Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Zingatithandize Ngati Tatopa ndi Mliri

Zimene Zingatithandize Ngati Tatopa ndi Mliri

 Kodi mwatopa chifukwa choyesetsa nthawi zonse kupewa mliri wa COVID-19? Ngati zili choncho, si inu nokha. Kwa miyezi yambiri, anthu padziko lonse anafunika kusintha zinthu pa moyo wawo chifukwa cha mliriwu. Hans Kluge, yemwe ndi dailekitala wa ku Europe wa Bungwe Loona za Umoyo pa Dziko Lonse ananena kuti anthu ambiri “adzimana zinthu zambiri pofuna kuthandiza kuti mliri wa COVID-19 usafalikire. Zimenezi zingatitopetse komanso kutigwetsa ulesi.”

 Ngati nanunso mwatopa ndi mmene mliriwu wasinthira zinthu pa moyo wanu, limbani mtima. Baibulo likuthandiza anthu ambiri kuti apirire nthawi yovutayi ndipo lingakuthandizeninso.

 N’chifukwa chiyani anthu ena atopa ndi mliri?

 Anthu akafunika kusintha zinthu pa moyo wawo kwa nthawi yaitali chifukwa chofuna kupewa mliri, akhoza kutopa kwambiri. Kutopa ndi mliri kungakhudze anthu mosiyanasiyana koma anthu ambiri angakhale ndi zizindikiro izi:

  •   Kusafuna kuchita chilichonse

  •   Kuvutika kudya kapena kugona, apo ayi kudya kapena kugona kwambiri

  •   kusachedwa kupsa mtima

  •   Kuda nkhawa chifukwa cha ntchito zimene mumatha kugwira mosavuta

  •   Kuvutika kuika maganizo pa zinthu

  •   Kukhumudwa kwambiri mpaka kufika pomaona kuti zinthu sizingasinthe

 N’chifukwa chiyani kutopa ndi mliri n’koopsa?

 Kutopa ndi mliri kungaike moyo wanu komanso wa anthu ena pa ngozi. Zili choncho chifukwa kungachititse kuti musiye kutsatira malangizo otetezera ku COVID-19. Pang’ono ndi pang’ono, mungayambe kuona kuti mliriwu si woopsa ngakhale kuti ukufalikirabe komanso kupha anthu. Chifukwa chotopa ndi ziletso zimene zabwera ndi mliriwu, mungayambe kufuna ufulu wambiri. Ndipo zimenezi zingaike moyo wanu ndi wa anthu ena pa ngozi.

 Pa nthawi yovutayi, anthu ambiri akuona umboni wa mawu a m’Baibulo akuti: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.” (Miyambo 24:10) M’Baibulo muli mfundo zimene zingatithandize kupirira mavuto monga mliri wa COVID-19.

 Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingakuthandizeni ngati mwatopa ndi mliri?

  •   Muzichezabe ndi anthu koma musamayandikane nawo

     Zimene Baibulo limanena: ‘Bwenzi lenileni linabadwira kuti likuthandize pakagwa mavuto.’—Miyambo 17:17.

     Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji? Anzathu enieni amatilimbikitsa. (1 Atesalonika 5:11) Koma tikhoza kudwala ngati timapewa anthu.—Miyambo 18:1.

     Tayesani izi: Pitirizani kucheza ndi anzanu pa vidiyokomfelensi, pa foni kapena polemberana mameseji. Muzicheza nawo pamene mukuvutika komanso muziona pafupipafupi ngati iwowo ali bwino. Muziuzana zimene zikukuthandizani kupirira pa nthawi ya mliriyi. Mukakhala wokhumudwa, muzipeza njira zochitira anzanu zinthu zabwino ndipo nanunso mudzasangalala.

  •   Muzichita zimene mungathe

     Zimene Baibulo limanena: “Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”—Aefeso 5:16.

     Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji? Kugwiritsa ntchito bwino nthawi yanu kungakuthandizeni kuti muziona zinthu moyenera m’malo moda nkhawa kwambiri.—Luka 12:25.

     Tayesani izi: M’malo moganizira zimene simungathe kuchita, muziyesetsa kuona zimene mungakwanitse kuchita. Mwachitsanzo, kodi pali ntchito kapena zosangalatsa zimene panopa muli ndi nthawi yozichitira? Kapena kodi mungacheze kwambiri ndi am’banja lanu?

