Danieli 2:1-49

  • Mfumu Nebukadinezara inalota maloto ochititsa mantha (1-4)

  • Anthu anzeru analephera kumasulira maloto (5-13)

  • Danieli anapempha Mulungu kuti amuthandize (14-18)

  • Anatamanda Mulungu chifukwa anawaululira chinsinsi (19-23)

  • Danieli anauza mfumu maloto ake (24-35)

  • Kumasulira maloto (36-45)

    • Mwala umene ukuimira Ufumu, unaphwanya chifaniziro (44, 45)

  • Danieli analemekezedwa ndi mfumu (46-49)

2  Mʼchaka chachiwiri cha ufumu wake, Nebukadinezara analota maloto angapo, moti anavutika maganizo+ ndipo tulo tinamuthera.  Choncho mfumuyo inalamula kuti aitane ansembe onse ochita zamatsenga, anthu olankhula ndi mizimu, Akasidi* ndi anthu ena ochita zamatsenga kuti adzauze mfumu maloto akewo. Anthu amenewa anafika nʼkuima pamaso pa mfumu.+  Ndiyeno mfumuyo inawauza kuti: “Ine ndalota maloto ndipo ndikuvutika maganizo kwambiri chifukwa ndikufuna kudziwa zimene ndalotazo.”  Akasidi anayankha mfumu mʼchinenero cha Chiaramu*+ kuti: “Inu mfumu mukhale ndi moyo mpaka kalekale. Tiuzeni ife atumiki anu zimene mwalota ndipo tikumasulirani malotowo.”  Mfumuyo inayankha Akasidiwo kuti: “Ndikukuuzani komaliza kuti: Ngati simundiuza zimene ndalota nʼkundimasulira, ndikudulani nthulinthuli ndipo nyumba zanu ndidzazisandutsa zimbudzi za anthu onse.*  Koma mukandiuza malotowo nʼkuwamasulira, ine ndikupatsani mphatso, mphoto ndi ulemerero waukulu.+ Choncho ndiuzeni malotowo ndipo muwamasulire.”  Iwo anayankha kachiwiri kuti: “Inu mfumu, tiuzeni ife atumiki anu zimene mwalota ndipo ife tikumasulirani malotowo.”  Ndiyeno mfumuyo inanena kuti: “Ine ndikudziwa kuti mukuzengereza dala kuti mukhale ndi nthawi yambiri yoganiza chifukwa mukudziwa kale zimene ndalamula.  Mukapanda kundiuza malotowo, chilango chimene nonsenu mulandire chikhala chofanana. Koma mwagwirizana kuti mundiuze zabodza komanso zachinyengo mpaka zinthu zitasintha. Ndiye ndiuzeni zimene ndalota ndipo mukatero, ndidziwa kuti mungathe kumasulira malotowo.” 10  Akasidiwo anayankha mfumuyo kuti: “Palibe munthu padziko lapansi amene angathe kuchita zimene inu mfumu mukufuna. Palibe mfumu yaikulu kapena bwanamkubwa amene anauzapo wansembe wochita zamatsenga, munthu wolankhula ndi mizimu kapena Mkasidi kuti achite zimenezi. 11  Zimene inu mfumu mukufuna kuti tichite ndi zovuta, ndipo palibe munthu amene angakuuzeni maloto anu kupatulapo milungu, imene sikhala pakati pa anthu.” 12  Mfumu itamva zimenezi inakwiya kwambiri ndipo inalamula kuti amuna onse anzeru a mʼBabulo aphedwe.+ 13  Lamulo limenelo litaperekedwa ndipo amuna anzeru atatsala pangʼono kuphedwa, anthu anayambanso kufunafuna Danieli ndi anzake kuti awaphe. 14  Pa nthawi imeneyo Danieli analankhula mwanzeru komanso mosamala kwambiri ndi Arioki mkulu wa asilikali olondera mfumu, amene anali atanyamuka kale kuti akaphe amuna anzeru a mʼBabulo. 15  Iye anafunsa Arioki mkulu wa asilikali olondera mfumu uja kuti: “Nʼchifukwa chiyani mfumu yapereka lamulo lokhwima chonchi?” Ndiyeno Arioki anafotokozera Danieli zonse zimene zinachitika.+ 16  Choncho Danieli anapita kwa mfumu kukapempha kuti imupatse nthawi kuti adzamasulire maloto ake. 17  Kenako Danieli anabwerera kunyumba kwake ndipo anauza anzake aja, Hananiya, Misayeli ndi Azariya za nkhani imeneyi. 