Pitani ku nkhani yake

Kodi Mawu Akuti Kuuka kwa Akufa Amatanthauza Chiyani?

Kodi Mawu Akuti Kuuka kwa Akufa Amatanthauza Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

 Mawu amene anawamasulira m’Baibulo kuti ‘kuuka kwa akufa,’ anachokera ku mawu achigiriki akuti a·naʹsta·sis, omwe amatanthauza “kudzuka” kapena “kuimiriranso.” Munthu amene waukitsidwa kwa akufa amakhalanso ndi moyo ngati mmene analili asanamwalire.—1  Akorinto 15:12, 13.

 N’zoona kuti mawu akuti “kuuka kwa akufa” sapezeka m’Malemba Achiheberi, amene nthawi zambiri amatchedwa Chipangano Chakale. Komabe, mfundo yakuti akufa adzauka imapezeka m’malemba amenewa. Mwachitsanzo, kudzera mwa mneneri Hoseya, Mulungu analonjeza kuti: “Ine ndidzawawombola ku Manda ndiponso ku imfa.”​—Hoseya 13:14; Yobu 14:13-​15; Yesaya 26:19; Danieli 12:​2, 13.

 Kodi anthu oukitsidwa adzakhala kuti? Anthu ena akaukitsidwa, amapita kumwamba kuti akalamulire monga mafumu pamodzi ndi Khristu. (2 Akorinto 5:1; Chivumbulutso 5:9, 10) Baibulo limanena kuti kuuka kumeneku ndi “kuuka koyamba” kapena “kuuka koyambirira,” ndipo mawu awiri onsewa akusonyeza kuti padzakhalanso kuuka kwina. (Chivumbulutso 20:6; Afilipi 3:​11) Anthu omwe adzaukitsidwe pa kuuka kwinako adzakhala ambirimbiri ndipo adzasangalala ndi moyo wosatha padziko lapansi.​—Salimo 37:29.

 Kodi anthu adzaukitsidwa bwanji? Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zoukitsira akufa. (Yohane 11:25) Yesu adzaukitsa ‘onse amene ali m’manda achikumbutso,’ munthu aliyense ngati mmene analili poyamba. (Yohane 5:​28, 29) Anthu oukitsidwa kuti apite kumwamba amauka ndi thupi lauzimu, koma anthu oukitsidwa kuti akhale padziko lapansi adzauka ndi thupi labwino, lopanda matenda komanso lopanda chilema chilichonse.​—Yesaya 33:24; 35:​5,  6; 1 Akorinto 15:42-​44, 50.

 Kodi ndi anthu otani amene adzaukitsidwe? Baibulo limanena kuti “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) M’gulu la anthu olungamali muli anthu ngati Nowa, Sara ndiponso Abulahamu. (Genesis 6:9; Aheberi 11:11; Yakobo 2:21) M’gulu la anthu osalungama muli anthu amene sankatsatira mfundo za Mulungu koma analibe mwayi woti n’kuphunzira Mawu a Mulungu n’kumawatsatira.

 Komabe, anthu amene amachita zinthu zoipa kwambiri ndipo safuna kusintha sadzaukitsidwa. Anthu oterewa akamwalira, zawo zimathera pomwepo ndipo sangayembekezere kuti angadzakhalenso ndi moyo.—Mateyu 23:33; Aheberi 10:26, 27.

 Kodi anthu akufa adzaukitsidwa liti? Baibulo linalosera kuti anthu opita kumwamba adzayamba kuukitsidwa m’nthawi ya kukhalapo kwa Khristu, yomwe inayamba mu 1914. (1 Akorinto 15:21-​23) Koma anthu oukitsidwa kuti akhale ndi moyo padziko lapansi adzayamba kuukitsidwa mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Yesu Khristu. Mu ulamuliro umenewu, dziko lapansi lidzakonzedwa n’kukhala paradaiso.—Luka 23:43; Chivumbulutso 20:6, 12, 13.

 N’chifukwa chiyani n’zomveka kukhulupirira kuti akufa adzauka? M’Baibulo muli nkhani za anthu 9 amene anaukitsidwa, ndipo nkhani iliyonse imasonyeza kuti panali anthu amene anaonadi anthu oukitsidwawo. (1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:32-37; 13:20, 21; Luka 7:11-17; 8:40-56; Yohane 11:38-44; Machitidwe 9:36-42; 20:7-12; 1 Akorinto 15:3-6) Mwachitsanzo, nkhani ya Lazaro amene anaukitsidwa ndi Yesu ndi yochititsa chidwi kwambiri. Izi zili choncho chifukwa panadutsa masiku 4 Lazaroyo atamwalira m’pamene Yesu anamuukitsa ndipo anthu ambiri anamuona. (Yohane 11:39, 42) Ngakhale anthu amene ankatsutsa Yesu, sanatsutse zoti Lazaro waukitsidwa. M’malomwake, iwo anakonza chiwembu choti aphe Yesu ndi Lazaro yemwe.—Yohane 11:47, 53; 12:9-11.

 Baibulo limasonyeza kuti Mulungu ali ndi mphamvu zoti angaukitse akufa komanso ali ndi mtima wofunitsitsa kuwaukitsa. Palibe chimene iye angaiwale ndipo amakumbukira chilichonse chokhudza munthu aliyense amene anamwalira. Choncho adzagwiritsa ntchito mphamvu zake zopanda malire poukitsa akufa. (Yobu 37:23; Mateyu 10:30; Luka 20:37, 38) Monga mmene taonera, Mulungu ali ndi mphamvu zoukitsa akufa komanso ndi wofunitsitsa kuwaukitsa. Potsimikizira zoti anthu adzaukitsidwa m’tsogolomu, Baibulo limati Mulungu ‘adzalakalaka ntchito ya manja ake.”—Yobu 14:15.

Maganizo olakwika pa nkhani ya kuuka kwa akufa

 Zimene ena amakhulupirira: Mawu akuti kuuka kwa akufa amatanthauza kugwirizananso kwa thupi ndi mzimu.

 Zoona zake: Baibulo limaphunzitsa kuti mzimu, kapena kuti moyo, ndi munthu weniweniyo osati chinthu chinachake chimene chimakhala mwa munthu ndipo chimapitiriza kukhala ndi moyo munthuyo akamwalira. (Genesis 2:7; Ezekieli 18:4) Munthu akamaukitsidwa sikuti thupi ndi mzimu wake zimagwirizanitsidwanso ayi. Koma munthuyo amakhala kuti walengedwanso.

 Zimene ena amakhulupirira: Anthu ena amaukitsidwa kenako n’kuwonongedwa nthawi yomweyo.

 Zoona zake: Baibulo limanena kuti anthu “amene anali kuchita zoipa adzauka kuti aweruzidwe.” (Yohane 5:29) Koma anthuwo adzaweruzidwa potengera zimene adzachite ataukitsidwa, osati zimene anachita asanamwalire. Yesu anati: “Akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu, ndipo olabadirawo adzakhala ndi moyo.” (Yohane 5:25) Anthu amene ‘adzalabadire,’ kapena kumvera zinthu zimene adzaphunzitsidwe akadzaukitsidwa, mayina awo adzalembedwa mu “mpukutu wa moyo.”—Chivumbulutso 20:12, 13.

 Zimene ena amakhulupirira: Munthu adzaukitsidwa ndi thupi limene anali nalo asanamwalire.

 Zoona zake: Munthu akamwalira, thupi lake limawonongeka n’kusanduka dothi.—Mlaliki 3:19, 20.