Mika 4:1-13

  • Phiri la Yehova lidzakwezedwa (1-5)

    • Kusula malupanga kuti akhale makasu a pulawo (3)

    • ‘Ife tidzayenda mʼdzina la Yehova’ (5)

  • Ziyoni adzakhalanso wamphamvu (6-13)

4  Mʼmasiku otsiriza,Phiri la nyumba ya Yehova+Lidzakhazikika pamwamba penipeni pa mapiri akuluakulu,Ndipo lidzakwezedwa kupitirira mapiri angʼonoangʼono.Anthu a mitundu yosiyanasiyana adzapita kumeneko.+  2  Anthu ochokera mʼmitundu yosiyanasiyana adzabwera nʼkunena kuti: “Bwerani, tiyeni tipite kuphiri la Yehova,Tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo.+ Iye akatiphunzitsa njira zake,Ndipo ife tidzayenda mʼnjira zakezo.” Chifukwa chilamulo,* chidzaphunzitsidwa mu ZiyoniNdipo mawu a Yehova adzaphunzitsidwa mu Yerusalemu.  3  Mulungu adzaweruza mitundu yambiri ya anthu,+Ndipo adzakonza zinthu zolakwika zokhudza anthu ochokera mʼmitundu yamphamvu yakutali. Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo,Ndiponso mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo.+ Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake,Ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.+  4  Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu,+Ndipo sipadzakhala wowaopseza,+Chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena zimenezi.  5  Anthu a mtundu uliwonse adzayenda mʼdzina la mulungu wawo.Koma ife tidzayenda mʼdzina la Yehova Mulungu+ wathu mpaka kalekale.  6  Yehova wanena kuti, “Pa tsiku limenelo,Ndidzasonkhanitsa anthu amene ankayenda motsimphina.Ndidzasonkhanitsanso anthu amene anamwazikana,+Komanso anthu amene ndinawalanga.  7  Anthu amene ankayenda motsimphina, ndidzawasonkhanitsanso ngati anthu otsala.+Anthu amene anachotsedwa mʼdziko lawo nʼkupita kutali, ndidzawasandutsa mtundu wamphamvu.+Ndipo Yehova adzakhala mfumu yawo mʼphiri la Ziyoni,Kuyambira panopa mpaka kalekale.  8  Koma iwe nsanja ya gulu la nkhosa,Malo okwera a mwana wamkazi wa Ziyoni,*+Ulamuliro udzabwerera. Ulamuliro woyamba udzabwerera kwa iwe,+Ufumu wa mwana wamkazi wa Yerusalemu.*+  9  Ndiye nʼchifukwa chiyani ukufuula kwambiri? Kodi ulibe mfumu?Kapena alangizi ako awonongedwa?Moti ukumva zowawa ngati mkazi amene akubereka?+ 10  Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni udzamva ululu woopsa,Ngati mkazi amene akubereka.Chifukwa tsopano uchoka mʼtauni nʼkupita kukakhala kumudzi. Ukafika mpaka ku Babulo,+Ndipo kumeneko udzapulumutsidwa.+Kumeneko Yehova adzakuwombola mʼmanja mwa adani ako.+ 11  Anthu amitundu yosiyanasiyana adzasonkhana kuti akuukire.Anthuwo adzanena kuti, ‘Tiyeni timuwononge,Ndipo maso athu aone zimenezi zikuchitikira Ziyoni.’ 12  Koma iwo sakudziwa maganizo a Yehova.Iwo sakumvetsa cholinga chake.Chifukwa adzawasonkhanitsa pamalo opunthira mbewu ngati mmene amasonkhanitsira tirigu amene angomumweta kumene. 13  Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, nyamuka upunthe tirigu.+Chifukwa nyanga zako ndidzazisandutsa chitsulo.Ziboda zako ndidzazisandutsa kopa.*Ndipo udzanyenyanyenya mitundu yambiri ya anthu.+ Phindu limene iwo apeza mwachinyengo, udzalipereka kwa Yehova.Ndipo zinthu zawo udzazipereka kwa Ambuye woona wa dziko lonse lapansi.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “malangizo.”
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Yerusalemu” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Kapena kuti, “mkuwa.”