Kalata Yopita kwa Aroma 2:1-29

  • Chiweruzo cha Mulungu kwa Ayuda ndi Agiriki (1-16)

    • Mmene chikumbumtima chimagwirira ntchito (14, 15)

  • Ayuda ndiponso Chilamulo (17-24)

  • Mdulidwe wa mumtima (25-29)

2  Choncho kaya ndiwe ndani,+ ngati umaweruza ena, ulibe chifukwa chomveka chodzilungamitsira. Popeza ukamaweruza ena, umakhala ukudzitsutsa wekha, chifukwa iwenso umachita zomwezo.+ 2  Tikudziwa kuti Mulungu akamaweruza anthu amene amachita zimenezi kuti ndi oyenera kulandira chilango, amawaweruza mogwirizana ndi choonadi. 3  Koma iweyo ukamaweruza anthu amene amachita zinthu zimene iwenso umachita, kodi ukuganiza kuti udzazemba chiweruzo cha Mulungu? 4  Kodi sukudziwa kuti Mulungu akukusonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu,+ kusakwiya msanga+ komanso kuleza mtima+ nʼcholinga choti ulape?+ 5  Koma chifukwa chakuti sukufuna kusintha, ndipo ukusonyeza mtima wosalapa, Mulungu adzakulanga ndithu pa tsiku la mkwiyo wake akamadzaulula chiweruzo chake cholungama.+ 6  Iye adzaweruza aliyense mogwirizana ndi zochita zake.+ 7  Adzapereka moyo wosatha kwa anthu amene akupitirizabe kuchita zabwino.+ Anthu amenewa akuyesetsa kupeza ulemerero, ulemu ndi moyo wosawonongeka. 8  Koma anthu amene amakonda mikangano, satsatira choonadi komanso amachita zosalungama, Mulungu adzawasonyeza mkwiyo wake.+ 9  Munthu aliyense wochita zoipa, kaya akhale Myuda kapena Mgiriki, adzakumana ndi mavuto komanso zowawa. 10  Koma aliyense wochita zabwino adzalandira ulemerero, ulemu ndi mtendere, choyamba Myuda+ kenako Mgiriki.+ 11  Chifukwa Mulungu alibe tsankho.+ 12  Anthu onse amene anachimwa asakudziwa Chilamulo, adzafa asakudziwa Chilamulo.+ Koma onse amene anachimwa akudziwa Chilamulo, adzaweruzidwa mogwirizana ndi Chilamulocho.+ 13  Paja anthu ongomva Chilamulo, Mulungu samawaona kuti ndi olungama koma amene amatsatira Chilamulo ndi amene adzaonedwe kuti ndi olungama.+ 14  Anthu a mitundu ina alibe Chilamulo.+ Koma akamachita mwachibadwa zinthu zomwe zili mʼChilamulo, ngakhale kuti alibe Chilamulo, amasonyeza kuti ali ndi Chilamulo mumtima mwawo. 15  Amenewa amasonyeza kuti mfundo za mʼChilamulo zinalembedwa mʼmitima mwawo ndipo chikumbumtima chawo chimawachitira umboni. Anthu amenewa maganizo awo amawatsutsa kapenanso kuwavomereza. 16  Zimenezi zidzaonekera pa tsiku limene Mulungu, kudzera mwa Khristu Yesu, adzaweruze zinthu zachinsinsi zimene anthu amachita komanso kuganiza.+ Ndipo adzaweruza mogwirizana ndi uthenga wabwino umene ndikulalikira. 17  Enanu mumadzitchula kuti ndinu Ayuda,+ mumadalira Chilamulo ndiponso mumadzitama kuti muli pa ubwenzi ndi Mulungu. 18  Mumadziwa zimene Mulungu amafuna komanso mumasangalala ndi zinthu zabwino kwambiri chifukwa chakuti munaphunzitsidwa Chilamulo.+ 19  Mumakhulupirira kuti mungathe kutsogolera akhungu komanso kuunikira anthu amene ali mumdima. 20  Mumaganiza kuti mungathe kuwongolera anthu opanda nzeru. Mumaganizanso kuti mungathe kuphunzitsa ana chifukwa mumamvetsa komanso kudziwa choonadi chopezeka mʼChilamulo. 21  Kodi iwe amene umaphunzitsa ena, bwanji sudziphunzitsa wekha?+ Umalalikira kuti, “Usabe,”+ ndiye iwe umabanso? 22  Iwe amene umanena kuti, “Usachite chigololo,”+ kodi umachitanso chigololo? Iweyo amene umalankhula zosonyeza kuti umanyansidwa ndi mafano, ndiye umabanso zamʼkachisi? 23  Iwe wonyadira Chilamulo, kodi umachitiranso Mulungu chipongwe pophwanya Chilamulo? 24  “Dzina la Mulungu likunyozedwa pakati pa anthu amitundu ina chifukwa cha inu,” ngati mmene Malemba amanenera.+ 25  Mdulidwe+ ndi waphindu pokhapokha ngati iweyo umatsatiradi Chilamulo.+ Koma ngati umaphwanya Chilamulo, mdulidwe wako ndi wopanda ntchito. 26  Choncho ngati munthu wosadulidwa+ akutsatira mfundo zolungama za mʼChilamulo, kusadulidwa kwake kudzaonedwa ngati kudulidwa, si choncho?+ 27  Munthu amene ndi wosadulidwa akamatsatira Chilamulo, adzakuweruza. Adzakuweruza iweyo amene umaphwanya Chilamulo ngakhale kuti uli ndi malamulo olembedwa ndiponso ndiwe wodulidwa. 28  Amene ali Myuda kunja kokha si Myuda,+ ndiponso mdulidwe wakunja kokha wochitidwa pathupi, si mdulidwe.+ 29  Kukhala Myuda weniweni kuli mumtima+ ndipo mdulidwe wake umakhalanso wamumtima+ wochitidwa ndi mzimu, osati ndi malamulo olembedwa.+ Munthu woteroyo amatamandidwa ndi Mulungu, osati anthu.+

Mawu a M'munsi