Ezara 2:1-70

  • Anthu amene anabwerera kuchokera ku ukapolo (1-67)

    • Atumiki a pakachisi (43-54)

    • Ana a atumiki a Solomo (55-57)

  • Zopereka zaufulu pakachisi (68-70)

2  Awa ndi anthu amʼchigawo* amene anatuluka mu ukapolo+ pa anthu omwe Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anawatengera ku Babulo.+ Anthuwa anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense kumzinda wakwawo.+ 2  Amenewa anabwera pamodzi ndi Zerubabele,+ Yesuwa,*+ Nehemiya, Seraya, Reelaya, Moredikayi, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Bana. Chiwerengero cha amuna a Isiraeli chinali ichi:+ 3  Ana a Parosi, 2,172. 4  Ana a Sefatiya, 372. 5  Ana a Ara,+ 775. 6  Ana a Pahati-mowabu,+ ochokera mwa ana a Yesuwa ndi Yowabu, 2,812. 7  Ana a Elamu,+ 1,254. 8  Ana a Zatu,+ 945. 9  Ana a Zakai, 760. 10  Ana a Bani, 642. 11  Ana a Bebai, 623. 12  Ana a Azigadi, 1,222. 13  Ana a Adonikamu, 666. 14  Ana a Bigivai, 2,056. 15  Ana a Adini, 454. 16  Ana a Ateri, a mʼbanja la Hezekiya, 98. 17  Ana a Bezai, 323. 18  Ana a Yora, 112. 19  Ana a Hasumu,+ 223. 20  Ana a Gibara, 95. 21  Ana a Betelehemu, 123. 22  Amuna a ku Netofa, 56. 23  Amuna a ku Anatoti,+ 128. 24  Ana a Azimaveti, 42. 25  Ana a Kiriyati-yearimu, Kefira ndi Beeroti, 743. 26  Ana a Rama+ ndi Geba,+ 621. 27  Amuna a ku Mikemasi, 122. 28  Amuna a ku Beteli ndi a ku Ai,+ 223. 29  Ana a Nebo,+ 52. 30  Ana a Magabisi, 156. 31  Ana a Elamu wina, 1,254. 32  Ana a Harimu, 320. 33  Ana a Lodi, Hadidi ndi Ono, 725. 34  Ana a Yeriko, 345. 35  Ana a Senaya, 3,630. 36  Ansembe:+ Ana a Yedaya,+ a mʼbanja la Yesuwa,+ 973. 37  Ana a Imeri,+ 1,052. 38  Ana a Pasuri,+ 1,247. 39  Ana a Harimu,+ 1,017. 40  Alevi:+ Ana a Yesuwa, a mʼbanja la Kadimiyeli+ ochokera pakati pa ana a Hodaviya, 74. 41  Oimba,+ ana a Asafu,+ 128. 42  Ana a alonda apageti:+ ana a Salumu, ana a Ateri, ana a Talimoni,+ ana a Akubu,+ ana a Hatita ndi ana a Sobai, onse analipo 139. 43  Atumiki apakachisi:*+ Ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti, 44  ana a Kerosi, ana a Siyaha, ana a Padoni, 45  ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Akubu, 46  ana a Hagabu, ana a Salimai, ana a Hanani, 47  ana a Gideli, ana a Gahara, ana a Reyaya, 48  ana a Rezini, ana a Nekoda, ana a Gazamu, 49  ana a Uziza, ana a Paseya, ana a Besai, 50  ana a Asena, ana a Meyuni, ana a Nefusimu, 51  ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri, 52  ana a Baziluti, ana a Mehida, ana a Harisa, 53  ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema, 54  ana a Neziya ndi ana a Hatifa. 55  Ana a atumiki a Solomo: Ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Peruda,+ 56  ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gideli, 57  ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-hazebaimu ndi ana a Ami. 58  Atumiki onse apakachisi* pamodzi ndi ana a atumiki a Solomo analipo 392. 59  Amene anachokera ku Tele-mela, Tele-harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, koma sanathe kufotokoza mzere wa makolo awo ndi kumene anachokera komanso kuti anali Aisiraeli kapena ayi, ndi awa:+ 60  ana a Delaya, ana a Tobia ndi ana a Nekoda, 652. 61  Ana a ansembe anali awa: ana a Habaya, ana a Hakozi,+ ana a Barizilai amene anatenga mkazi pakati pa ana aakazi a Barizilai+ wa ku Giliyadi nʼkuyamba kutchedwa ndi dzina lawo. 62  Amenewa ndi amene mayina awo anawayangʼana mʼkaundula kuti atsimikizire anthu onse za mzere wawo wobadwira koma sanapezekemo. Choncho anawaletsa kuti asatumikire ngati ansembe.*+ 63  Choncho, bwanamkubwa* anawauza kuti asamadye zinthu zopatulika koposa,+ mpaka patakhala wansembe amene angagwiritse ntchito Urimu ndi Tumimu.+ 64  Anthu onse analipo 42,360.+ 65  Apa sanawerengere akapolo awo aamuna ndi aakazi amene analipo 7,337. Iwo analinso ndi oimba aamuna ndi aakazi okwana 200. 66  Anali ndi mahatchi* 736 ndi nyulu* 245. 67  Ngamila zawo zinalipo 435 ndipo abulu awo analipo 6,720. 68  Atsogoleri ena a nyumba za makolo awo atafika kunyumba ya Yehova imene inali ku Yerusalemu, anapereka zopereka zaufulu+ kunyumba ya Mulungu woona kuti imangidwenso pamalo ake.+ 69  Mogwirizana ndi chuma chawo, anapereka zinthu zoti zithandize pa ntchitoyo. Anapereka madalakima* agolide 61,000, ma mina*+ asiliva 5,000 ndi mikanjo 100 ya ansembe. 70  Ndiyeno ansembe, Alevi, anthu ena, oimba, alonda apageti, atumiki apakachisi* ndi Aisiraeli onse anayamba kukhala mʼmizinda yawo.+

Mawu a M'munsi

^ Nʼkutheka kuti chinali chigawo cha ku Babulo kapena cha ku Yuda.
^ Nʼkutheka kuti akunena za “Yoswa” yemwe akutchulidwa pa Hag 1:1 ndi Zek 3:1.
^ Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”
^ Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”
^ Kapena kuti, “anawachotsa pa udindo wokhala ansembe chifukwa anali odetsedwa.”
^ Kapena kuti, “Tirisata.” Dzinali ndi la Chiperisiya la bwanamkubwa wachigawo.
^ Ena amati “mahosi.”
^ “Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.
^ “Dalakima” imeneyi inali yofanana ndi ndalama yagolide ya ku Perisiya yotchedwa dariki, yomwe inkalemera magalamu 8.4. Koma si yofanana ndi dalakima yomwe imatchulidwa mʼMalemba a Chigiriki. Onani Zakumapeto B14.
^ “Mina” yotchulidwa mʼMalemba a Chiheberi inkalemera magalamu 570. Onani Zakumapeto B14.
^ Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”