Kalata Yoyamba ya Yohane 5:1-21

  • Amene amakhulupirira Yesu amagonjetsa dziko (1-12)

    • Tanthauzo la kukonda Mulungu (3)

  • Tizikhulupirira kuti pemphero ndi lamphamvu (13-17)

  • Tizisamala mʼdziko loipali (18-21)

    • Dziko lonse lili mʼmanja mwa woipayo (19)

5  Aliyense amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Khristu, ndi mwana wa Mulungu.+ Ndipo onse amene amakonda Atate amakondanso mwana wake.  Timakonda Mulungu komanso kutsatira malamulo ake. Tikamachita zimenezi timadziwa kuti tikukondanso ana a Mulungu.+  Kukonda Mulungu kumatanthauza kutsatira malamulo ake,+ ndipo malamulo akewo si ovuta kuwatsatira.+  Aliyense amene ndi mwana wa Mulungu amagonjetsa dziko.+ Ndipo chikhulupiriro chathu chatithandiza kugonjetsa dziko.+  Kodi ndi ndani amene angagonjetse dziko?+ Kodi si amene amakhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu?+  Pamene Yesu Khristu ankabwera panali madzi komanso magazi. Sikuti panali madzi okha,+ koma panalinso magazi.+ Ndipo mzimu woyera ukuchitira umboni zimenezi,+ chifukwa mzimuwo umabweretsa choonadi poyera.  Pali zinthu zitatu zimene zimatithandiza kumudziwa bwino Yesu Khristu.  Zinthu zake ndi mzimu,+ madzi+ komanso magazi,+ ndipo umboni wa zinthu zitatuzi ndi wogwirizana.  Nʼzoona kuti timakhulupirira umboni umene anthu amapereka, komatu umboni umene Mulungu amapereka ndi woposa umboni umenewo. Choncho timakhulupirira umboni umene Mulungu amapereka wokhudza Mwana wake. 10  Munthu amene amakhulupirira Mwana wa Mulungu amavomereza mumtima mwake umboni umene Mulungu wamupatsa. Munthu amene sakhulupirira Mulungu amamupangitsa kuoneka ngati wabodza,+ chifukwa sakhulupirira umboni umene Mulungu anapereka wokhudza Mwana wake. 11  Umboni umene Mulungu anapereka ndi wakuti, iye anatipatsa moyo wosatha+ kudzera mwa Mwana wake.+ 12  Munthu amene wavomereza Mwana ndiye kuti ali ndi moyo umenewu. Ndipo amene sanavomereze Mwana wa Mulungu alibe moyo umenewu.+ 13  Ndikukulemberani zimenezi kuti mudziwe zoti inu amene mumakhulupirira Mwana wa Mulungu*+ mudzapeza moyo wosatha.+ 14  Ndipotu ife sitikayikira*+ kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi zimene amafuna, amatimvera.+ 15  Komanso, popeza timadziwa kuti amatimvera tikapempha chilichonse, timakhala ndi chikhulupiriro kuti tilandira zinthu zimene tamupemphazo.+ 16  Ngati wina waona mʼbale wake akuchita tchimo lomwe silingabweretse imfa, amupempherere ndipo Mulungu adzamupatsa moyo.+ Pamenepa ndikunena za anthu omwe achita tchimo limene silingabweretse imfa. Komabe pali tchimo lomwe limabweretsa imfa+ ndipo sindikunena kuti apempherere munthu amene wachita tchimo ngati limeneli. 17  Kuchita chilichonse chosalungama ndi tchimo.+ Komabe pali tchimo lomwe silingabweretse imfa. 18  Tikudziwa kuti munthu aliyense yemwe ndi mwana wa Mulungu alibe chizolowezi chochita tchimo, koma mwana* wa Mulungu amamuyangʼanira ndipo woipayo sangamugwire.+ 19  Tikudziwa kuti ndife anthu a Mulungu, koma dziko lonse lili mʼmanja mwa woipayo.*+ 20  Komabe, tikudziwa kuti Mwana wa Mulungu anabwera padzikoli+ ndipo anatipatsa nzeru kuti tidziwe Mulungu woona. Kudzera mwa Mwana wake Yesu Khristu, ndife ogwirizana naye.+ Iyeyo ndi Mulungu woona ndipo amapereka moyo wosatha.+ 21  Ana anga okondedwa, muzipewa mafano.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “mumakhulupirira mʼdzina la Mwana wa Mulungu.”
Kapena kuti, “ife tili ndi ufulu wakulankhula.”
“Mwana” ameneyu ndi Yesu Khristu.
Yemwe ndi Satana.