Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto 10:1-33
10 Tsopano abale, ndikufuna mudziwe kuti makolo athu akale, onse anali pansi pa mtambo+ ndipo onse anawoloka nyanja.+
2 Onse anabatizidwa mwa Mose, kudzera mu mtambo ndi nyanja.
3 Onse ankadya chakudya chauzimu chofanana.+
4 Ndipo onse ankamwa madzi auzimu ofanana.+ Chifukwa ankamwa pathanthwe lauzimu limene linkawatsatira, ndipo thanthwelo linali* Khristu.+
5 Ngakhale zinali choncho, ambiri a iwo Mulungu sanakondwere nawo ndipo anaphedwa mʼchipululu.+
6 Zinthu zimenezi ndi zitsanzo kwa ife, kuti nafenso tisamalakelake zinthu zoipa ngati mmene iwo anachitira.+
7 Ndipo tisamalambire mafano ngati mmene ena a iwo anachitira, mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Anthu anakhala pansi ndipo anadya ndi kumwa. Kenako anaimirira nʼkuyamba kusangalala.”+
8 Komanso tisamachite chiwerewere,* mmene ena a iwo anachitira, nʼkufa anthu 23,000 tsiku limodzi.+
9 Tisamamuyesenso Yehova,* mmene ena a iwo anamuyesera,+ nʼkufa atalumidwa ndi njoka.+
10 Tisakhalenso ongʼungʼudza, ngati mmene ena a iwo anachitira,+ nʼkuphedwa ndi mngelo wowononga.+
11 Zinthu zimene zinawachitikirazi ndi zitsanzo kwa ife ndipo zinalembedwa kuti zitichenjeze ifeyo+ amene tikukhala kumapeto a nthawi ino.
12 Choncho amene akuganiza kuti waima bwinobwino asamale kuti asagwe.+
13 Palibe mayesero amene mwakumana nawo osiyana ndi amene anthu ena amakumana nawo.+ Koma Mulungu ndi wokhulupirika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire,+ koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.+
14 Choncho okondedwa anga, pewani* kulambira mafano.+
15 Ndikulankhula nanu ngati anthu ozindikira. Weruzani nokha ngati zimene ndikunenazi nʼzoona.
16 Kodi kapu ya madalitso imene timadalitsa, sitanthauza kugawana magazi a Khristu?+ Kodi mkate umene timaugawagawa, sutanthauza kugawana thupi la Khristu?+
17 Popeza pali mkate umodzi, ifeyo, ngakhale kuti tilipo ambiri, ndife thupi limodzi,+ chifukwa tonse tikudya nawo mkate umodziwo.
18 Taganizirani zimene Aisiraeli* amachita: Kodi amene amadya zinthu zoperekedwa paguwa la nsembe si ndiye kuti amakhala ngati akudya ndi Mulungu?+
19 Kodi mfundo yake ndi yotani? Kodi zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano kapena mafano enieniwo ndi kanthu?
20 Ayi, koma ndikutanthauza kuti zinthu zimene anthu a mitundu ina amapereka nsembe amazipereka kwa ziwanda, osati kwa Mulungu.+ Ndipo sindikufuna kuti muzichita chilichonse chogwirizana ndi ziwanda.+
21 Sizingatheke kuti muzimwa zamʼkapu ya Yehova* komanso zamʼkapu ya ziwanda. Sizingathekenso kuti muzidya “patebulo la Yehova”*+ komanso patebulo la ziwanda.
22 Kapena ‘kodi tikufuna kuti Yehova* achite nsanje?’+ Kodi mphamvu zathu zingapose mphamvu zake?
23 Zinthu zonse nʼzololeka, koma si zonse zimene zili zaphindu. Zinthu zonse nʼzololeka, koma si zonse zomwe zimalimbikitsa.+
24 Aliyense asamangofuna zopindulitsa iyeyo basi, koma zopindulitsanso ena.+
25 Muzidya chilichonse chogulitsidwa pamsika wa nyama muli ndi chikumbumtima chabwino ndipo musafunse mafunso.
26 Chifukwa “dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo ndi za Yehova.”*+
27 Ngati munthu wosakhulupirira wakuitanani ndipo mukufuna kupita, kadyeni chilichonse chimene wakupatsani muli ndi chikumbumtima chabwino ndipo musafunse mafunso.
28 Koma wina akakuuzani kuti: “Izi zaperekedwa nsembe,” musadye zimenezo kuopera amene wakuuzaniyo ndiponso chikumbumtima.+
29 Sindikunena chikumbumtima chako, koma cha munthu winayo. Sindikufuna kuti ndizigwiritsa ntchito ufulu wanga kenako nʼkumaweruzidwa ndi chikumbumtima cha munthu wina.+
30 Ngakhale nditakhala ndi ufulu wodya chakudyacho nʼkuyamika Mulungu, kodi ndi bwino kuchita zimenezo ngati zingachititse kuti anthu ena andinyoze?+
31 Choncho kaya mukudya kapena kumwa, kapena kuchita china chilichonse, muzichita zinthu zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.+
32 Muzipewa kukhumudwitsa Ayuda, Agiriki ndiponso mpingo wa Mulungu.+
33 Zimenezi ndi zimene inenso ndikuyesetsa kuchita. Ndikuyesetsa kusangalatsa anthu onse pa zonse zimene ndikuchita. Sindikufuna zopindulitsa ine ndekha,+ koma zopindulitsa anthu ambiri kuti apulumutsidwe.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “linkatanthauza.”
^ MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Kapena kuti, “thawani.”
^ Kapena kuti, “Aisiraeli akuthupi.”
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.
^ Onani Zakumapeto A5.