18  Iye anawapempha kuti apemphere kwa Mulungu wakumwamba kuti awachitire chifundo nʼkuwaululira chinsinsi chimenechi, kuti Danieli ndi anzakewo asaphedwe limodzi ndi amuna ena onse anzeru a mʼBabulo. 19  Ndiyeno usiku, chinsinsicho chinaululidwa kwa Danieli mʼmasomphenya.+ Choncho Danieli anatamanda Mulungu wakumwamba. 20  Iye anati: “Dzina la Mulungu litamandike mpaka kalekale,*Chifukwa nzeru ndi mphamvu ndi zake.+ 21  Iye amasintha nthawi ndi nyengo,+Amachotsa mafumu komanso kuika mafumu,+Amapereka nzeru kwa anthu anzeru ndiponso amachititsa kuti anthu ozindikira adziwe zinthu.+ 22  Amaulula zinthu zozama ndi zinthu zobisika,+Amadziwa zinthu zimene zili mumdima,+Ndipo iye wazunguliridwa ndi kuwala.+ 23  Ndikukutamandani komanso kukuyamikani, inu Mulungu wa makolo anga,Chifukwa mwandipatsa nzeru ndi mphamvu. Ndipo tsopano mwandiuza zimene tinakupemphani,Mwatidziwitsa zinthu zimene mfumu ikuda nazo nkhawa.”+ 24  Kenako Danieli anapita kwa Arioki amene anatumidwa ndi mfumu kuti aphe amuna anzeru a ku Babulo+ ndipo anamuuza kuti: “Musaphe mwamuna aliyense wanzeru mʼBabulo. Ndipititseni kwa mfumu ndipo ine ndikamasulira maloto ake.” 25  Mofulumira, Arioki anapititsa Danieli kwa mfumu nʼkuiuza kuti: “Ndapeza munthu pakati pa anthu amene anatengedwa ukapolo ku Yuda+ yemwe angamasulire maloto anu mfumu.” 26  Mfumuyo inafunsa Danieli, amene dzina lake linali Belitesazara+ kuti: “Kodi ungathedi kundiuza maloto amene ndinalota komanso kuwamasulira?”+ 27  Danieli anayankha mfumuyo kuti: “Palibe amuna anzeru, anthu olankhula ndi mizimu, ansembe ochita zamatsenga kapena anthu okhulupirira nyenyezi amene angakwanitse kukuuzani inu mfumu chinsinsi chimene mukufuna kudziwa.+ 28  Koma kumwamba kuli Mulungu amene ndi Woulula zinsinsi,+ ndipo wakudziwitsani inu Mfumu Nebukadinezara zimene zidzachitike mʼmasiku otsiriza. Maloto anu komanso masomphenya amene munaona muli pabedi lanu ndi awa: 29  Inu mfumu, mutagona pabedi lanu munayamba kuganiza za zinthu zimene zidzachitike mʼtsogolo ndipo Mulungu amene ndi Woulula zinsinsi wakudziwitsani zimene zidzachitike. 30  Sikuti chinsinsi chimenechi chaululidwa kwa ine chifukwa chakuti ndine wanzeru kuposa munthu wina aliyense, koma chaululidwa nʼcholinga chakuti ndikumasulireni malotowo inu mfumu ndiponso kuti mudziwe maganizo amumtima mwanu.+ 31  Inuyo mfumu munalota mukuona chifaniziro chachikulu kwambiri. Chifanizirocho chinali chitaima patsogolo panu ndipo chinali chachikulu komanso chowala kwambiri ndipo chimaoneka mochititsa mantha. 32  Mutu wa chifanizirocho unali wagolide wabwino kwambiri,+ pachifuwa pake ndi manja ake zinali zasiliva,+ mimba yake ndi ntchafu zake zinali zakopa,*+ 33  miyendo yake inali yachitsulo+ ndipo mapazi ake anali achitsulo chosakanikirana ndi dongo.+ 34  Munapitiriza kuyangʼana mpaka mwala unadulidwa kuphiri koma osati ndi manja a munthu. Mwalawo unamenya chifanizirocho kumapazi ake achitsulo chosakanikirana ndi dongo nʼkuwaphwanya.+ 35  Pa nthawi imeneyo chitsulo, dongo, kopa, siliva ndi golide, zonse zinaphwanyikaphwanyika ndipo zinakhala ngati mankhusu* apamalo opunthirapo mbewu mʼchilimwe. Mphepo inaziuluza moti sizinaonekenso. Koma mwala umene unamenya chifanizirocho unakhala phiri lalikulu ndipo linadzaza dziko lonse lapansi. 36  Maloto anu ndi amenewa mfumu ndipo tsopano tikuuzani kumasulira kwake. 