Zekariya 9:1-17

  • Mulungu adzaweruza anthu a mitundu ina (1-8)

  • Kubwera kwa mfumu ya Ziyoni (9, 10)

    • Mfumu yodzichepetsa inakwera bulu (9)

  • Anthu a Yehova adzamasulidwa (11-17)

9  Uthenga wokhudza dziko la Hadiraki: “Uwu ndi uthenga wa Yehova wokhudza dziko la Hadiraki,Ndipo makamaka ukupita kumzinda wa Damasiko.+Chifukwa maso a Yehova ali pa anthu,+Komanso pa mafuko onse a Isiraeli.  2  Uthengawu ukupitanso kwa Hamati+ amene anachita naye malire.Komanso kwa Turo+ ndi Sidoni+ chifukwa ali ndi nzeru zambiri.+  3  Turo anamanga malo okwera omenyerapo nkhondo. Anadziunjikira siliva wambiri ngati fumbi,Ndiponso golide wambiri ngati dothi lamʼmisewu.+  4  Yehova adzamulanda zinthu zake.Gulu lake lankhondo adzaliponyera mʼnyanja.+Ndipo iye adzatenthedwa ndi moto.+  5  Asikeloni adzaona zimenezi ndipo adzachita mantha.Gaza adzamva ululu waukulu.Izi zidzachitikiranso Ekironi chifukwa amene ankamudalira wachititsidwa manyazi. Ku Gaza sikudzakhalanso mfumu,Ndipo ku Asikeloni sikudzakhalanso anthu.+  6  Mwana wochokera mu mtundu wina wa anthu azidzakhala ku Asidodi,Ndipo ndidzathetsa kunyada kwa Afilisiti.+  7  Ndidzachotsa zinthu zamagazi mʼkamwa mwawo,Komanso chakudya chonyansa pakati pa mano awo.Ndipo aliyense amene adzatsale, adzakhala wa Mulungu wathu.Iye adzakhala ngati mtsogoleri mu Yuda,+Ndipo Ekironi adzakhala ngati munthu wa Chiyebusi.+  8  Ndidzamanga msasa kunja kwa nyumba yanga kuti ndizidzailondera,+Moti sipadzakhala munthu wolowa kapena kutuluka.Aliyense amene ankawagwiritsa ntchito* sadzadutsanso pakati pawo+Chifukwa ine ndaona ndi maso anga.*  9  Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni* sangalala kwambiri. Fuula mokondwera iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu.* Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe.+ Mfumuyo ndi yolungama ndipo ikubweretsa chipulumutso.*Ndi yodzichepetsa+ ndipo ikubwera itakwera bulu.Ikubwera itakwera mwana wamphongo wa bulu.+ 10  Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku EfuraimuNdiponso mahatchi ku Yerusalemu. Mauta omenyera nkhondo adzachotsedwa. Mfumuyo idzalalikira uthenga wamtendere kwa anthu a mitundu ina.+Ulamuliro wake udzayambira kunyanja mpaka kukafika kunyanja ina.Ndiponso kuchokera ku Mtsinje* mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+ 11  Koma mkazi iwe, chifukwa cha magazi a pangano limene unapangana ndi ine,Ndidzatulutsa akaidi ako mʼdzenje lopanda madzi.+ 12  Inu akaidi amene muli ndi chiyembekezo, bwererani kumalo a chitetezo champhamvu.+ Lero ndikukuuza kuti,‘Mkazi iwe, ndidzakupatsa magawo awiri a madalitso.+ 13  Ndidzapinda Yuda kuti akhale uta wanga. Efuraimu ndidzamuika pa uta umenewo ngati muvi.Ndidzadzutsa ana ako, iwe Ziyoni,Kuti aukire ana a Girisi.Ndipo ndidzakusandutsa lupanga la msilikali.’ 14  Zidzakhala zoonekeratu kuti Yehova ali ndi anthu ake,Ndipo muvi wake udzathamanga ngati mphezi. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa adzaliza lipenga,+Ndipo adzapita ndi mphepo yamkuntho yakumʼmwera. 15  Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzateteza anthu ake.Adani awo adzawaponyera miyala ndi gulaye,* koma iwo adzawagonjetsa.+ Iwo adzasangalala ndipo adzafuula ngati amwa vinyo.Adzakhala ngati mbale zolowa zodzaza vinyo,Ndiponso ngati magazi amene athiridwa mʼmakona a guwa lansembe.+ 16  Pa tsiku limenelo, Yehova Mulungu adzapulumutsa nkhosa zake,Zomwe ndi anthu ake.+Popeza iwo adzakhala ngati miyala yamtengo wapatali yapachisoti chachifumu yomwe ikunyezimira mʼdziko lake.+ 17  Ubwino wake ndi waukulu kwambiri,+Ndiponso iye ndi wooneka bwino kwambiri. Tirigu adzapatsa mphamvu anyamata,Ndipo vinyo watsopano adzapatsa mphamvu anamwali.”+

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “amene ankawapondereza.”
^ Mwina kutanthauza kuvutika kwa anthu ake.
^ Kapena kuti, “yapambana; yapulumutsidwa.”
^ Mawu akuti “mwana wamkazi wa Yerusalemu” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
^ Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
^ Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
^ Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala chimene amachita kupukusa ndi dzanja.