Mika 1:1-16

  • Chiweruzo cha Samariya ndi Yuda (1-16)

    • Machimo ndi kugalukira zinabweretsa mavuto (5)

1  Yehova analankhula ndi Mika*+ wa ku Morese mʼmasiku a Yotamu,+ Ahazi+ ndi Hezekiya,+ mafumu a Yuda.+ Analankhula naye kudzera mʼmasomphenya ndipo anamuuza zokhudza Samariya ndi Yerusalemu kuti:  2  “Tamverani anthu nonsenu! Mvetsera mwatcheru iwe dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo.Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa akhale mboni yokutsutsani,+Yehova akutsutseni ali mʼkachisi wake woyera.  3  Tamverani! Yehova akuchoka pamalo ake,Ndipo atsika nʼkupondaponda malo okwezeka apadziko lapansi.  4  Mapiri adzasungunuka kumapazi ake,+Ndipo zigwa zidzagawanika,Ngati phula losungunuka ndi moto.Ndipo zidzayenda ngati madzi othiridwa pamalo otsetsereka.  5  Zonsezi zidzachitika chifukwa chakuti Yakobo wandigalukira.Ndiponso chifukwa cha machimo a nyumba ya Isiraeli.+ Kodi wachititsa kuti Yakobo andigalukire ndani? Kodi si anthu a ku Samariya?+ Wachititsa ndani kuti Yuda akhale ndi malo okwezeka?+ Si anthu a ku Yerusalemu kodi?  6  Samariya ndidzamusandutsa bwinja,Malo oyenera kudzalapo mpesa.Miyala yake ndidzaiponya* mʼchigwa.Ndipo maziko ake ndidzawafukula nʼkuwasiya pamtunda.  7  Zifaniziro zake zonse zogoba zidzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswazidutswa.+Ndipo mphatso zonse zimene ankalandira ngati malipiro zidzatenthedwa pamoto.+ Mafano ake onse ndidzawawononga. Chifukwa anawapeza kuchokera ku ndalama zimene ankalandira pochita uhule.Ndipo tsopano zinthu zimenezi zidzatengedwa kuti zikakhale malipiro a mahule kwinakwake.”  8  Chifukwa cha zimenezi ndidzalira ndi kufuula.+Ndidzayenda wopanda nsapato komanso wosavala.+ Ndidzalira ngati mimbulu,Ndiponso ngati nthiwatiwa.  9  Bala lake ndi losachiritsika,+Ndipo lakafika mpaka ku Yuda.+ Mliri umenewu wafalikira mpaka kukafika pageti la anthu amtundu wanga ku Yerusalemu.+ 10  “Musanene zimenezi ku Gati.Ndipo musalire ngakhale pangʼono. Gubudukani pafumbi ku Beti-afira.* 11  Inu anthu a ku Safiri, tulukani mʼdziko lanu muli maliseche ndiponso mukuchititsa manyazi. Anthu a ku Zaanana sanachoke mʼdziko lawo. Ku Beti-ezeli kuzingomveka kulira kokhakokha ndipo anthu ake adzasiya kukuthandizani. 12  Anthu a ku Maroti ankayembekezera zinthu zabwino,Koma zoipa zochokera kwa Yehova zafika pageti la ku Yerusalemu. 13  Inu anthu a ku Lakisi, mangirirani galeta ku gulu la mahatchi.*+ Ndinu amene munayambitsa tchimo la mwana wamkazi wa Ziyoni,*Popeza kugalukira kwa Isiraeli kunapezeka mwa inu.+ 14  Choncho mudzapereka mphatso zotsanzikirana kwa Moreseti-gati. Anthu a ku Akizibu+ anapusitsa mafumu a Isiraeli. 15  Inu anthu a ku Maresha+ ndidzakubweretserani munthu wokugonjetsani,*+ Ulemerero wa Isiraeli udzafika mpaka ku Adulamu.+ 16  Muchotse tsitsi lonse ndipo mumete mpala chifukwa cha ana anu amene mumawakonda. Metani mpala ngati wa chiwombankhanga,Chifukwa chakuti ana anuwo atengedwa kupita kudziko lina.”+

Mawu a M'munsi

^ Chidule cha dzina lakuti Mikayeli (kutanthauza “Ndani Ali Ngati Mulungu”) kapena Mikaya (kutanthauza “Ndani Ali Ngati Yehova”).
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “ndidzaikhuthulira.”
^ Kapena kuti, “mʼnyumba ya Afira.”
^ Ena amati “mahosi.”
^ Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
^ Kapena kuti, “wolanda zinthu za ena.”