Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chiutsi cha moto wa bomba la nyukiliya lomwe laphulika

KHALANI MASO

Atsogoleri Andale Akuchenjeza za Aramagedo—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Atsogoleri Andale Akuchenjeza za Aramagedo—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Lolemba m’mawa pa 10 October 2022, asilikali a Russia anaphulitsa mizinda ya m’dziko la Ukraine pobwezera zimene asilikali a ku Ukraine anachita. Zimenezi zinachitika patadutsa masiku awiri asilikali a dzikoli ataphulitsa mlatho wolumikiza Crimea ndi Russia. Apa n’kuti atsogoleri andale ena atangochenjeza kumene kuti Aramagedo ikhoza kuchitika posachedwapa.

  •   “Zikuoneka kuti panopa tayandikira kwambiri Aramagedo kuposa mmene zinalili m’nthawi ya ulamuliro wa [Pulezidenti John F. Kennedy wa ku America] komanso pamene ku Cuba kunaphulitsidwa maboma oopsa kwambiri. . . . Ndikuganiza kuti ndi zosatheka kugwiritsa ntchito zida za nyukiliya popanda Aramagedo kuchitika.”—Joe Biden Pulezidenti wa ku America, 6 October 2022.

  •   Pulezidenti wa ku Ukraine, Volodymyr Zelensky, atafunsidwa maganizo ake pa nkhani ya zotsatirapo zogwiritsa ntchito zida za nyukiliya, ananena kuti: “Inenso ndikugwirizana ndi zoti imeneyi ndi Aramagedo ndipo dziko lonse lapansi lili pachiopsezo.”—BBC News, 8 October 2022.

 Kodi n’zoona kuti kugwiritsa ntchito zida za nyukiliya kungayambitse Aramagedo? Kodi Baibulo limanena zotani?

Kodi kugwiritsa ntchito zida za nyukiliya kungayambitse Aramagedo?

 Ayi. Mawu akuti “Aramagedo” amapezeka kamodzi kokha m’Baibulo pa Chivumbulutso 16:16. Mawuwa sanena za nkhondo yapakati pa mitundu ya anthu koma amanena za nkhondo yapakati pa Mulungu ndi “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chivumbulutso 16:14) Mulungu adzagwiritsa ntchito nkhondo ya Aramagedo pothetsa maulamuliro onse a anthu.—Danieli 2:44.

 Kuti mudziwe zambiri zokhudza zimene zidzachitikire dzikoli pa Aramagedo, werengani nkhani yakuti Kodi Nkhondo ya Aramagedo Idzakhala Yotani?

Kodi nkhondo ya nyukiliya idzawononga dzikoli komanso anthu onse?

 Ayi. Ngakhale kuti m’tsogolomu maulamuliro a anthu akhoza kugwiritsa ntchito zida za nyukiliya, koma Mulungu sadzalola kuti dzikoli liwonongedwe. Baibulo limati:

  •   “Dziko lapansi lidzakhalapobe mpaka kalekale.”—Mlaliki 1:4.

  •   “Olungama adzalandira dziko lapansi, Ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.

 Komabe, maulosi a m’Baibulo komanso zochitika za masiku ano, zikusonyeza kuti zinthu zatsala pang’ono kusintha padzikoli. (Mateyu 24:3-7; 2 Timoteyo 3:1-5) Onani zimene Baibulo limanena zokhudza m’tsogolo pophunzira Baibulo kwaulere mochita kukambirana.