37  Inuyo mfumu yomwe ndi mfumu ya mafumu, amene Mulungu wakumwamba wakupatsani ufumu,+ mphamvu ndi ulemerero, 38  inuyo amene Mulungu wakupatsani mphamvu zolamulira anthu kulikonse kumene akukhala komanso nyama zakutchire ndi mbalame zamumlengalenga, amene Mulungu wakuikani kuti muzilamulira zonsezi,+ inuyo ndi mutu wagolide.+ 39  Koma pambuyo panu padzabwera ufumu+ wina wotsikirapo kwa inu. Kenako padzabweranso ufumu wina wachitatu, wakopa, umene udzalamulire dziko lonse lapansi.+ 40  Ufumu wa nambala 4 udzakhala wolimba ngati chitsulo.+ Mofanana ndi chitsulo chimene chimaphwanya nʼkupera china chilichonse, ufumuwo udzaphwanya nʼkuwonongeratu maufumu ena onsewa.+ 41  Mogwirizana ndi zimene munaona kuti mapazi ndi zala zakumiyendo zinali zadongo la woumba mbiya losakanikirana ndi chitsulo, ufumuwo udzakhala wogawanika. Koma udzakhala wolimba pa zinthu zina ngati chitsulo, ngati mmene munaonera kuti chitsulocho chinali chosakanikirana ndi dongo lofewa. 42  Popeza zala zakumiyendo zinali zachitsulo chosakanikirana ndi dongo, pa zinthu zina ufumuwo udzakhala wolimba koma pa zinthu zina udzakhala wosalimba. 43  Mogwirizana ndi zimene munaona kuti chitsulo chinasakanikirana ndi dongo lofewa, mbali zake zina zidzasakanikirana ndi anthu* koma sadzagwirizana mofanana ndi mmene zimakhalira kuti chitsulo sichingasakanikirane bwinobwino ndi dongo. 44  Mʼmasiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu+ umene sudzawonongedwa.+ Ufumu umenewu sudzaperekedwa kwa anthu a mtundu wina uliwonse.+ Koma udzaphwanya nʼkuthetsa maufumu ena onsewa+ ndipo ndi ufumu wokhawu umene udzakhalepo mpaka kalekale.+ 45  Zidzachitika mogwirizana ndi zimene munaona kuti mwala unadulidwa kuphiri koma osati ndi manja a munthu ndipo unaphwanya chitsulo, kopa, dongo, siliva ndi golide.+ Inu mfumu, Mulungu Wamkulu wakudziwitsani zimene zidzachitike mʼtsogolo.+ Maloto amenewa adzakwaniritsidwa ndithu ndipo kumasulira kwake nʼkodalirika.” 46  Ndiyeno Mfumu Nebukadinezara anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi pamaso pa Danieli nʼkumupatsa ulemu. Iye analamula kuti Danieli apatsidwe mphatso komanso kuti amufukizire zofukiza zonunkhira. 47  Mfumuyo inauza Danieli kuti: “Ndithudi Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu, Ambuye wa mafumu komanso Woulula zinsinsi, chifukwa iwe wakwanitsa kuulula chinsinsi chimenechi.”+ 48  Kenako mfumu inamukweza pa udindo Danieli ndipo inamupatsa mphatso zambiri zabwino. Inamuikanso kuti akhale wolamulira wa chigawo chonse cha Babulo+ ndiponso mkulu wa akuluakulu a boma amene ankayangʼanira amuna onse anzeru a mʼBabulo. 49  Ndipo Danieli anapempha mfumu kuti iike Shadireki,* Misheki* ndi Abedinego+ kuti akhale oyangʼanira ntchito za boma mʼchigawo cha Babulo, ndipo mfumuyo inawaikadi. Koma Danieli ankagwira ntchito kunyumba ya mfumu.

Mawu a M'munsi

Kameneka kanali kagulu ka anthu amene anali ndi luso lolosera zamʼtsogolo komanso kuphunzira zokhudza nyenyezi.
Mawu a pa Da 2:4b mpaka 7:28 poyambirira analembedwa mʼChiaramu.
Mabaibulo ena amati, “kudzala; milu ya ndowe.”
Kapena kuti, “kuyambira kalekale mpaka kalekale.”
Kapena kuti, “zamkuwa.”
“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Kapena kuti, “ana a anthu,” amene ndi anthu wamba.
Kapena kuti, “Sadirake.”
Kapena kuti, “Mesake.”