  •   Muzikhala ndi ndandanda

     Zimene Baibulo limanena: “Zinthu zonse zizichitika . . . mwadongosolo.”—1 Akorinto 14:40.

     Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji? Anthu ambiri amakhala osangalala komanso amakhala ndi mtendere wamumtima akakhala ndi ndandanda yochitira zinthu.

     Tayesani izi: Mukhale ndi ndandanda yogwirizana ndi mmene zinthu zilili panopa pa moyo wanu. Muzikhala ndi nthawi yochitira ntchito zanu zakusukulu, ntchito zapakhomo komanso zinthu zauzimu. Muzikhalanso ndi nthawi yochezera ndi a m’banja lanu, masewera olimbitsa thupi komanso zinthu zina zosangalatsa zimene mungachite panja. Nthawi zina, muzionanso ndandanda yanu kuti muone ngati muyenera kuisintha.

  •   Muzichita zinthu mogwirizana ndi mmene nyengo ilili

     Zimene Baibulo limanena: “Wochenjera ndi amene amati akaona tsoka amabisala.”—Miyambo 22:3.

     Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji? Malinga ndi kumene mumakhala, nthawi zina nyengo ingakhale yoipa kwambiri moti simungakhale padzuwa kapena kupuma mpweya wabwino mokwanira. Zimenezi zingakhudze thanzi komanso maganizo anu.

     Tayesani izi: Ngati nyengo yozizira ikuyamba, sinthani zinthu m’nyumba yanu kuti dzuwa lizilowa. Muziyesetsa kuchita zinthu zina panja ngakhale kuti kukuzizira. Ngati zingatheke, pezani zovala zotenthera kuti muzitha kuchita zinthu panja.

     Ngati nyengo yotentha yafika, anthu ambiri azichita zinthu panja. Choncho muziyesetsa kukhala otetezeka. Muzisankha bwino malo komanso nthawi imene mungapite kumaloko n’cholinga choti musamakumane ndi anthu ambiri.

  •   Pitirizani kutsatira malangizo otetezera ku mliri wa COVID-19

     Zimene Baibulo limanena: “Wopusa amapsa mtima ndiponso amakhala wodzidalira.”—Miyambo 14:16.

     Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji? Mliri wa COVID-19 ndi woopsa ndipo tikasiya kutsatira malangizo tikhoza kudwala.

     Tayesani izi: Nthawi ndi nthawi muziona malangizo amene akuperekedwa kwanu kuti muone ngati mukuwatsatira bwinobwino. Muziganizira mmene zochita zanu zingakhudzire inuyo, a m’banja lanu komanso ena.

  •   Muzilimbikitsa ubwenzi wanu ndi Mulungu

     Zimene Baibulo limanena: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.”—Yakobo 4:8.

     Kodi nkhaniyi ndi yofunika bwanji? Mulungu angakuthandizeni kupirira vuto lililonse.—Yesaya 41:13.

     Tayesani izi: Muziwerenga mavesi ena a m’Baibulo tsiku lililonse. Njira yowerengera Baibulo imeneyi ingakuthandizeni kuti muyambe kuliwerenga tsiku ndi tsiku.

 Mungachite bwino kufunsa a Mboni za Yehova kuti akuuzeni zimene akuchita kuti apitirize kusonkhana pamodzi ngakhale pa nthawi ya mliri wa COVID-19 imeneyi. Mwachitsanzo, padziko lonse ambiri akhala akugwiritsa vidiyokomfelensi kuti azipanga misonkhano yawo yampingo, mwambo wa pa chaka wokumbukira imfa ya Yesu komanso msonkhano wachigawo.

 Mavesi a m’Baibulo amene angakuthandizeni ngati mwatopa ndi mliri

 Yesaya 30:15: “Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi achikhulupiriro.”

 Mfundo yake: Kukhulupirira malangizo a Mulungu kungatithandize kukhala ndi mtendere wamumtima pa nthawi ya mavuto.

 Miyambo 15:15: “Masiku onse a munthu wosautsika amakhala oipa, koma munthu wamtima wosangalala amachita phwando nthawi zonse.”

 Mfundo yake: Kuganizira zinthu zabwino kungatithandize kukhala osangalala pa nthawi ya mavuto.

 Miyambo 14:15: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.”

 Mfundo yake: Tizitsatira malangizo otetezera ku matenda ndipo tisafulumire kukhulupirira kuti malangizowo ndi osafunika.

 Yesaya 33:24: “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”

 Mfundo yake: Mulungu walonjeza kuti adzathetsa matenda onse.