Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

TheCrimsonMonkey/E+ via Getty Images

NTCHITO YAPADERA YOLALIKIRA

Mavuto Okhudza Zachilengedwe—Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?

Mavuto Okhudza Zachilengedwe—Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?

 “Pali mavuto aakulu a zachilengedwe omwe akukhudza anthu, mizinda komanso zamoyo zina. Mphepo zamphamvu zomwe zikuchulukirachulukirabe chifukwa cha kusintha kwa nyengo zikuwononga nyumba ndiponso miyoyo ya anthu ambiri padzikoli. Zamoyo zam’nyanja zikuluzikulu zikuvutika chifukwa cha kutentha koopsa ndipo zimenezi zikubweretsa chiopsezo [chakuti zikhoza kufa.]”​—Inger Andersen, pansi pa mlembi wamkulu wa bungwe la United Nations komanso mkulu woyang’anira bungwe la UN Environment Programme, July 25, 2023.

 Kodi maboma angakwanitse kuthetsa mavuto amenewa padziko lonse? Kodi ali ndi mphamvu zochititsa kuti zinthu ziyambirenso kuyenda bwino?

 Baibulo limanena kuti pali boma limene lingakwanitse kuchita zimenezi ndipo bomali lidzathetsadi mavuto onse okhudza zachilengedwe padzikoli. Limanena kuti “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu,” womwe ndi boma limene lizidzalamulira dziko lonse lapansi. (Danieli 2:44) Boma limenelo likadzayamba kulamulira, anthu ‘sazidzavulazana,’ kuwononga zinthu ndipo sadzawononganso dziko lapansi.​—Yesaya 11:9.