Kalata Yopita kwa Aroma 6:1-23

  • Moyo watsopano kudzera mu ubatizo wogwirizana ndi Khristu (1-11)

  • Musalole kuti uchimo uzilamulira matupi anu (12-14)

  • Kuchoka ku ukapolo wauchimo nʼkukhala akapolo a Mulungu (15-23)

    • Malipiro a uchimo ndi imfa; mphatso ya Mulungu ndi moyo (23)

6  Ndiye tinene kuti chiyani? Kodi tipitirize kuchimwa kuti kukoma mtima kwakukulu kuwonjezeke?  Ayi ndithu. Popeza tinafa ku uchimo,+ ndiye tipitirize kuchimwa chifukwa chiyani?+  Kapena simudziwa kuti tonsefe amene tinabatizidwa ndipo tsopano ndife ogwirizana ndi Khristu Yesu+ tinabatizidwanso mu imfa yake?+  Choncho tinaikidwa naye limodzi mʼmanda pamene tinabatizidwa mu imfa yake,+ kuti mofanana ndi Khristu amene anaukitsidwa kudzera mu ulemerero wa Atate, ifenso tikhale moyo watsopano.+  Chifukwa ngati tagwirizana naye pofa imfa yofanana ndi yake,+ ndithudi tidzagwirizananso naye poukitsidwa mofanana naye.+  Chifukwa tikudziwa kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa naye+ limodzi pamtengo nʼcholinga chakuti thupi lathu lauchimo likhale lopanda mphamvu,+ kuti tisakhalenso akapolo a uchimo.+  Chifukwa munthu amene wafa sakhalanso ndi mlandu* wa machimo ake.  Ndiponso, ngati tinafa limodzi ndi Khristu, timakhulupirira kuti tidzakhalanso ndi moyo limodzi ndi iye.  Tikudziwa kuti popeza Khristu waukitsidwa,+ sadzafanso+ ndipo imfa sikumulamuliranso ngati mfumu. 10  Iye anafa kuti achotse uchimo kamodzi kokha basi+ ndipo moyo umene ali nawo, ali nawo kuti azichita chifuniro cha Mulungu. 11  Nanunso muzidziona ngati akufa pa nkhani ya uchimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.+ 12  Choncho musalole kuti uchimo uzilamulirabe ngati mfumu mʼmatupi anu oti akhoza kufawo+ kuti muzitsatira zilakolako zawo. 13  Ndipo musapereke matupi* anu ku uchimo kuti akhale zida zochitira zinthu zosalungama, koma dziperekeni kwa Mulungu ngati anthu amene aukitsidwa. Matupi anunso muwapereke kwa Mulungu ngati zida zochitira chilungamo.+ 14  Uchimo usamakulamulireni ngati mfumu, chifukwa simukutsatira Chilamulo,+ koma mukusangalala ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.+ 15  Kodi zikatere ndiye kuti tizichita tchimo chifukwa chakuti sitikutsatira Chilamulo koma tikusangalala ndi kukoma mtima kwakukulu?+ Ayi ndithu. 16  Kodi simukudziwa kuti mukamadzipereka kwa winawake ngati akapolo omvera, mumakhala akapolo a amene mukumumverayo?+ Mumakhala akapolo a uchimo+ umene umatsogolera ku imfa,+ kapena akapolo a kumvera komwe kumatsogolera ku chilungamo. 17  Koma tikuthokoza Mulungu kuti ngakhale kuti poyamba munali akapolo a uchimo, munamvera mochokera pansi pa mtima mfundo zatsopano zomwe munaphunzitsidwa. 18  Inde, popeza munamasulidwa ku uchimo,+ munakhala akapolo a chilungamo.+ 19  Ndikulankhulatu ngati munthu chifukwa cha kufooka kwa matupi anu. Mmene munaperekera ziwalo zanu kuti zikhale akapolo a zonyansa ndiponso akapolo a kusamvera malamulo nʼcholinga chakuti muzichita zinthu zophwanya malamulo, perekaninso ziwalo zanu kuti mukhale akapolo a chilungamo ndiponso oyera.+ 20  Chifukwa pamene munali akapolo a uchimo, munali omasuka ku chilungamo. 21  Kodi pa nthawiyo munkabala zipatso zotani? Zinali zinthu zimene panopa mumachita nazo manyazi. Ndipo mapeto a zinthu zimenezo ndi imfa.+ 22  Koma tsopano chifukwa munamasulidwa ku uchimo nʼkukhala akapolo a Mulungu, mukubala zipatso za chiyero+ ndipo pamapeto pake mudzakhala ndi moyo wosatha.+ 23  Chifukwa malipiro a uchimo ndi imfa,+ koma mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha+ kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “wamasuka; wakhululukidwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ziwalo.”