Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Dzikoli Lidzatha? Kodi Baibulo Limanena Kuti Zinthu Zonse Zidzawonongedwa?

Kodi Dzikoli Lidzatha? Kodi Baibulo Limanena Kuti Zinthu Zonse Zidzawonongedwa?

 Kodi mumaganizira chiyani mukamva za “kutha kwa dziko”? Mwina mumaganiza kuti zinthu zonse zapadzikoli zidzawonongedwa. Anthu ena amakhulupirira kuti zimenezi zidzachitikadi, makamaka akawerenga m’nyuzi nkhani zochititsa mantha monga izi:

  •   “Nkhondo yanyukiliya ikhoza kuyamba mosavuta, kaya mwadala, mwangozi kapena chifukwa cholephera kumvana bwino.”​—Bulletin of the Atomic Scientists.

  •   “Pa zaka 10 zapitazi padziko lonse lapansi, kwakhala kukuchitika ngozi zambiri zachilengedwe monga mphepo zamkuntho, moto wam’nkhalango, chilala, kuwonongeka kwa miyala yakunyanja, kutentha koopsa komanso kusefukira kwa madzi.​—National Geographic.

  •   “Dzombe lakhala likuwononga zinthu zambiri ku Africa kuposa kale.”​—The Associated Press.

 Kodi dzikoli lidzawonongedwa? Kodi Baibulo limanena zotani pa nkhaniyi?

Kodi dziko lapansi lidzatha?

 Ayi. Baibulo limalonjeza kuti dziko lapansi lidzakhala mpaka kalekale. (Mlaliki 1:4) M’malo mowononga dziko lapansi limene analilenga, Mulungu adzawononga anthu “amene akuwononga dziko lapansi.”​—Chivumbulutso 11:18.

Kodi dziko lomwe lidzathe ndi liti?

 Mogwirizana ndi Baibulo, dziko limene lidzathe ndi la anthu onse amene amanyalanyaza Mulungu n’kumangochita zofuna zawo. Mofanana ndi zimene anachita m’nthawi ya Nowa, Mulungu adzawononga ‘anthu osamuopa.’​—2 Petulo 2:5; 3:7.

 Lemba la 1 Yohane 2:17 limati: “Dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake.” Lembali likusonyeza kuti Mulungu sadzawononga dziko lapansi koma adzawononga anthu amene akutsatira zilakolako zawo zoipa.

Kodi mapeto adzafika liti?

 Baibulo silinena nthawi imene mapeto afike. (Mateyu 24:36) Koma limasonyeza kuti afika posachedwapa. Baibulo linaneneratu kuti zinthu zotsatirazi zizichitika pamene mapeto ali pafupi:

 Anthu ambiri amavomera kuti kuyambira m’chaka cha 1914, zimene zakhala zikuchitika padzikoli zikufanana ndi zimene Baibulo linaneneratu ndipo mapeto ali pafupi. Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yakuti “Kodi Ulosi wa M’Baibulo Umatiuza Zotani pa Nkhani ya Chaka cha 1914?” komanso yakuti “Kodi Chizindikiro cha ‘Masiku Otsiriza Kapena Kuti ‘Nthawi ya Mapeto’ N’chiyani?

Kodi buku la m’Baibulo la Chivumbulutso limanena kuti zinthu zonse zidzawonongedwa?

 Buku la Chivumbulutso limanena za ‘kuonekera kwa Ambuye Yesu.’ Kuonekera kumeneku kudzachitika pamene Yesu adzaonekeretu kuti ndi amene ali ndi mphamvu zochotsa zinthu zonse zoipa padzikoli komanso zopereka mphoto kwa anthu amene akulambira Mulungu.​—2 Atesalonika 1:6, 7; 1 Petulo 1:7, 13.

 Dzina la buku lomaliza la m’Baibulo ndi Chivumbulutso chifukwa choti limavumbula, kapena kuti kuulula, zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo. (Chivumbulutso 1:1) M’bukuli muli uthenga wabwino wotithandiza kumayembekezera zinthu zabwino m’tsogolo. (Chivumbulutso 1:3) Limasonyeza kuti Mulungu adzathetseratu zinthu zonse zopanda chilungamo ndipo adzasintha dzikoli kuti likhale labwino kwambiri. Pa nthawi imeneyo, anthu sadzavutikanso, kumva kupweteka, kapena kufa kumene.​—Chivumbulutso 21:3, 4.

 Kodi mungakonde kudziwa zambiri zokhudza zinthu zabwino zimene Baibulo limalonjeza? A Mboni za Yehova amaphunzira Baibulo ndi anthu kwaulere. Mukhoza kuwapempha kuti aziphunzira nanu.