeli.+ 15  Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: “Tenga zida za mʼbusa wopanda pake.+ 16  Chifukwa ndilola kuti mʼdzikoli mukhale mʼbusa wina. Mʼbusa ameneyu sadzasamalira nkhosa zimene zikuwonongeka.+ Iye sadzafunafuna nkhosa yaingʼono, sadzachiritsa yovulala+ komanso sadzapatsa chakudya nkhosa zimene zikadali zamphamvu. Mʼmalomwake adzadya nyama ya nkhosa yonenepa+ ndipo adzakupula* ziboda za nkhosazo.+ 17  Tsoka kwa mʼbusa wanga wopanda pake+ amene akusiya nkhosa.+ Lupanga lidzamutema padzanja ndi diso lake lakumanja. Dzanja lake lidzalumala kwambiri,Ndipo diso lake lamanja lidzachita khungu.”*

Mawu a M'munsi

^ Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.
^ Ena amati, “nthundu.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anandiyezera.”
^ Ena amati, “kusupula.”
^ Kapena kuti, “lidzachita mdima.”