Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

CreativeDesignArt/DigitalVision Vectors via Getty Images

KHALANI MASO

Kodi N’zotheka Kuti Anthu a Mitundu Yonse Azionedwa Mofanana?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi N’zotheka Kuti Anthu a Mitundu Yonse Azionedwa Mofanana?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Anthu ambiri amaona kuti n’zosatheka kuti anthu a mitundu yonse azionedwa mofanana, moti amati amenewa ndi maloto chabe.

  •   A António Guterres yemwe ndi Mlembi wa bungwe la UN ananena kuti: “Pa dziko lonse lapansi, mabungwe, magulu a anthu komanso moyo wa anthu wa tsiku ndi tsiku zikusokonekera chifukwa cha tsankho lomwe lili ngati poizoni.”

 Kodi zidzathekadi kuti anthu amitundu yonse azionedwa mofanana? Kodi Baibulo limanena zotani?

Mmene Mulungu amaonera mitundu ya anthu

 Baibulo limatiuza mmene Mulungu amaonera mitundu yosiyanasiyana ya anthu.

  •   “Kuchokera mwa munthu mmodzi [Mulungu] anapanga mtundu wonse wa anthu, kuti akhale padziko lonse lapansi.”—Machitidwe 17:26.

  •   “Mulungu alibe tsankho, Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”—Machitidwe 10:34, 35.

 Baibulo limanena kuti tonse ndife anthu a banja limodzi ndipo Mulungu amalandira anthu ochokera ku mitundu yonse.

Mmene kusankhana mitundu kudzathere

 Ufumu wa Mulungu womwe ndi boma lakumwamba udzathetsa kusankhana mitundu. Bomali lidzaphunzitsa anthu mmene angamachitire zinthu ndi ena m’njira yoyenerera ndipo anthu adzaphunzira mmene angathetsere tsankho la mtundu uliwonse.

  •   “Anthu okhala panthaka ya dzikolo adzaphunzira chilungamo.”—Yesaya 26:9.

  •   “Ntchito ya chilungamo chenicheni idzakhala mtendere, ndipo zochita za chilungamo chenicheni zidzakhala bata ndi mtendere mpaka kalekale.”—Yesaya 32:17.

 Masiku ano, anthu mamiliyoni akuphunzira kuchokera m’Baibulo mmene angamachitire zinthu mwa ulemu ndi ena.